Ntc. 17 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za ku Tesalonika

1Paulo ndi anzake aja adapitirira mizinda ya Amfipoli ndi Apoloniya nakafika ku Tesalonika. Kumeneko kunali nyumba yamapemphero ya Ayuda.

2Tsono Paulo adaloŵa nawo monga adaazoloŵera, ndipo adakambirana nawo za m'Malembo pa masabata atatu.

3Adaŵamasulira za m'Malembomo ndi kuŵatsimikizira kuti Mpulumutsi wolonjezedwa uja adaayenera kumva zoŵaŵa kenaka nkuuka kwa akufa. Paulo adati, “Yesu amene ndikukulalikiraniyu, ndiye Mpulumutsiyo.”

4Tsono ena mwa iwo adakopeka, natsata Paulo ndi Silasi. Agriki ambirimbiri opembedza Mulungu adateronso, pamodzi ndi akazi ambiri apamwamba.

5Koma Ayuda ena adachita nsanje, choncho adasonkhanitsa anthu opandapake ongoyendayenda, nayambitsa chipolowe mumzindamo. Adathamangira ku nyumba ya Yasoni, kukafuna Paulo ndi Silasi kuti aŵatulutsire ku anthu.

6Poona kuti sadaŵapeze, adamtenga Yasoniyo pamodzi ndi abale ena nkuŵaguzira kwa akulu amumzindamo. Tsono adafuula kuti, “Anthu aja amene akhala nasokoneza anthu ponseponse, tsopano afikanso kwathu kuno,

7ndipo Yasoni waŵalandira. Onseŵa akuchita zosagwirizana ndi malamulo a Mfumu ya ku Roma, pakunena kuti ati kulinso mfumu ina, dzina lake Yesu.”

8Mau ameneŵa adautsa mitima ya anthuwo ndi ya akulu amumzinda aja.

9Koma Yasoni ndi anzake aja atalipira mlanduwo, akuluwo adaŵamasula.

Za ku Berea

10Kutangoda, abale aja adapititsa Paulo ndi Silasi ku Berea. Atafika kumeneko, adakaloŵa m'nyumba yamapemphero ya Ayuda.

11Ayuda akumeneko anali a mitima yomasuka, kusiyana ndi aja a ku Tesalonika. Iwoŵa adalandira mau a Mulungu ndi mtima wofunitsitsa, ndipo tsiku ndi tsiku ankafufuza m'Malembo kuti aone ngati nzoona zimene Paulo ndi Silasi ankanena.

12Motero mwa iwowo ambiri adakhulupirira, ndiponso Agriki ambiripo, akazi apamwamba ndi amuna omwe, adakhulupirira.

13Koma Ayuda a ku Tesalonika aja atamva kuti Paulo adalalika mau a Mulungu ndi ku Berea komwe, adakafika komwekonso, nayamba kukolezera ndi kuutsa mitima ya anthu.

14Nthaŵi yomweyo abale aja adatuma anthu ena kuti aperekeze Paulo ku nyanja, koma Silasi ndi Timoteo adakhalira komweko.

15Anthu amene adaaperekeza Paulo aja adakafika naye mpaka ku Atene. Pambuyo pake adabwerera ku Berea, Paulo ataŵalamula kukauza Silasi ndi Timoteo kuti amlondole msanga.

Za ku Atene

16Pamene Paulo ankadikira Silasi ndi Timoteo ku Atene, mtima wake udavutika kwambiri poona kuti mzinda wonse ngwodzaza ndi mafano.

17Tsono adakambirana m'nyumba yamapemphero ndi Ayuda ndi anthu ena opembedza Mulungu. Adakambirananso ndi anthu amene ankangokumana nawo pa msika tsiku ndi tsiku.

18Anzeru enanso a magulu a Aepikurea ndi Astoiki adadzatsutsana naye. Ena ankati, “Kodi mbutuma yolongololayi ikufunanso kunena chiyani?” Enanso ankati, “Ameneyu akukhala ngati wolalika za milungu yachilendo.” Ankanena zimenezi chifukwa iye ankalalika Uthenga Wabwino wonena za Yesu, ndi za kuuka kwa akufa.

19Tsono adapita naye ku bwalo lamilandu lotchedwa Areopagi, namuuza kuti, “Ife timati mutidziŵitseko zatsopano zimene mukuphunzitsazi?

20Pakuti zina zimene mukutiwuzazi nzachilendo, ndipo tikufuna kudziŵa kuti zinthuzi nzotani.”

21Ndiye kuti nzika za ku Atene ndi alendo okhala kumeneko, inali ngati ntchito nthaŵi zonse kumangomvera zatsopano ndi kumazifotokozera.

22Paulo adaimirira pakati pa bwalo lija la Aeropagi nati, “Inu anthu a ku Atene, pa zonse ndikuwona kuti ndinu anthu opembedza kwambiri.

23 Adatsimikizira anthu onse zimenezi pakuukitsa Munthuyo kwa akufa.”

32Pamene anthuwo adamva za kuuka kwa akufa, ena adangoseka. Koma ena adati, “Bwanji mudzatiwuzenso zimenezi tsiku lina.”

33Choncho Paulo adaŵasiya.

34Koma ena adamtsata, nakhulupirira. Pakati pao panali Dionizio, mmodzi mwa a bwalo la milandu lotchedwa Areopagi, ndiponso mai wina, dzina lake Damalisi, ndi enanso.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help