1 Yer. 49.1-6; Ezek. 21.28-32; Amo. 1.13-15; Zef. 2.8-11 Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,
2“Iwe mwana wa munthu, tembenukira kwa anthu a ku Amoni, ulalike zoŵadzudzula.
3Unene kuti, inu Aamoni, imvani mau a Ambuye Chauta akuti, ‘Paja mudatchula mau onyodola, mutaona malo anga opatulika akuipitsidwa, nthaka ya Israele itaguga, ndipo anthu a ku Yuda atatengedwa ukapolo.
4Nchifukwa chake ndidzakuperekani m'manja mwa anthu akuvuma. Adzakhoma mahema ao ndi kumanga nyumba zao m'dziko mwanu. Adzakudyerani zipatso zanu, adzakumwerani mkaka wanu.
5Ndidzasandutsa Raba kuti akhale busa la ngamira, ndipo ndidzasandutsa mizinda ya Aamoni kuti ikhale makola a nkhosa. Motero mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.
6Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Mudaomba m'manja ndi kulumphalumpha mokondwa, ndipo mudanyodola dziko la Israele ndi kulinyoza ndi mtima wonse.
7Nchifukwa chake Ine ndidzakukanthani ndi dzanja langa ndipo ndidzakuperekani kuti mukhale chofunkha cha mitundu ina ya anthu. Ndidzakuchotsani pakati pa mitundu ina ya anthu, ndipo ndidzakufafanizani pa dziko lapansi. Ndidzakuwonongeranitu, ndipo mudzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.’
Za chilango cha Mowabu8 Yes. 15.1—16.14; 25.10-12; Yer. 48.1-47; Amo. 2.1-3; Zef. 2.8-11 “Mau a Ine Ambuye Chauta ndi aŵa: Chifukwa choti Mowabu adanena kuti a ku Yuda ali ngati anthu ena onse,
9ndidzagumula mbali ina ya Mowabu, ndidzaononga mizinda yake yakumalire, ndiye kuti mizinda ija yokongola kwambiriyi ya Beteyesimoti, Baala-Meyoni ndi Kiriyataimu.
10Ndidzapereka Amowabu pamodzi ndi Aamoni m'manja mwa mitundu yakuvuma, kotero kuti Aamoni adzaiŵalikiratu pakati pa mitundu ya anthu.
11Amowabunso ndidzaŵalangadi. Motero adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”
Za chilango cha Edomu12 Yes. 34.5-17; 63.1-6; Yer. 49.7-22; Ezek. 35.1-15; Amo. 1.11, 12; Oba. 1.1-14; Mal. 1.2-5 “Zimene ndikunena Ine Ambuye Chauta ndi izi: Chifukwa choti Edomu adalipsira Yuda mwankhanza, adapalamula kwambiri pakutero.
13Choncho Edomuyo ndidzamkantha ndi dzanja langa, ndipo ndidzaononga anthu pamodzi ndi nyama zomwe kumeneko. Dzikolo ndidzalisandutsa chipululu kuyambira ku Temani mpaka ku Dedani. Anthu ambiri adzaphedwa pa nkhondo.
14Ndidzalanga Edomu ndi dzanja la anthu anga Aisraele. Adzamchita monga m'mene mkwiyo wanga ndi ukali wanga udzafunire. Choncho adzaona kulipsira kwanga. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.
Za chilango cha Filistiya15 Yes. 14.29-31; Yer. 47.1-7; Yow. 3.4-8; Amo. 1.6-8; Zef. 2.4-7; Zek. 9.5-7 “Mau a Ine Ambuye Chauta ndi aŵa: Afilisti adalanga anthu anga mwankhanza ndi kuŵalipsira ndi mtima wonyoza ndi wofuna kuŵaononga malinga ndi chidani chao chachikhalire.
16Nchifukwa chake Afilistiwo ndidzaŵakantha ndi dzanja langa. Ndidzafafaniza Akereti ndi kuwononga ena onse okhala m'mbali mwa nyanja.
17Ndidzaŵalipsira koopsa ndi kuŵalanga mwaukali kwambiri. Ndikadzaŵalanga choncho, adzadziŵa kuti Ine ndine Chauta.”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.