Eks. 19 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Aisraele ku phiri la Sinai

1Pa tsiku loyamba la mwezi wachitatu chichokere cha Aisraele ku Ejipito, mpamene adafika ku chipululu cha Sinai.

2Atachoka ku Refidimu adakafika ku chipululu cha Sinai, kumene adamangako mahema pafupi ndi phirilo.

3Mose adakwera phiri kukakumana ndi Mulungu, ndipo Mulungu adamuitana m'phirimo namuuza kuti, “Uuze zidzukulu za Yakobe, ndiye kuti mtundu wonse wa Aisraele kuti,

4‘Mudaona zimene ndidaŵachita Aejipito, ndiponso muja ndidakunyamulani monga m'mene mphungu imanyamulira ana ake pa mapiko ake, ndipo ndidakufikitsani kwa Ine.

51Pet. 2.9

Deut. 4.20; 7.6; 14.2; 26.18; Tit. 2.14 Tsono mukamandimvera ndi kusunga chipangano changa, mudzakhala anthu anga pakati pa makamu onse, pakuti dziko lonse lapansi ndi langa.

6Chiv. 1.6; 5.10 Ndipo inu mudzakhala anthu onditumikira Ine ngati ansembe, ndiponso ngati mtundu woyera. Tsono ukaŵauze mau ameneŵa Aisraele.’ ”

7Pamenepo Mose adakaitana atsogoleri a Aisraele, ndipo adaŵauza zonse zimene Chauta adamlamula.

8Anthuwo adayankha pamodzi kuti, “Tidzachita zonse zimene Chauta wanena.” Pambuyo pake Mose adakafotokozera Chauta zimene anthuwo adanena.

9Chauta adauza Mose kuti, “Ndikubwera kwa iwe mu mtambo wochindikira, kuti anthuwo azidzandimva ndikamalankhula ndi iwe, ndiponso kuti adzakhulupirire nthaŵi zonse.”

Tsono Mose adauza Chauta zimene anthu adanena.

10Chauta adauza Mose kuti, “Pita kwa anthuwo, ndipo uŵayeretse lero ndi maŵa. Achape zovala zao,

11ndipo akhale okonzeka mkucha. Pa tsiku limenelo, Ine Chauta ndidzatsika pa phiri la Sinai, ndipo kumeneko anthu onse adzandiwona Ine.

12Ahe. 12.18-20 Uŵalembere malire anthuwo pozungulira phirilo, ndipo uŵauze kuti, ‘Samalani, musakwere phiri kapena kukhudza tsinde lake. Wina aliyense akalikhudza, afa.

13Wina aliyense asakhudze munthuyo, koma anthu amponye miyala kapena kumubaya. Chikhale choŵeta, chidzaphedwa; akhale munthu, adzaphedwanso. Mbetete ikamalira, anthu abwere ku phiri.’ ”

14Mose adatsika phiri, nakafika kwa anthuwo, ndipo adaŵayeretsa. Anthuwo adachapadi zovala zao.

15Kenaka Mose adaŵauza kuti, “Mkucha uno, mukonzeke. Musayandikize mkazi.”

16 Chiv. 4.5 Deut. 4.11, 12 Tsono m'maŵa, pa tsiku lakelo, panali mabingu ndi mphezi paphiripo. Kunalinso mtambo wochindikira, ndiponso kulira kwakukulu kwa mbetete. Anthu onse m'mahemamo ankangonjenjemera ndi mantha.

17Mose adaŵatsogolera anthuwo kuchoka kumahemako, kuti akakumane ndi Mulungu, ndipo onsewo adaima patsinde pa phiri.

18Phiri lonse la Sinai lidaphimbidwa ndi utsi, chifukwa choti Mulungu adaatsikira paphiripo. Utsiwo unkangokwera ngati utsi wam'ng'anjo, ndipo anthu onse aja ankangonjenjemera kwambiri.

19Liwu la mbetete linkakulirakulira. Apo Mose adalankhula, ndipo Mulungu adamuyankha ndi mabingu.

20Chauta adafika pamwamba pa phiri la Sinai, adaitana Mose pamwamba pa phiri, ndipo Moseyo adakwera phirilo.

21Chauta adauza Mose kuti, “Tsika pansi, ndipo uza anthu kuti asapitirire malire ndi kubwera kumadzayang'ana kwa Ine, kuti ambiri mwa iwowo angadzafe.

22Ngakhale ansembe amene akufika pafupi ndi Ine adziyeretse, kuti ndingadzaŵalange.”

23Mose adayankha Chauta kuti, “Anthuwo sangakwere ai, chifukwa mudachenjezeratu kuti, ‘Mulembe malire kuzungulira phirilo, ndipo mulipatule kuti likhale loyera.’ ”

24Tsono Chauta adauza Moseyo kuti, “Tsika pansi, ndipo ukamtenge Aroni, ubwere naye kuno. Koma ansembe pamodzi ndi anthu asabzole malirewo kubwera kwa Ine kuno, kuti ndingadzaŵalange.”

25Apo Mose adatsikira kwa anthu kuja kukaŵauza zimenezo.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help