Yer. 46 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Zakuti mfumu ya ku Babiloni idzagonjetsa Ejipito

1Chauta adauza mneneri Yeremiya mau onena za anthu a mitundu ina.

2 Yes. 19.1-25; Ezek. 29.1—32.32 Kunena za Ejipito, adanena za gulu lankhondo la Farao Neko, mfumu ya ku Ejipito, limene Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adaligonjetsa ku Karikemisi ku mtsinje wa Yufurate pa chaka chachinai cha ufumu wa Yehoyakimu, mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda. Adati,

3“Konzani zishango ndi malihawo,

yambanipo wa ku nkhondo.

4Mangani akavalo,

ndipo amene amakwerapo akwere.

Khalani pa mzere mutavala zisoti zanu.

Nolani mikondo yanu,

valani malaya anu achitsulo.

5Koma tsopano ndikuwona chiyani?

Achita mantha, abwerera.

Ankhondo ao agonjetsedwa.

Akuthaŵa kaŵeraŵera, osacheukanso m'mbuyo.

Agwidwa ndi mantha ponseponse,”

akutero Chauta.

6Waliŵiro sangathe kupulumuka.

Ngakhale wankhondo wamphamvu

sangathe kudzipulumutsa.

Akunka naphunthwa,

kumagwa kumpoto kwa mtsinje wa Yufurate.

7“Kodi ndani akukwera ngati mtsinje wa Nailo,

ngati mitsinje ya madzi achigumula?

8Ejipito akukwera ngati mtsinje wa Nailo,

ngati mitsinje ya madzi achigumula.

Akuti,

‘Ndidzambatuka ndi kuliphimba dziko lapansi.

Ndiwononga mizinda ndi anthu ake.’

9Tiyeni inu akavalo,

thamangani inu magaleta.

Pitani patsogolo inu ankhondo,

inu anthu a ku Etiopiya ndi a ku Puti,

ogwira zishango,

ndiponso inu anthu a ku Ludi,

akatswiri pogwira uta.

10Koma tsikulo ndi tsiku la Chauta Wamphamvuzonse,

tsiku lolipsira,

lolipsira adani ake.

Lupanga lake lidzaŵaononga,

lidzakhuta magazi,

lidzachita kuledzera nawo.

Ambuye Chauta Wamphamvuzonse akukonzera nsembe

ku dziko lakumpoto, pafupi ndi mtsinje wa Yufurate.

11Pita ku Giliyadi, ukatenge mankhwala,

namwali iwe Ejipito.

Wayesayesa mankhwala ambiri koma walephera,

matenda akowo sadzachira.

12Anthu a mitundu ina amva za manyazi ako,

kulira kwako kwadzaza dziko lapansi.

Ankhondo akunka nagwetsanagwetsana,

onse pansi ndu kugwera limodzi.”

Za kubwera kwa Nebukadinezara

13 Yer. 43.10-13 Naŵa mau amene Chauta adalankhula ndi mneneri Yeremiya za kubwera kwa Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, kudzathira nkhondo dziko la Ejipito:

14“Mulengeze ku Ejipito,

mulalike ku Migidoli, ku Memfisi ndi ku Tapanesi.

Anthu akumeneko muŵauze kuti,

‘Imani pamalo panu, mukhale okonzeka

chifukwa chakuti nkhondo idzaononga

zonse pokuzungulirani.’

15Chifukwa chiyani mulungu wanu Apisi wathaŵa?

Chifukwa chiyani nkhunzi yanu yoipembedza ija

sidalimbike?

Nchifukwa choti Chauta waigwetsa.

16Anthu ako akukhumudwa, akugwerana.

Aliyense akunena kuti,

‘Nyamukani, tiyeni tizibwerera kwathu,

kudziko kumene tidabadwira,

tithaŵe lupanga la adani athuŵa!’

17Farao, mfumu ya ku Ejipito,

mpatseni dzina lakuti ‘Waphokoso, wotaya mwai wake.’

18“Pali Ine ndemwe!” Ikutero Mfumu,

imene dzina lake ndi Chauta Wamphamvuzonse.

Wina wamphamvu adzabwera

wonga ngati Tabori phiri lopambana mapiri ena,

wonga ngati phiri la Karimele,

loti joo m'mbali mwa nyanja.

19Konzani katundu wanu wopita naye ku ukapolo,

inu anthu a ku Ejipito,

pakuti Memfisi adzasanduka chipululu,

ngati bwinja, mopanda anthu.

20“Ejipito ali ngati mwanawang'ombe wokongola.

Koma chimphanga chochokera kumpoto chidzamtera.

21Ankhondo aganyu amene ali nawo,

ali ngati anaang'ombe onenepa.

Nawonso abwerera m'mbuyo nathaŵa pamodzi,

palibe amene walimbikira.

Ndithu, nthaŵi ya tsoka yaŵafikira,

ndiyo nthaŵi yoŵalanga!

22“Liwu la Ejipito likunga ngati la njoka yothaŵa,

chifukwa choti adani ake abwera ndi zida zao,

kubwera ndi nkhwangwa,

ngati anthu odula mitengo.

23Adzaduladi nkhalango ya ku Ejipito

ngakhale njoŵirira,

chifukwa anthuwo ndi ochuluka ngati dzombe,

sangathe kuŵerengeka.

24Anthu a ku Ejipito adzachitadi manyazi,

adzatengedwa ukapolo ndi anthu akumpoto,”

akutero Chauta.

25Chauta Wamphamvuzonse, Mulungu wa Israele, wanena kuti, “Ndidzalanga Amoni, mulungu wa Thebesi. Ndidzalanganso Farao ndi Ejipito pamodzi ndi milungu yake ndi akalonga ake. Ndidzalanga Farao ndi onse amene amamkhulupirira.

26Ndidzaŵapereka kwa amene afuna kuŵaononga, ndiye kuti kwa Nebukadinezara, mfumu ya ku Babiloni, ndi atsogoleri ake a ankhondo. Komabe patapita nthaŵi, Ejipito adzakhalanso ndi anthu monga kale,” akutero Chauta.

Zakuti Chauta adzapulumutsa anthu ake

27 Yer. 30.10, 11 “Koma iwe Yakobe, mtumiki wanga, usachite mantha,

Iwe Israele, usataye mtima,

chifukwa ndidzakupulumutsa kuchokera ku maiko akutali.

Ndidzapulumutsanso zidzukulu zako

kuchokera kumaiko kumene adapita nazo ku ukapolo.

Yakobe adzabwerera, nadzapumula pabwino, ndi pa mtendere.

Palibe winanso amene adzamuwopsa.”

28Chauta akunena kuti,

“Iwe Yakobe, mtumiki wanga, usachite mantha,

pakuti Ine ndili nawe.

Ndidzaonongeratu mitundu yonse ya anthu

a kumaiko kumene ndidakupirikitsira.

Koma iweyo sindidzakuwononga kotheratu ai.

Kulanga ndidzakulanga monga m'mene kuyenera,

sindingakulekelere osakulanga konse.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help