1Ndine, Paulo, mtumwi wa Khristu Yesu, monga adalamulira Mulungu, Mpulumutsi wathu, ndiponso Khristu Yesu, chiyembekezo chathu.
2 Ntc. 16.1 Ndikulembera iwe Timoteo, mwana wanga weniweni m'chikhulupiriro.
Mulungu Atate ndi Khristu Yesu Ambuye athu akukomere mtima, akuchitire chifundo ndi kukupatsa mtendere.
Achenjere ndi zophunzitsa zonama3Pamene ndinkanyamuka kupita ku Masedoniya, paja ndidaakupempha kuti ukhalire ku Efeso. Kuli anthu ena kumeneko amene akuphunzitsa zina zachilendo, ndiye ndikufuna kuti iweyo uŵaletse.
4Uŵauze kuti aleke kumangoika mtima pa nthano zopeka, ndi pa kufufuza kosalekeza dongosolo la maina a makolo. Zimenezi zimangoutsa mikangano chabe, siziphunzitsa konse zimene Mulungu adakonzeratu, zomwe zimadziŵika pakukhulupirira.
5Cholinga changa pokupatsa malangizo ameneŵa, nchakuti pakhale chikondi chochokera mu mtima woyera, mu mtima wopanda kanthu koutsutsa, ndiponso m'chikhulupiriro chopanda chiphamaso.
6Anthu ena adapatuka pa zimenezi, ndipo adasokera nkumatsata nkhani zopanda pake.
7Iwo amafuna kukhala aphunzitsi a Malamulo a Mulungu, chonsecho samvetsa zimene iwo omwe akunena kapena zimene akufuna kutsimikiza.
8Tikudziŵa kuti Malamulo ngabwino, malinga nkuŵagwiritsa ntchito moyenera.
9Koma mumvetsetse kuti saika malamulo chifukwa cha anthu olungama, koma chifukwa cha anthu osamvera, ndi osaweruzika, anthu ochimwa ndi osapembedza, monga anthu opha atate ao, amai ao, kapena anthu ena.
10Malamulo amaŵaika chifukwa cha anthu adama, ochimwa ndi amuna anzao, oba anthu, amabodza, olumbira monama, ndi ochita chilichonse chotsutsana ndi chiphunzitso choona.
11Chiphunzitso choonacho chimapezeka mu Uthenga Wabwino wonena za ulemerero wa Mulungu wolemekezeka, umene Iye mwini adandisungiza.
Athokoza Mulungu chifukwa cha chifundo chake12Ndikuthokoza Khristu Yesu Ambuye athu, amene adandipatsa mphamvu pa ntchitoyi. Ndikumthokoza pondiwona wokhulupirika nandipatsa ntchito yomtumikira,
13Ntc. 8.3; 9.4, 5ngakhale kuti kale ndinkamuchita chipongwe, kumzunza ndi kumnyoza. Koma Mulungu adandichitira chifundo chifukwa ndinkazichita mosadziŵa, poti ndinali wopanda chikhulupiriro.
14Ambuye athu adandikomera mtima koposa, nkundipatsa chikhulupiriro ndi chikondi zimene tili nazo chifukwa chogwirizana ndi Khristu Yesu.
15Aŵa ndi mau otsimikizika, oyenera kuŵavomereza ndi mtima wonse, akuti Khristu Yesu adabwera pansi pano kuti adzapulumutse anthu ochimwa. Ndipo mwa iwowo ine ndiye wochimwa koposa.
16Koma Mulungu adandichitira chifundo, kuti mwa ine, wochimwa koposane, Khristu Yesu aonetse kuleza mtima kwake konse. Adafuna kuti ndikhale chitsanzo cha kuŵalezera mtima onse amene adzamkhulupirire kuti alandire moyo wosatha.
17Kwa Mfumu yamuyaya, yosafa, yosaoneka, amene Iye yekha ndiye Mulungu, kukhale ulemu ndi ulemerero mpaka muyaya. Amen.
Mau ena a Paulo olangiza Timoteo18Iwe Timoteo, mwana wanga, ndikukupatsa malangizo ameneŵa molingana ndi zimene aneneri adaanenapo kale za iwe. Mau amenewo akuthandize kumenya nkhondo yabwino,
19uli ndi chikhulupiriro ndiponso ndi mtima wopanda kanthu koutsutsa. Ena sadamvere pamene mtima wao unkaŵatsutsa, motero chikhulupiriro chao chidaonongeka.
20Mwa iwowo wina ndi Himeneo, wina Aleksandro, anthu amene ndaŵapereka kwa Satana kuti aphunzire kusanyoza Mulungu mwachipongwe.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.