Yer. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Aŵa ndi mau a Yeremiya, mwana wa Hilikiya, mmodzi mwa ansembe a ku Anatoti, m'dziko la Benjamini.

22Maf. 22.3—23.27; 2Mbi. 34.8—35.19 Chauta adalankhula naye pa nthaŵi ya Yosiya, mfumu ya ku Yuda, mwana wa Amoni, pa chaka cha khumi ndi chitatu cha ufumu wake.

32Maf. 23.36—24.7; 2Mbi. 36.5-8; 2Maf. 24.18—25.21; 2Mbi. 36.11-21 Chauta adalankhula nayenso pa nthaŵi ya Yehoyakimu, mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda, mpaka mwezi wachisanu wa chaka cha khumi ndi chimodzi cha Zedekiya, mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda, pamene anthu a ku Yerusalemu adatengedwa ukapolo.

Mulungu aitana Yeremiya kuti akhale mneneri

4Chauta adandiwuza kuti,

5“Ndisanakulenge m'mimba mwa mai wako,

ndinali nditakudziŵa kale.

Usanabadwe nkomwe,

ndinali ntakupatula kale,

ndidakuika kuti ukhale mneneri

kwa anthu a mitundu yonse.”

6Ine ndidati, “Ha, Ambuye Chauta!

Ine ndine mwana,

kulankhula sindidziŵa.”

7Koma Iye adandiyankha kuti,

“Usati, ‘Ndine mwana.’

Udzapita ndithu kwa anthu onse kumene ndidzakutuma,

ndipo chilichonse chimene ndidzakulamula udzachilankhula.

8Usaŵaope,

Ine ndili nawe, ndidzakupulumutsa,”

akuterotu Chauta.

9Tsono Chauta adatambalitsa dzanja lake nakhudza pakamwa panga. Ndipo adandiwuza kuti,

“Tamvera, ndikuika mau anga m'kamwa mwako.

10Ndikukuika lero kuti ukhale ndi ulamuliro

pa maiko a anthu ndi maufumu ao,

kuti uzule ndi kugwetsa,

kuti uwononge ndi kugumula,

kuti umange ndi kubzala.”

Yeremiya aona zinthu m'masomphenya

11Chauta adandifunsa kuti, “Yeremiya, kodi ukuwona chiyani?” Ine ndidayankha kuti, “Ndikuwona nthambi ya mtowo.”

12Chauta adati, “Waona bwino. Ineyo ndikuwonetsetsa kuti zichitikedi zimene ndidanena.”

13Chauta adandifunsa kachiŵiri kuti, “Kodi ukuwona chiyani?” Ine ndidayankha kuti, “Ndikuwona mbiya yogaduka, yafulatira kumpoto.”

14Apo Iye adandiwuza kuti, “Ndiye kuti tsoka la anthu a m'dziko lino lidzachokera kumpoto.

15Ndikuitana anthu a mafuko onse a maufumu akumpoto,” akuterotu Chauta. “Mafumu ao adzabwera, aliyense adzaika mpando wake waufumu pa zipata za Yerusalemu, ndiponso pozungulira malinga ake. Iwo adzazinganso mizinda yonse ya Yuda.

16Ndidzatulutsa mlandu wanga wotsutsa anthu anga, chifukwa cha zoipa zimene adachita pakundisiya Ine. Adafukiza lubani kwa milungu ina, namapembedza zimene adapanga ndi manja ao.

17Koma iwe Yeremiya, ukonzeke. Nyamuka, ukaŵauze zonse zimene ndikukulamula. Iwowo asakuwopse, kuwopa kuti Ineyo ndingakuwopse iwo akuwona.

18Lero ine ndikukulimbitsa ngati mzinda wamalinga, mzati wachitsulo, ndiponso ngati makoma amkuŵa, kuti usachite mantha ndi wina aliyense m'dziko lonse, kaya ndi mafumu a ku Yuda, nduna zakumeneko, ansembe kapena anthu wamba.

19Iwo adzalimbana nawe, koma sadzakupambana, pakuti ine ndili nawe ndipo ndidzakupulumutsa,” akuterotu Chauta.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help