1Anthu ena adauza Yowabu kuti, “Amfumutu akulira maliro a Abisalomu.”
2Choncho chikondwerero cha tsikulo chidasanduka maliro kwa anthu onse, pakuti anthu adamva kuti mfumu ili pa chisoni chachikulu chifukwa cha mwana wake.
3Tsiku limenelo anthu adaloŵa mu mzinda kachetechete, monga momwe anthu amaloŵera mu mzinda mwamanyazi, akamathaŵa kunkhondo.
4Mfumu idaphimba kumaso, nimalira kuti, “Kalanga ine, mwana wanga Abisalomu, iwe Abisalomu mwana wanga, mwana wanga!”
5Tsono Yowabu adaloŵa m'nyumba ya mfumu nakafika kwa mfumu, nati, “Inu lero mwachititsa manyazi ankhondo anu amene apulumutsa moyo wanu, ndiponso moyo wa ana anu aamuna ndi aakazi, kudzanso moyo wa akazi anu ndi wa azikazi anu,
6poti inu mumakonda anthu odana nanu, ndipo mumadana ndi anthu okukondani. Lero ndiye mwatiwonetsa poyera kuti akalonga ndi ankhondo anu mulibe nawo kanthu. Ha, ndikudziŵa kuti Abisalomu adakakhala moyo, tonsefe nkufa, inu mukadakondwa.
7Koma nyamukani tsono mutuluke, mukaŵalimbitse mtima ankhondo anu moŵakondweretsa. Ndithu ndikulumbira pali Chauta kuti, ngati simupita, onse akuthaŵani usiku uno. Ndipo zimenezi zidzakuipirani kwambiri kupambana zoipa zonse zimene zidakugweranipo kale, kuyambira muli mwana mpaka tsopano lino.”
8Itamva zimenezi mfumu idanyamuka, nikakhala pansi pafupi ndi chipata. Choncho anthu onse atamva kuti mfumu ili ku chipata, adabwera pamaso pa mfumuyo.
Davide abweranso ku Yerusalemu.Nthaŵi imeneyo nkuti Aisraele atathaŵa, aliyense kunka kwao.
9Ndipo onsewo ankangokangana okhaokha. Ankati, “Mfumu Davide adatipulumutsa kwa adani athu, ndipo adatilanditsa kwa Afilisti. Koma tsopano watuluka m'dziko muno, kuthaŵa Abisalomu.
10Koma Abisalomuyo amene ife tidamdzoza kuti akhale mfumu yathu, adafa ku nkhondo. Chifukwa chiyani tsono simukunena kanthu zokatenga mfumu Davide kuti abwerenso?”
11Mfumu Davide adatumiza mau kwa ansembe aja, Zadoki ndi Abiyatara, akuti, “Mufunse atsogoleri a ku Yuda kuti, ‘Chifukwa chiyani inu mukuzengereza kwambiri osakaitenganso mfumu kuti ibwerere ku nyumba kwake, pamene Aisraele onse atumiza kale mau kwa mfumu onena kuti mfumu ibwerere kunyumba kwake?
12Inu ndinu abale anga enieni. Chifukwa chiyani inuyo mukufuna kukhala otsirizira pakuiitananso mfumu?’
13Ndipo mukauze Amasa mau anga oti, ‘Kodi iwe, sindiwe mbale wanga weniweni?’ Ndithu Mulungu andilange, mpaka ndife ndithu, ngati sindikuika iwe kuti ukhale mkulu wankhondo m'malo mwa Yowabu kuyambira tsopano lino.”
14Choncho Davide adakopa mitima ya Ayuda onse, ndipo adamangana chimodzi. Motero anthuwo adatumiza mau kwa mfumu kuti, “Bwererani inu pamodzi ndi ankhondo anu onse.”
15Motero mfumu idabwerera ku Yordani. Ndipo anthu onse a mtundu wa Yuda adafika ku Giligala kudzakumana ndi mfumu ndi kuiwolotsa Yordani.
16 2Sam. 16.5-13 Tsono Simei, mwana wa Gera, Mbenjamini wa ku Bahurimu, adabwera mofulumira pamodzi ndi Ayuda kudzakumana ndi mfumu Davide.
17Iyeyo anali ndi anthu 1,000 a ku Benjamini. Zibanso mtumiki uja wa m'banja la Saulo, pamodzi ndi ana ake aamuna khumi ndi asanu ndiponso antchito ake makumi aŵiri, adathamangira ku Yordani, nakafikako isanafike mfumu.
18Ndipo adaolotsa onse a m'banja la mfumu, nachita zonse zokondweretsa mfumuyo.
Davide achitira Simei chifundo.Tsono pamene mfumu Davide anali pafupi kuwoloka Yordani, Simei mwana wa Gera, adadzigwetsa pansi pamaso pa mfumuyo.
19Adauza mfumu kuti, “Mbuyanga, chonde mundikhululukire, musakumbukirenso tchimo limene ine kapolo wanu ndidachita pa tsiku lija, pamene inu mbuyanga mfumu munkachoka mu Yerusalemu. Amfumu musazisunge kukhosi zimenezi.
20Ine kapolo wanu ndikudziŵa kuti ndidalakwa. Nchifukwa chake mukuwona kuti ndabwera lero lino, ndipo m'banja lonse la Yosefe, ndayambira ndine kubwera kudzakuchingamirani inu mbuyanga mfumu.”
21Pompo Abisai, mwana wa Zeruya, adafunsa kuti, “Kodi Simeiyu ndiye saphedwa chifukwa chotukwana wodzozedwa wa Chauta?”
22Koma Davide adayankha kuti, “Za ine zikukukhudzani bwanji, inu ana a Zeruya, kuti lero lino mukhale ngati adani anga. Kodi lero m'dziko la Israele nkuphamo munthu? Kodi sindikudziŵa kuti tsopano ndine mfumu ya Aisraele?”
23Ndipo mfumu idauza Simei kuti, “Ndikunenetsa molumbira kuti iwe Simei suphedwa.”
Davide achitira Mefiboseti chifundo.24 2Sam. 9.1-13; 16.1-4 Tsono Mefiboseti, mdzukulu wa Saulo, adapita kukakumana ndi mfumu. Sadasambe m'miyendo, ndevu osameta, ndipo sadachape zovala zake kuyambira tsiku limene mfumu idachoka, mpaka tsiku limene idabwerera mwamtendere.
25Ndiye pamene ankabwera ku Yerusalemu kudzakumana ndi mfumu, mfumuyo idamufunsa kuti, “Iwe Mefiboseti, chifukwa chiyani sudapite nane limodzi?”
26Mefiboseti adayankha kuti, “Ine mbuyanga mfumu, adaandilakwitsa ndi wantchito wanga. Kapolo wanune wantchitoyo ndidamuuza bwinobwino kuti, ‘Undimangire chishalo pa bulu kuti ndikwere, ndipite nawo limodzi amfumu,’ poti paja ine kapolo wanu ndine wolumala.
27Koma iyeyo nkundisinjirira ine kapolo wanu kwa inu mbuyanga mfumu. Komatu inu muli ngati mngelo wa Mulungu. Nchifukwa chake tsono, muchite zimene zikukomereni.
28Paja anthu onse a banja la bambo wanga anali oyenera kuphedwa ndi inu mbuyanga mfumu. Koma ine mtumiki wanu mudaandiika pakati pa anthu amene ankadya ndi inu pa tebulo lanu. Nanga ndingakhale ndi chiyaninso ine chimene chingandiyenereze kuti ndingadandaule kwa inu amfumu?”
29Apo mfumu idati, “Basi ndamva usaonjezenso mau ena ai. Ine ndikufuna kuti iwe ndi Ziba mugaŵane chuma cha Saulo.”
30Koma Mefiboseti adauza mfumu kuti, “Mloleni mnzangayu kuti atenge ndiye chuma chonsecho. Kwa ine kwakwana kuti inu mbuyanga mfumu mwafika kwanu kuno mwamtendere.”
Davide achitira Barizilai chifundo.31 2Sam. 17.27-29 Tsono Barizilai Mgiliyadi adafika kuchokera ku Rogelimu. Adapita ndi mfumu mpaka ku Yordani kuti akaiperekeze pooloka Yordani.
32Barizilai anali munthu wokalamba, wa zaka 80 zakubadwa. Ndipo iye ndiye ankapatsa mfumu chakudya nthaŵi imene mfumuyo inkakhala ku Mahanaimu, pakuti iyeyo anali munthu wolemera kwambiri.
33Choncho mfumu idauza Barizilai kuti, “Tiye tipite limodzi, ndikakusunga ku Yerusalemu.”
34Koma Barizilai adafunsa mfumu kuti, “Kodi ine zanditsalira zaka zingati zokhalabe moyo, kuti ndingapite nanu amfumu ku Yerusalemu?
35Tsopano ine zaka zanga zakwana 80. Kodi ndingathe kusiyanitsa zinthu zokondwetsa ndi zosakondwetsa? Kodi ine mtumiki wanu ndingathe kuzindikira kukoma kwake kwa zakudya kapena zakumwa? Kodi ine ndingathebe kumamvera kuimba kwa amuna ndi kwa akazi? Chifukwa chiyani ine mtumiki wanu ndikakhale ngati katundu wolemera wosanjikiza pa inu, mbuyanga mfumu?
36Koma ine mtumiki wanu ndingoyenda pang'ono kuti ndiwoloke Yordani pamodzi ndi inu amfumu. Amfumu mungandipatsirenji mphotho yotere?
37Chonde, ingondilolani ine mtumiki wanu ndibwerere kuti ndikafere kumudzi kwathu, pafupi ndi manda a bambo wanga ndi a mai wanga. Koma suyu mwana wanga Kimuhamu, akhale mtumiki wanu. Iyeyu ndiye aoloke pamodzi ndi inu mbuyanga mfumu. Ndipo mumchitire chilichonse chimene chikukomereni.”
38Apo mfumu idayankha kuti, “Kimuhamu ndiwoloka naye limodzi, ndipo ndidzamchitira chilichonse chimene chikukomereni inu. Ndipo zonse zimene mufuna kuti ndikuchitireni, ndidzakuchitirani.”
39Choncho anthu onse adaoloka Yordani, nayonso mfumu idaoloka. Ndipo mfumu idampsompsona Barizilai, nimdalitsa, ndipo iye adabwerera kwao.
40Mfumu idapitirira mpaka kukafika ku Giligala, ndipo Kimuhamu adapita nao. Anthu onse a ku Yuda ndiponso theka la anthu a ku Israele, onse adaperekeza mfumu.
41Kenaka Aisraele onse adafika kwa mfumu, nadzafunsa kuti, “Chifukwa chiyani abale athu Ayuda achita ngati kukubani, nabwera ndi inu amfumu pamodzi ndi banja lanu ndi anthu anu onse, kuwoloka Yordani?”
42Ayuda adayankha Aisraelewo kuti, “Chifukwa chake nchakuti mfumuyi ndi mbale wathu weniweni. Inu chakukwiyitsani nchiyani pamenepa? Kodi mfumu taidyera chiyani? Nanga yatipatsa mphatso yanji?”
43Apo Aisraelewo adayankha Ayuda aja kuti, “Tili ndi zigawo khumi mwa mfumu imeneyi, ndipo mwa ufumu wa Davide ife tili ndi zigawo zambiri kupambana inu. Nanga chifukwa chiyani tsono mukutinyoza? Kodi ife sindife amene tidayamba kulankhula zoti mfumu yathu ibwerenso?” Koma anthu a ku Yuda adalankhula mwaukali kwambiri kupambana anthu a ku Israele.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.