Ezek. 33 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mulungu aika Ezekiele kuti akhale mlonda(Ezek. 3.16-21)

1Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,

2“Iwe mwana wa munthu, uza anthu a mtundu wako zimene zimachitika ndikatumiza nkhondo m'dziko. Suja anthu am'dzikomo amasankha mmodzi pakati pao kuti akhale mlonda.

3Iye akaona mdani akubwera, amaliza lipenga kuti achenjeze aliyense.

4Wina akalimva lipengalo, koma osasamala, ndipo mdani akabwera nkumupha, wadziphetsa ndi mtima wake.

5Wadziphetsa yekha chifukwa choti sadasamale chenjezo. Akadasamala, akadapulumuka.

6Koma mlonda akaona mdani akubwera, iye osaliza lipenga kuti achenjeze anthu, tsono mdani nkubwera napha munthu wina, ngakhale kuti munthuyo wafera machimo ake, Ine ndidzamzenga mlandu mlonda uja chifukwa cha imfa ya mnzakeyo.

7“Tsono iwe mwana wa munthu, ndakuika kuti ukhale mlonda wa Aisraele. Ukamva mau anga, uŵachenjeze.

8Ndikauza munthu woipa kuti, ‘Munthu woipa iwe, udzafa,’ iwe nupanda kumchenjeza kuti aleke makhalidwe oipa, kuti akhalebe ndi moyo, munthuyo adzafadi ali wochimwa, koma iweyo ndidzakuzenga mlandu chifukwa cha imfa yake.

9Koma munthu woipa ukamchenjeza kuti asiye njira zake zoipa, iye nkupitiriza makhalidwe ake oipawo, adzafa ali wochimwa, koma iweyo udzapulumutsa moyo wako.

Udindo wa munthu aliyense

10“Iwe mwana wa munthu, uŵakumbutse Aisraele mau ao akuti, ‘Talemedwa ndi machimo athu ndipo tikuwonda nazo zolakwa zimene tachita. Kodi tingakhale ndi moyo bwanji?’

11Uŵauze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, Ndithudi, pali Ine ndemwe, sindikondwa ndikaona munthu woipa alikufa. Ndikadakonda kuti aleke kuchimwako kuti akhale ndi moyo. Inu Aisraele, muferanji? Tembenukani, lekani zoipa zimene mukuchita.

12“Tsono iwe mwana wa munthu, uza anthu ako kuti, Pamene munthu wochita chifuniro cha Mulungu achimwa, zabwino zimene adaachita sizidzampulumutsa. Woipa akaleka kuchimwa, sadzalangidwa. Ndipo munthu wochita chifuniro cha Mulungu akayamba kuchimwa, sadzatha kukhala ndi moyo chifukwa cha ntchito zake zabwino.

13Ngakhale ndiwuze munthu wochita chifuniro cha Mulungu kuti adzakhala ndi moyo, ngati iye agonera pa zabwino zimene adaachita kale, nayamba kuchimwa, zabwino zake zonse zimene adaachitazo zidzaiŵalika. Adzafera zochimwa zakezo.

14Chimodzimodzi ndikamchenjeza munthu wochimwa kuti adzafa, tsono iye nkuleka kuchimwako, namachita zolungama ndi zabwino,

15monga kubweza chigwiriro chimene adatenga chifukwa cha ngongole, kubweza zimene adaba, kusiya zochimwa ndi kumasunga malamulo opatsa moyo, ndithu sadzafa, adzakhala ndi moyo.

16Ndidzamkhululukira machimo ake amene adaachita. Chifukwa cha zabwino ndi zolungama zimene adachitazo, ndithu adzakhala ndi moyo.

17“Komabe anthu a mtundu wako amati, ‘Zimene Chauta amachitazi nzopanda chilungamo.’ Iyai, koma makhalidwe ao ndiwo amene ali osalungama.

18Munthu wabwino akaleka kuchita zabwino, nayamba kumachita zoipa, adzafa nazo.

19Munthunso woipa, akaleka kuchimwa, namachita zolungama ndi zabwino, adzapulumutsa moyo wake.

20Tsono inu am'banja la Israele, mumanena kuti, ‘Zimene Chauta amachitazi nzopanda chilungamo.’ Iyai, aliyense mwa inu Ine ndidzamuweruza potsata zochita zake.”

Mbiri ya kugwa kwa Yerusalemu

21 2Maf. 25.3-10; Yer. 39.2-8; 52.4-14 Pa tsiku lachisanu la mwezi wakhumi, chaka cha khumi ndi chiŵiri cha ukapolo wathu, munthu amene adapulumuka ku Yerusalemu, adabwera kudzandiwuza kuti mzinda wagwa.

22Madzulo, iyeyo asanabwere, ndidaagwidwa ndi mphamvu za Chauta. Koma m'maŵa mwake, munthuyo atafika, Chauta adandibwezera mphamvu zolankhulira, ndipo sindinalinso bububu.

Machimo a anthu

23Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,

24“Iwe mwana wa munthu, anthu amene akukhala m'mizinda yamabwinja ku dziko la Israele, akunena kuti, ‘Abrahamu anali munthu mmodzi yekha, ndipo adamupatsa dziko lonse. Koma ife tilipo ambiri, motero tsopano dzikolo ndi lathu.’

25Tsono uŵauze kuti Ine Ambuye Chauta ndikuti, ‘Mumadya nyama pamodzi ndi magazi omwe. Mumapembedza mafano, mumapha anthu. Kodi tsono dzikolo nkudzakhaladi lanu?’

26Mumadalira malupanga anu. Mumachita zonyansa, ndipo aliyense amachita chigololo ndi mkazi wa mnzake. Kodi dzikolo nkudzakhaladi lanu?

27Uŵauze kuti, Ine Ambuye Chauta ndikuti, Pali ine ndemwe wamoyo, anthu amene adatsala m'mizinda yamabwinja, adzaphedwa ndi lupanga. Amene adatsala m'midzi, ndidzaŵapereka ku zilombo kuti ziŵadye. Amene adabisala m'mapiri ndi m'mapanga, adzafa ndi mliri.

28Dzikolo ndidzalisandutsa tsala ndiponso chipululu. Mphamvu zimene ankanyada nazo zidzatheratu. Mapiri a ku Israele adzasanduka thengo, kotero kuti munthu sadzadutsako.

29Ndikadzalanga anthu chifukwa cha zonyansa zimene adachita, ndi kusandutsa dzikolo kuti likhale tsala ndiponso chipululu, pamenepo adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.

Zotsatira za uthenga wa mneneri

30“Koma kunena za iwe, mwana wa munthu, anthu a mtundu wako amalankhula za iwe, akamakumana pafupi ndi makoma a mzinda ndi pa makomo a nyumba zao. Amauzana kuti, ‘Tiyeni tsopano tikamve zimene Chauta wanena.’

31Anthu anga amadzasonkhana kwa iwe nakhala pansi kuti amve zimene iweyo unene. Koma akazimva, sazitsata zimenezo. Zokamba zao zimaonetsa chikondi, m'menemo mitima yao imangokonda phindu chabe.

32Kwa iwowo sindiwe kanthu konse, ndiwe munthu wamba chabe womangoimba nyimbo zachikondi ndi liwu lokoma poimba zeze. Kumva amamva mau ako onse, koma saŵagwiritsa ntchito.

33Koma zimene wanena zikadzachitikadi—ndipo zidzachitika kumene—apo adzadziŵa kuti pakati pao panalidi mneneri.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help