1 Yer. 51.13 Pambuyo pake mmodzi mwa angelo asanu ndi aŵiri aja, amene anali ndi mikhate isanu ndi iŵiri ija, adadzalankhula nane. Adati, “Tiye kuno ndikakuwonetse m'mene akukaweruzidwira mkazi wadama wotchuka uja, amene akukhala pambali pa madzi ambiri.
2Yes. 23.17; Yer. 51.7Mafumu a pa dziko lapansi ankachita naye chigololo, ndipo anthu okhala pa dziko lapansi ankaledzera naye vinyo wa dama lakelo.”
3 Chiv. 13.1 Tsono mngelo uja adanditenga chamumzimu kupita nane ku chipululu. Kumeneko ndidaona mkazi atakhala pa chilombo chofiira. Pathupi ponse chilombocho chidaalembedwa maina onyozera Mulungu. Chinali ndi mitu isanu ndi iŵiri ndi nyanga khumi.
4Yer. 51.7Mkaziyo adaavala zovala zofiirira ndi zamlangali, ndipo adaadzikongoletsa ndi golide, ndi ngale zamtengowapatali zamitundumitundu. M'manja mwake anali ndi chikho chagolide chodzaza ndi zonyansa, ndi zoipa za ntchito zake zadama.
5Pamphumi pake padaalembedwa dzina lachinsinsi lakuti, “Babiloni wotchuka uja, manthu wa achiwerewere onse, ndi a zonyansa zonse za dziko lapansi.”
6Ndipo ndidaona kuti mkaziyo anali ataledzera ndi magazi a anthu a Mulungu, ndi a anthu ophedwera umboni wa Yesu.
Nditamuwona mkaziyo, ndidadabwa kwambiri.
7Koma mngelo uja adandifunsa kuti, “Ukudabwiranji? Ndikuululira chinsinsi chake cha mkazi ameneyu, ndi cha chilombo chimene iye wakwerapo, chokhala ndi mitu isanu ndi iŵiri ndi nyanga khumi.
8Dan. 7.7; Chiv. 11.7; Mas. 69.28Chilombo chimene unachiwona chija, kale chidaali chamoyo, koma tsopano sichilinso chamoyo. Chiyenera kutuluka kuchokera m'chiphompho chija kupita kukaonongedwa. Anthu onse okhala pa dziko lapansi, amene chilengedwere dziko lapansi maina ao sadalembedwe m'buku la amoyo, azidzadabwa poona chilombocho. Azidzadabwa poona kuti kale chidaali chamoyo koma tsopano sichilinso chamoyo, komabe m'tsogolo muno chidzaonekanso.
9“Pano pafunika nzeru ndi kumvetsa bwino: Mitu isanu ndi iŵiri ija, ikufanizira mapiri asanu ndi aŵiri amene mkazi uja amakhalapo.
10Ikufaniziranso mafumu asanu ndi aŵiri. Mwa iwo, asanu adagwa, imodzi ikulamulirabe, imodzi inayo siinafikebe. Koma ikadzafika, idzayenera kungokhala kanthaŵi.
11Tsono chilombo chija chimene kale chidaali chamoyo, koma tsopano si chamoyonso, chikufanizira mfumu yachisanu ndi chitatu ichocho, komabe ndi imodzi mwa mafumu asanu ndi aŵiri aja, ndipo ikupita kukaonongedwa.
12 Dan. 7.24 “Nyanga khumi zimene unaona, zikufanizira mafumu khumi amene asanayambebe kulamulira. Koma adzalandira mphamvu zolamulira ngati mafumu pa ora limodzi, pamodzi ndi chilombo chija.
13Mafumu khumi ameneŵa, cholinga chao ndi chimodzi, ndipo amapereka mphamvu zao ndi ulamuliro wao m'manja mwa chilombo chija.
14Iwoŵa adzachita nkhondo ndi Mwanawankhosa uja. Koma Mwanawankhosayo adzaŵagonjetsa, pakuti ndi Mbuye wa ambuye onse, ndi Mfumu ya mafumu onse. Ndipo anthu ake oitanidwa, osankhidwa ndi okhulupirika, nawonso adzapambana pamodzi naye.”
15Mngelo uja adandiwuzanso kuti, “Madzi unaona aja amene mkazi wadama uja wakhalapo, akufanizira mitundu ya anthu, makamu a anthu, mafuko a anthu ndiponso anthu a zilankhulo zosiyanasiyana.
16Tsono nyanga khumi unaona zija, pamodzi ndi chilombo chija, zidzadana naye mkazi wadamayo. Zidzamlanda zake zonse ndi kumsiya maliseche. Zidzadyako mnofu wake, kenaka nkumuponya pa moto kuti apserere.
17Zidzaterodi, pakuti Mulungu adazipatsa mtima wofuna kuchita zimene Iye adazikonzeratu. Zimenezi nzakuti zidzagwirizana pakupereka mphamvu zake zolamulira kwa chilombo chija, mpaka zitachitika zonse zimene Mulungu adanena.
18“Mkazi unaona uja akufanizira mzinda waukulu uja wolamulira mafumu onse a pa dziko lapansi.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.