1Yowasi anali wa zaka zisanu ndi ziŵiri pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka 40 ku Yerusalemu. Mai wake anali Zibiya wa ku Beereseba.
2Tsono Yowasiyo adachita zolungama pamaso pa Chauta nthaŵi yonse ya moyo wa wansembe Yehoyada.
3Yehoyada adaipezera mfumuyo akazi aŵiri, ndipo idabereka ana aamuna ndi ana aakazi.
4Pambuyo pake Yowasi adatsimikiza zokonzanso Nyumba ya Mulungu.
5Adasonkhanitsa ansembe ndi Alevi, naŵauza kuti, “Pitani ku mizinda ya Yuda, mukasonkhetse ndalama pakati pa Aisraele onse, kuti muzikonzera Nyumba ya Chauta wanu chaka ndi chaka. Muwone kuti zimenezi zichitike mwachangu.” Koma Alevi sadachite zimenezo mofulumira.
6Eks. 30.11-16 Motero mfumu idaitana Yehoyada mkulu wa ansembe nimfunsa kuti, “Kodi chifukwa chiyani sudaŵauze Alevi kuti asonkhetse ndalama ku Yuda ndi ku Yerusalemu, ndalama zimene adalamula Mose mtumiki wa Chauta ku mpingo wonse wa Aisraele, ndalama zokonzera hema lamsonkhano?”
7Paja anthu ake a Ataliya, mkazi woipa uja, adaaonongapo Nyumba ya Mulungu, ndiponso adaatenga zinthu zonse zopatulika za ku Nyumba ya Chautayo, nazipereka kwa Abaala.
8Motero mfumu idalamula kuti apange bokosi, aliike panja pa khomo la Nyumba ya Chauta.
9Ndipo adalengeza kwa anthu onse a ku Yuda ndi a mu Yerusalemu, kuti adzapereke kwa Chauta ndalama zimene Mose mtumiki wa Mulungu adaalamula kuchipululu kuja kuti Aisraele onse azipereka.
10Tsono akalonga onse, pamodzi ndi anthu onse adakondwa, nabwera ndi ndalama zao. Ankaponya ndalamazo m'bokosimo mpaka lidadzaza lonse.
11Nthaŵi zonse Alevi ankabwera nalo bokosilo kwa nduna zake za mfumu, akaona kuti muli ndalama zambiri. Tsono mlembi wa mfumu pamodzi ndi nduna ya mkulu wa ansembe, ankadzakhuthula ndalamazo, kenaka ankalitenga bokosilo nkulibweza pamalo pake. Umu ndimo m'mene ankachitira tsiku ndi tsiku, mwakuti adasonkha ndalama zambirimbiri.
12Ndipo mfumu pamodzi ndi Yehoyada ankazipereka kwa akapitao oyang'anira ntchito ya ku Nyumba ya Chauta. Tsono adalemba amisiri omanga ndi miyala ndi amisiri a matabwa, kuti akonzenso Nyumba ya Chauta. Adalembanso amisiri ogwira ntchito ndi chitsulo ndi mkuŵa, kuti akonze Nyumba ya Chauta.
13Anthu amene adalembedwawo ankagwiradi ntchito, ndipo ntchito yokonzayo idapita m'tsogolo akuigwira ndi manja ao. Choncho anthuwo Nyumba ya Chauta ija adaisandutsanso monga momwe idaaliri kale, ndipo adailimbitsa.
14Ataimaliza, ndalama zotsala adabwera nazo kwa mfumu ndi kwa Yehoyada. Iwo adapanga ziŵiya za ku Nyumba ya Chauta ndi ndalamazo, ziŵiya zogwirira ntchito ndiponso za nsembe zopsereza. Adapanganso mbale za lubani ndiponso ziŵiya zagolide ndi zasiliva.
Anthu asiya njira za YehoyadaAnthu ankapereka nsembe zopsereza ku Nyumba ya Chauta kosalekeza, pa nthaŵi yonse ya Yehoyada.
15Koma Yehoyada adakalamba kwambiri, masiku ake adachuluka, ndipo adamwalira ali wa zaka 130.
16Adamuika m'manda ku mzinda wa Davide pamodzi ndi mafumu, chifukwa chakuti adaachita zabwino m'dziko la Israele ndipo ankatumikira Mulungu ndi Nyumba yake.
17Yehoyada atamwalira, akalonga a ku Yuda adabwera kudzalambira mfumu, ndipo mfumu idaŵamvera.
18Anthu adasiya Nyumba ya Chauta, Mulungu wa makolo ao, namatumikira mafano. Tsono mkwiyo wa Mulungu udagwera anthu a ku Yuda ndi a mu Yerusalemu, chifukwa cha tchimo laoli.
19Komabe Mulungu adatuma aneneri pakati pao kuti anthuwo aŵabweze kwa Chauta. Koma aneneriwo ataŵadzudzula, anthuwo sadasamaleko ai.
20 Mt. 23.35; Lk. 11.51 Tsono mzimu wa Mulungu udaloŵa mwa Zekariya, mwana wa wansembe Yehoyada. Iye adaimirira pakati pa anthu naŵauza kuti, “Chauta akufunsa kuti, ‘Chifukwa chiyani mukuchimwira malamulo a Chauta? Ndithu simudzapindula kanthu?’ ”
21Koma anthuwo adamchita chiwembu, ndipo mfumu italamula, adamponya miyala m'bwalo la Nyumba ya Chauta.
22Motero mfumu Yowasi sadakumbukire zabwino zimene Yehoyada bambo wake wa Zekariya adamchitira, koma adapha mwana wake. Ndipo pamene ankafa, mwanayo adati, “Chauta apenye, ndipo abwezere chilango.”
Kutha kwa ufumu wa Yowasi23Pa kutha kwa chaka, gulu lankhondo la ku Siriya lidadzamenyana ndi Yowasi. Adabwera ku Yuda ndi ku Yerusalemu, napha akazembe onse a anthu pakati pa anthuwo. Ndipo adatumiza zofunkha zao zonse kwa mfumu ya ku Damasiko.
24Ngakhale gulu lankhondo la ku Siriya lidadza ndi anthu ochepa, Chauta adapereka m'manja mwao gulu lalikulu kwambiri la ankhondo, chifukwa chakuti anthuwo anali atasiya Chauta, Mulungu wa makolo ao. Umu ndimo m'mene anthu a ku Siriya adalangira Yowasi.
25Asiriya aja atamsiya wovulazidwa kwambiri, anyamata ake adamchita chiwembu, chifukwa cha magazi a mwana wa Yehoyada wansembe uja, ndipo adamphera pabedi pake. Motero iyeyo adafa. Ndipo adamuika m'manda mu mzinda wa Davide, koma sadamuike m'manda a mafumu.
26Anthu amene adamchita chiwembuwo ndi Zabadi mwana wa Simea Mwamoni, ndi Yehozabadi mwana wa Simeriti Mmowabu.
27Za ana ake aamuna ndiponso za mau ambiri omtsutsa iyeyo, kudzanso za kumanganso Nyumba ya Chauta, izo zidalembedwa m'buku lofotokoza za mafumu. Ndipo Amaziya mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.