Mas. 133 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kutamanda chikondi chachibaleNyimbo yoimba pokwera ku Yerusalemu.

1Ati kukoma ndi kukondweretsa ati,

anthu akakhala amodzi mwaubale!

2Ndi ngati mafuta amtengowapatali oĊµathira pa mutu,

otsikira ku ndevu, ku ndevu za Aroni,

oyenderera mpaka ku khosi la mkanjo wake.

3Ndi ngati mame a ku Heremoni,

omatsikira ku mapiri a Ziyoni.

Ku Ziyoni Chauta amaperekako madalitso,

ndiye kuti moyo wamuyaya.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help