1Chauta akapanda kumanga nawo nyumba,
omanga nyumbayo angogwira ntchito pachabe.
Chauta akapanda kulonda nawo mzinda,
mlonda angochezera pachabe.
2Mungodzivuta nkulaŵirira m'mamaŵa
ndi kukagona mochedwa,
kugwira ntchito movutikira kuti mupeze chakudya.
Paja Chauta amapatsa okondedwa ake zosoŵa zao
iwowo ali m'tulo.
3Zoonadi, ana ndi mphatso yochokera kwa Chauta,
zidzukulu ndi mphotho yake.
4Ana apaunyamata ali ngati mivi m'manja
mwa munthu wankhondo.
5Ngwodala amene phodo lake nlodzaza ndi mivi yotere.
Sadzamchititsa manyazi
akamalankhula ndi adani ake pa bwalo lamilandu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.