1Samuele atakalamba, adaika ana ake kuti akhale oweruza Aisraele.
2Mwana wake wachisamba anali Yowele, wachiŵiri anali Abiya. Iwoŵa ankaweruza ku Beereseba.
3Koma ana akewo sanali ndi makhalidwe abwino a bambo wao, ankapotokera ku zoipa, namatsata phindu. Ankalandira ziphuphu, namaweruza milandu mopanda chilungamo.
4Tsono akuluakulu onse a Aisraele adasonkhana nadza kwa Samuele ku Rama.
5Deut. 17.14 Adamuuza kuti, “Taonani, inu tsopanotu mwakhwima, ndipo ana anu sali ndi makhalidwe onga anu. Tsono mutipatse mfumu kuti izitilamulira, monga m'mene ikuchitira mitundu ina ya anthu.”
6Mau ameneŵa akuti “Mutipatse mfumu yoti izitilamulira” sadamkondwetse Samuele. Nchifukwa chake Samueleyo adapemphera kwa Chauta.
7Apo Chauta adayankha kuti, “Umvere zonse zimene anthuwo akukuuza. Sakukana iwe koma Ine. Sakufuna kuti ndikhale mfumu yao.
8Kuyambira tsiku limene ndidaŵatulutsa ku Ejipito mpaka pano, zochita zao nzokhazokha za kundikana ine ndi kutumikira milungu ina. Tsono nawenso akukuchita zomwezo.
9Motero tsono umvere zimene iwowo akunena. Koma ndiye uŵachenjeze kwambiri, ndipo uŵauzitse za mkhalidwe wake wa mfumu imene izidzaŵalamulirayo.”
10Choncho Samuele adaŵauza anthu amene ankafuna mfumu aja mau onse a Chauta.
11Adati, “Izi ndizo zimene mfumu yanuyo izidzakuchitani: izidzakulandani ana anu aamuna kuti akhale ankhondo, ena pa magaleta ake ankhondo, ena pa akavalo ake, ndipo ena othamanga patsogolo pa magaletawo.
12Ena idzaŵaika kuti akhale olamulira ankhondo chikwi chimodzi kapena makumi asanu. Ndipo ena azidzalima kumunda kwake ndi kumakolola zolima zake, kusula zida zankhondo ndiponso zipangizo za magaleta ankhondo.
13Izidzatenga ana anu aakazi kuti azidzayenga mafuta onunkhira, ndi kumaphika chakudya ndi kumapanga buledi.
14Idzakulandani minda yanu yabwino kwambiri, minda yanu yamphesa ndi yaolivi, kudzanso minda yanu yazipatso, ndi kuipatsa nduna zake.
15Idzalanda gawo lachikhumi la tirigu wanu ndi la mphesa zanu, nidzapatsa kwa akapitao ake ndi nduna zake.
16Idzakulandani antchito anu aamuna ndi adzakazi anu. Idzakulandaninso ng'ombe zanu zonenepa ndi abulu anu, ndi kumazigwiritsa ntchito zake.
17Idzalanda chigawo chachikhumi cha nkhosa zanu, ndipo inuyo mudzakhala akapolo ake.
18Nthaŵi imeneyo ikadzafika, mudzalira komvetsa chisoni chifukwa cha mfumu imene mwadzisankhirayo, koma Chauta sadzakuyankhani.”
19Koma anthuwo adakana kumvera mau a Samuele. Adati, “Iyai! Ife tikufuna mfumu yotilamulira.
20Tikufuna kuti nafenso tikhale ngati mitundu ina yonse, ndipo kuti mfumu yathu izitiweruza, kutitsogolera ndi kumatimenyera nkhondo.”
21Samuele atamva mau onse a anthuwo, adakakambira Chauta mau onsewo.
22Tsono Chauta adauza Samuele kuti, “Umvere zimene akunena, ndipo uŵapatse mfumu.” Choncho Samuele adauza Aisraelewo kuti, “Nonse bwererani kwanu.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.