1Nthaŵi imeneyo Hezekiya adaadwala, ndipo anali pafupi kufa. Mneneri Yesaya, mwana wa Amozi, adapita kukamuwona, namuuza kuti, “Chauta akuti ukonze zonse bwino lomwe, poti ufa, suchira ai.”
2Pomwepo Hezekiya adatembenuka nayang'ana ku khoma, nayamba kupemphera kwa Chauta kuti,
3“Inu Chauta, mukumbukire kuti ndakhala ndikukutumikirani mokhulupirika ndi modzipereka. Ndipo nthaŵi zonse ndinali kuchita zokukomerani.” Atatero adayamba kulira ndi mtima woŵaŵa.
4Tsono Yesaya asanatuluke m'bwalo lapakati, Chauta adamuuza kuti,
5“Bwerera, kamuuze Hezekiya, mfumu ya anthu anga, mau aŵa, ‘Ine Chauta, Mulungu wa Davide kholo lako, ndamva pemphero lako, ndipo misozi yako ndaiwona. Chabwino, ndidzakuchiritsa. Udzatha kukapembedza ku Nyumba ya Chauta mkucha.
6Ndipo ndidzakuwonjezera zaka khumi ndi zisanu pa moyo wako. Ndidzakupulumutsa iwe pamodzi ndi mzindawu kwa mfumu ya ku Asiriya. Mzindawu ndidzautchinjiriza chifukwa cha ulemu wanga ndiponso chifukwa cha Davide mtumiki wanga.’ ”
7Pambuyo pake Yesaya adauza antchito a mfumu kuti, “Konzani phala lankhuyu. Kenaka mutengeko phalalo nkulimata pa chithupsa chake, kuti mfumu ichire.”
8Apo Hezekiya adafunsa Yesaya uja kuti, “Kodi padzakhala chizindikiro chanji choonetsa kuti Chauta adzandichiritsa, ndipo kuti ndidzatha kukapembedza ku Nyumba ya Chauta mkucha uno?”
9Yesaya adayankha kuti, “Chizindikiro chimene Chauta wakupatsa chakuti adzachitadi zimene adalonjeza nachi: Kodi chithunzithunzi chipite patsogolo kapena chibwerere pambuyo makwerero khumi?”
10Hezekiyayo adayankha kuti, “Nchapafupi kuti chithunzithunzi chipite patsogolo makwerero khumi, koma kuti chithunzithunzicho chibwerere m'mbuyo makwerero khumi, apo ndiponi.”
11Pamenepo mneneri Yesaya adatama Chauta mopemba. Ndipo Chauta adabweza chithunzithunzicho pambuyo makwerero khumi pa makwerero amene mfumu Ahazi adaamanga.
Akazembe ochokera ku Babiloni(Yes. 39.1-8)12Pa nthaŵi imeneyo Merodaki-Baladani, mwana wa Baladani, mfumu ya ku Babiloni, adatuma amithenga naŵapatsira makalata ndi mphatso, kuti akapereke kwa Hezekiya, poti adaamva kuti ankadwala.
13Hezekiya adaŵalandira anthuwo, naŵaonetsa nyumba yosungiramo zinthu zake, monga siliva, golide, zokometsera chakudya, mafuta onunkhira amtengowapatali, zida zonse zankhondo, ndiponso zonse zimene ankazisunga m'nyumba zake zosungiramo chuma. Panalibe kanthu kalikonse m'nyumbamo ndi mu ufumu wake wonse kamene sadaŵaonetse.
14Tsono mneneri Yesaya adapita kwa mfumu Hezekiya, namufunsa kuti, “Kodi anthu amene aja adakuuzani zotani, ndipo adaachokera kuti?” Hezekiya adayankha kuti, “Adaachokera ku dziko lakutali, ku Babiloni.”
15Yesaya adamufunsanso kuti, “Kodi m'nyumba mwanumo adaona chiyani?” Hezekiya adayankha kuti, “Adaona zonse za m'nyumba mwanga. Palibe ndi chinthu chimodzi chomwe chimene sindidaŵaonetse m'nyumba zanga zosungiramo chuma.”
16Pamenepo Yesaya adauza Hezekiya kuti, “Chauta akunena kuti
172Maf. 24.13; 2Mbi. 36.10nthaŵi idzafika pamene zonse za m'nyumba mwanu ndi zonse zimene makolo anu adazisonkhanitsa mpaka lero lino, adzakulandani kupita nazo ku Babiloni. Sipadzatsalapo ndi kanthu kamodzi komwe.
182Maf. 24.14, 15; Dan. 1.1-7Ambiri mwa ana anu, obala inu nomwe adzatengedwa, ndipo adzaŵasandutsa adindo ofulidwa otumikira ku nyumba ya mfumu ku Babiloni.”
19Tsono Hezekiya adauza Yesaya kuti, “Mau amene Chauta walankhulaŵa ngabwino.” Ponena zimenezo, Hezekiya ankaganiza kuti, “Palibe kanthu ai, malinga kuti padzakhale mtendere ndi bata masiku onse a moyo wanga.”
Kutha kwake kwa ufumu wa Hezekiya(2 Mbi. 33.1-20)20Tsono ntchito zina za Hezekiya ndi mphamvu zake zonse ndi m'menenso adakumbira chidziŵe ndi ngalande zobwera ndi madzi mumzindamo, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Yuda.
21Ndipo Hezekiya adamwalira naikidwa m'manda momwe adaikidwa makolo ake. Tsono Manase mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.