1Pamene Sanibalati adamva kuti tikumanga khoma, adapsa mtima nakalipa kwambiri, ndipo adayamba kuŵaseka Ayuda monyodola.
2Adalankhula pamaso pa abale ake, ndi pamaso pa gulu lankhondo la ku Samariya, adati, “Kodi Ayuda achabechabeŵa akuchita chiyani? Monga amati nkumanganso mzindawu? Kodi nsembe ndiye adzapereka? Kodi adzaumaliza pa tsiku limodzi? Kodi adzachita kutolatolanso miyala yakale ija, ndi m'mene idapsera muja?”
3Tobiya Mwamoni amene anali naye adati, “Inde, chimene akumangacho, ngati nkhandwe ikwerapo, idzagwetseratu khoma la miyala laolo.”
4Pamenepo ndidayamba kupemphera, ndidati, “Inu Mulungu wathu, imvani m'mene akutinyozera. Mau ao otonza aŵabwerere, anthu ameneŵa alandidwe zao zonse, ndipo atengedwe ukapolo ku dziko lachilendo.
5Musaŵakhululukire cholakwa chao, musafafanize tchimo lao, popeza kuti aputa ukali wanu pamaso pa amisiri omanga.”
6Motero tidamangabe khoma, ndipo khoma lonse tidatha kulimanga mpaka theka la msinkhu wake, chifukwa chakuti anthu adaaikapo mtima pa ntchitoyo.
7Koma pamene Sanibalati ndi Tobiya, ndiponso Arabu, Aamoni ndi Aasidodi adamva kuti ntchito yokonza makoma a Yerusalemu ikupita m'tsogolo, ndipo kuti malo ogamukagamuka aja akuŵakonzanso, adapsa mtima kwambiri.
8Tsono adapangana za chiwembu choti akathire nkhondo Yerusalemu ndi kusokoneza anthu amumzindamo.
9Apo ife tidapemphera kwa Mulungu wathu, ndipo tidaika alonda oti azititeteza kwa adani athuwo usana ndi usiku.
10Tsono Ayuda ankati, “Mphamvu za onyamula zinyalala zilikutha, ndipo zinyalala zoyenera kutayidwazo nzambiri. Ndiyetu sitiitha ife ntchito yomanga khomayi.”
11Adani athu ankanena zakuti ife Ayuda sitidzadziŵa kapena kuwona kanthu, mpaka iwo atafika pakati pathu, natipha ndi kuletsa ntchito yathuyi.
12Tsono Ayuda okhala pafupi ndi adani athuwo ankabwera natichenjeza kakhumi konse kuti “Iwo aja adzafika kudzalimbana nanu kuchokera kulikonse kumene amakhala.”
13Choncho paliponse pamene khomalo linali lisanathe, kumbuyo kwake, cha m'munsi mwake, m'malo okonza bwino, ndidaikamo anthu, m'mabanjam'mabanja, atatenga malupanga, mikondo ndi mauta.
14Koma nditazindikira mantha ao, ndidachitapo kanthu. Mwakuti ndidauza atsogoleri ndi akulu olamula, ndiponso anthu ena onse kuti, “Musaŵaope ameneŵa. Kumbukirani kuti Chauta ndi wamkulu ndiponso ndi woopsa, tsono mumenyere nkhondo abale anu, ana anu, akazi anu, ndi nyumba zanu.”
15Pamene adani athu adamva kuti ife tikudziŵa cholinga chao, adazindikira kuti Mulungu walepheretsa zimene iwowo adaapangana kuti atichite. Tsono tonse tidapitanso ku ntchito yomanga khoma, aliyense ku ntchito yake.
16Kuyambira tsiku limenelo mpaka m'tsogolo mwake, theka lina la antchito anga linkagwira ntchitoyo, ndipo theka lina linkagwira mikondo, zishango, mauta ndiponso linkavala malaya achitsulo. Tsono akulu a Ayuda ankalimbitsa anthu ao amene ankamanga khoma.
17Anthu onyamula zinyalala aja ankagwira ntchito ndi dzanja limodzi, kwinaku atagwira chida chankhondo.
18Mmisiri aliyense anali atamangirira lupanga m'chiwuno mwake pamene ankamanga. Munthu woimba lipenga anali pambali panga nthaŵi zonse.
19Ndidaŵauza atsogoleri ndi akuluakulu ndiponso anthu ena onse aja kuti, “Ntchitoyi njaikulu, ili pa dera lalikulu, ndipo ifeyo takhala motayanatayana kwambiri pa khoma.
20Tsono kumene muliriko mukamva kulira kwa lipenga, mudzasonkhane msanga kumene tili ife kuno. Mulungu wathu adzatimenyera nkhondo.”
21Choncho enafe tinkagwira ntchito, ndipo theka lina la anthuwo linkagwira zida zankhondo, kuyambira m'matandakucha mpaka nyenyezi zitaoneka.
22Pa nthaŵi imeneyi ndidaŵauzanso anthu kuti, “Aliyense pamodzi ndi wantchito wake agone m'Yerusalemu, kuti tikhale ndi otitchinjiriza usiku, ndipo kuti masana tizigwira ntchito.”
23Motero ine, anzanga, antchito anga, ndiponso anthu otitchinjiriza amene ankanditsata, panalibe ndi mmodzi yemwe mwa ife amene ankavula zovala zake usiku pogona. Aliyense ankasunga chida chankhondo pambalipa.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.