Esr. B - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Ahasuwero alengeza za kuzunza Ayuda

1Naŵa mau ake a kalatayo: “Ndine, Ahasuwero, mfumu yaikulu, ndikulembera abwanamkubwa a zigawo zonse 127 za dziko lake, kuyambira ku Indiya mpaka ku Etiopiya, ndiponso kwa nduna zao mau aŵa:

2Ine amene ndili wolamulira mitundu yambiri ya anthu ndi woyendetsa dziko lonse lapansi, ndikufuna ndithu kuti anthu anga azikhala pa mtendere nthaŵi zonse. Sindikuganiza zimenezi chifukwa cha kudzitukumula ndi ulamuliro wanga ai, koma chifukwa ndimayesa nthaŵi zonse kulamulira mwanzeru ndi mwachifundo. Choncho ndaganiza za kukhazikitsa mtendere umene munthu aliyense amafuna. Ndaganizanso za kuchita chotheka kuti m'dziko langa lonse mukhale mtendere ndi ufulu wa kuyendamo ponseponse mosavutika.

3Ndidafunsa aphungu anga m'mene ndingafikire pa cholinga changacho, ndipo Hamani adaperekapo maganizo ake. Hamani ameneyu ndi munthu wodziŵika kwambiri pakati pathu chifukwa cha nzeru zake. Ngwodziŵikanso chifukwa cha kufuna kwake kwabwino ndi kukhulupirika kwake kosalekeza. Ndiye chifukwa cha makhalidwe akewo, adalandira udindo waukulu wa kukhala wachiŵiri m'dziko mwathu muno.

4“Hamaniyo adatisimbira zakuti, pakati pa mitundu ya dziko lapansi, pakupezeka mtundu umodzi wovuta kwabasi. Mtundu umenewu anthu ake ali ndi malamulo osiyana ndi malamulo opezeka m'mitundu ina yonse. Ndiponso anthu ameneŵa nthaŵi zonse amakana malamulo a mafumu athu. Tsono chifukwa cha chimenechi sitikutha kukhazikitsa umodzi m'maiko mwathu, monga momwe tikufunira.

5Tikuwona kuti anthu a mtundu umenewu wokha nthaŵi zonse amachita zotsutsana ndi anthu ena onse. Amatsata miyambo yachilendo ndi malamulo aoao, ndipo amadana ndi boma lathu. Motero akuipitsa dziko lino, mpaka ife kulephera kukhazikitsa mtendere m'dziko mwathu.

6Nchifukwa chake tikulamula kuti aphedwe anthu onse amene Hamani, nduna yathu yaikulu ndi bambo wathu wachiŵiri, adaŵatchula m'makalata mwake. Aonongedwe ndithu onse, amuna ndi akazi ndi ana omwe, popanda chisoni konse, chaka chonchino, pa tsiku la 14 la Adara, mwezi wa khumi ndi chiŵiri.

7Chifukwa choti anthu ameneŵa akhala akuvutitsa pa nthaŵi yaitali, ayenera kuphedwa pa tsiku limodzi, kuti dziko lathu likhale lamtendere ndi lopanda vuto.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help