Mas. 59 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Pemphero lopempha chipulumutsoKwa Woimbitsa Nyimbo. Kutsata maimbidwe a nyimbo yoti: Musaononge. Salmo la Davide la mtundu wa Mikitamu. Saulo anali atatuma anthu kukadikirira pa nyumba ya Davide kuti amuphe.

1Pulumutseni kwa adani anga, Inu Mulungu wanga,

tetezeni kwa anthu ondiwukira.

2Pulumutseni kwa anthu ochita zoipa,

landitseni kwa anthu okhetsa magazi.

3Onani, iwo akubisalira moyo wanga,

anthu oopsa agwirizana kuti andithire nkhondo.

Ngakhale sindidachite choipa

kapena kuchimwa konse, Inu Chauta,

4ngakhale sindidalakwe,

anthuwo akuthamanga kukonzekera nkhondo.

Dzambatukani, mudzandithandize, ndipo muwone.

5Inu Chauta, Mulungu Wamphamvuzonse,

ndinu Mulungu wa Israele.

Dzambatukani kuti mulange anthu onse akunja.

Musasiye ndi mmodzi yemwe

mwa anthu onyengawo, ochita chiwembu.

6Amabweranso madzulo aliwonse

akuuwa ngati agalu,

nkumangoyendayenda mu mzinda.

7Awo ali ukowo, akulongolola kwambiri,

ndipo akufuula mwankhalwe,

chifukwa m'maganizo mwao amati,

“Ndani akutimva nanga?”

8Koma Inu Chauta, mumangoŵaseka.

Inu mumanyozera anthu onse akunja.

9Inu mphamvu zanga, maso anga ali pa Inu,

pakuti Inu Mulungu ndinu linga langa.

10Mulungu wanga adzandichingamira

chifukwa ndi wa chikondi chosasinthika.

Mulungu wanga adzandilola kuti ndisangalale

poona adani anga atagonja.

11Musaŵaphe pomwepa,

kuwopa kuti anthu anga angaiŵale,

koma muŵabalalitse ndi mphamvu zanu,

ndipo muŵagwetse,

Inu Ambuye, Inu chishango changa.

12Akodwe ndi kunyada kwao,

chifukwa cha uchimo wa m'kamwa mwao,

ndi mau a pakamwa pao.

Chifukwa chakuti amatemberera ndipo amanama,

13muŵakwiyire ndi kuŵaononga.

Muŵaonongeretu kuti asakhaleponso,

anthu azidziŵa kuti Mulungu ndiye wolamulira Yakobe,

mpaka ku mathero a dziko lapansi.

14Amabweranso madzulo aliwonse

akuuwa ngati agalu,

nkumangoyendayenda mu mzinda.

15Amanka nafunafuna chakudya

ndipo amangofuula akapanda kukhuta.

16Koma ndidzaimba nyimbo zotamanda mphamvu zanu,

m'maŵa ndidzaimba mokweza

nyimbo zoyamika chikondi chanu chosasinthika.

Pakuti Inu mwakhala ngati linga langa

ndi malo othaŵiramo pa nthaŵi ya mavuto anga.

17Inu mphamvu zanga,

ndidzakuimbirani nyimbo zokuyamikani,

pakuti Inu Mulungu ndinu linga langa,

ndinu Mulungu wondiwonetsa chikondi chosasinthika.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help