Miy. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1 1Maf. 4.32 Aŵa ndi malangizo a Solomoni, mwana wa Davide, mfumu ya Israele.

2Ngothandiza kuti anthu adziŵe nzeru ndi mwambo,

kuti amvetse mau a matanthauzo ozama,

3kuti alandire mwambo wochita zinthu mwanzeru,

akhale angwiro, achilungamo ndi osakondera.

4Ngophunzitsa anthu wamba nzeru za kuchenjera,

ndi achinyamata kudziŵa zinthu ndi kulingalira bwino.

5Ndi oti wanzeru akaŵamva, aonjezere kuphunzira kwake,

ndipo munthu womvetsa zinthu apate luso,

6kuti azimvetsa miyambi ndi mafanizo,

mau a anthu anzeru ndi mikuluŵiko yao.

7 Yob. 28.28; Mas. 111.10; Miy. 9.10; Mphu. 1.14 Kuwopa Chauta ndiye chiyambi cha nzeru.

Zitsiru ndiye zimanyoza nzeru ndi malangizo.

Malangizo kwa achinyamata

8Mwana wanga, umvere zimene bambo wako akukulangiza,

usakane zimene mai wako akukuphunzitsa.

9Zili ngati nsangamutu yokongola yamaluŵa pamutu pako,

zili ngati mkanda wa m'khosi mwako.

10Mwana wanga, anthu oipa akafuna kukukopa,

usamaŵamvera.

11Adzati,

“Tiye kuno, tikabisale kuti tiphe anthu,

tiye tikalalire anthu osalakwa.

12Tiyeni tiŵameze amoyo ngati manda,

tiŵameze athunthu ngati anthu otsikira ku manda.

13Motero tidzapata zinthu zambiri zamtengowapatali,

nyumba zathu tidzazidzaza ndi zofunkha.

14Tiye uloŵe m'gulu lathu,

chuma chathu tidzagaŵana tonse.”

15Mwana wanga, usamayenda nawo anthu amenewo,

usatsagane nawo pa njira yaoyo.

16Paja iwowo amangofuna zoipa zokhazokha,

amathamangira kupha basi.

17Nkopanda phindu kutchera kumwezi,

nanga mbalame siziwona!

18Koma anthu ameneŵa amangodzitchera okha msampha,

m'menemo muli imfa yao yomwe.

19Ameneŵa ndiwo mathero a anthu opata chuma mwankhondo.

Chumacho chimapha eniake ochikundika.

Nzeru ichenjeza anthu.

20 Miy. 8.1-3 Nzeru ikufuula mu mseu,

ikulankhula mokweza mau m'misika.

21Ikufuula pa mphambano za miseu,

ikulankhula pa zipata za mzinda, kuti,

22“Kodi anthu osachangamukanu,

mudzakondwerabe kupusaku mpaka liti?

Kodi anthu onyodola, adzakhalabe akunyodola mpaka liti?

Nanga opusa adzakana kuphunzira zanzeru mpaka liti?

23Musamale kudzudzula kwangaku,

ine ndikuuzani maganizo anga,

ndi kukudziŵitsani mau anga.

24Paja ine ndidaakuitanani, inu nkukana kumvera,

ndidaati ndikuthandizeni, koma popanda wosamalako.

25Uphungu wanga simudaulabadire,

kudzudzula kwanga simudakusamale.

26Ndiye inenso ndidzakusekani, mukadzagwa m'mavuto,

ndidzakunyodolani, mukadzazunguzika ndi mantha,

27pamene mantha adzakukunthani ngati namondwe,

pamene tsoka lidzakufikirani ngati kamvulumvulu,

pamene mavuto ndi masautso adzakugwerani.

28Tsono mudzandiitana, koma ine sindidzaitaŵa,

mudzandifunafuna mwakhama, koma simudzandipeza.

29Popeza kuti mudadana ndi nzeru,

ndipo simudasankhe kuwopa Chauta,

30popeza kuti simudasamale malangizo anga,

ndipo mudanyoza kudzudzula kwanga konse,

31basitu tsono mudzadya zipatso zoyenera ntchito zanuzo,

mudzakhuta zoipa zimene munkafuna kuŵachita ena.

32Anthu opusa amaphedwa chifukwa cha kusokera kwao.

Zitsiru zimadziwononga zokha nkudzitama kwao.

33Koma amene amamvera ine adzakhala pabwino,

adzakhala mosatekeseka, osaopa choipa chilichonse”.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help