Esr. E - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mfumu ikhazikitsa lamulo lokomera Ayuda

1Naŵa mau ake a m'kalatayo: “Ndine, Ahasuwero, mfumu yaikulu, ndikuti moni kwa abwanamkubwa a zigawo zonse 127 za dziko langa kuyambira ku Indiya mpaka ku Etiopiya, ndiponso kwa onse otumikira boma lathu.

2Anthu ochuluka amadzikuza kwambiri akaŵachitira ulemu ndi kuŵachitira zinthu zabwino.

3Samangolephera kuzigwiritsa ntchito zabwino zimene azilandira, komanso amavutitsa anthu athu, mpaka kuŵachita chiwembu anthu oŵachitira zabwino.

4Samangochotsa khalidwe la kuthokoza m'mitima ya anthu, komanso amadzikuza pomvera matamando a anthu osadziŵa konse zachifundo. Amaganiza kuti Mulungu amene amadziŵa zonse ndi kudana ndi zoipa sangaŵalange.

5Kaŵirikaŵiri amene ali ndi ulamuliro waukulu akhala akuumirizidwa ndi abwenzi ao a maudindo ena m'maboma kuti aŵathandize kupha anthu osapalamula kapena kuŵagwetsa m'zodetsa nkhaŵa zina zosatha kuziwongolanso.

6Abwenzi ameneŵa, chifukwa cha mabodza ao ndi makhalidwe ao onyenga, amaipitsa makhalidwe abwino a mafumu ao.

7“Zitsanzo za m'mene anthuwo ankagwirira ntchito moipa pa nthaŵi imene ankalamulira mwankhanza, tingathe kuziwona osati m'nkhani za masiku amakedzana zokha zimene ife lero tikuzidziŵa, komanso pa zinthu zimene zakhala zikuchitika pakati pathu masiku omwe ano.

8Tikufuna kuti kutsogoloko dziko lathu lidzakhale lamtendere ndi lopanda mavuto kwa anthu onse.

9Zimenezi zingathe kutheka titasinthako njira zathu zina ndi kuweruza nkhani zonse mosakondera.

10Mwachitsanzo, ganizirani mlandu wa Hamani, mwana wa Hamedata, wa ku Masedoniya. Adaali mlendo, sanali konse wa ku Persiya, ndipo analibe khalidwe lathu lachifundo, komabe ine nkumulandira.

11Tidamuwonetsa ubwenzi monga timachitira ndi anthu a mitundu yonse, mpaka ndithu kumtchula bambo wathu. Anthu onse ankamuŵeramira pomuwona kuti ngwachiŵiri kwa ine mfumu.

12“Koma iye, ndi kunyada kwake kwakukulu, adafuna kulanda ufumu wathu ndi moyo wathu womwe.

13Ndi nzeru zake zochenjera ndi zonyenga adaayesa kupha Mordekai mpulumutsi wathu ndi munthu wotichitira zabwino nthaŵi zonse. Adaafunanso kupha Estere, mfumukazi yathu yosalakwa, pamodzi ndi anthu onse a mtundu wao.

14Ankafuna kuti ife tikhale ofooka, kuti choncho anthu a ku Masedoniya adzalande dziko lathu la Persiyali.

15Koma Ayuda amene munthu woipitsitsayo adaafuna kuŵaononga, ife tikuwona kuti si anthu ovuta mpang'ono pomwe. Amatsata malamulo olungama,

16ndipo amapembedza Mulungu wamoyo, Wopambanazonse ndi wamphamvu kwambiri. Ndipo Mulungu ameneyu wakhala akusunga bwino kwambiri dziko lathu, kuyambira nthaŵi ya makolo athu mpaka lero lino.

17“Nchifukwa chake ine ndikukuchenjezani kuti musachite zimene zidalembedwa m'makalata amene adaatumiza Hamani, mwana wa Hamedata uja.

18Iyeyo amene adachita zoipa zonsezo, pamodzi ndi banja lake lonse, onse adapachikidwa pa chipata cha mzinda wa Susa. Choncho Mulungu amene amalamulira zinthu zonse, wamulanga moyenera ndi mofulumira.

19Tsono kalata ino muipachike ponseponse poonekera, ndipo Ayuda muŵalole kuti azitsata miyambo yao.

20Ndipo muŵathandize ndi kuŵatchinjiriza kwa anthu ofuna kuŵachita zoipa pa tsiku la chisoni chao, tsiku la 13 la mwezi wa khumi ndi chiŵiri wa Adara.

21Mulungu, amene amalamulira zinthu zonse, wasandutsa tsiku lachiwonongekolo kuti likhale tsiku lachisangalalo kwa anthu ake.

22Tsiku limeneli, muliŵerengere pamodzi ndi masiku ena achikondwerero m'dziko mwanu, kuti muzilisunga.

23Kuyambira lero mpaka m'tsogolo, tsiku limeneli lizidzatikumbutsa ife ndi abale athu a ku Persiya za kupulumuka kwathu. Koma kwa anthu onse amene amatichita chiwembu, lizidzaŵakumbutsa za kuwonongeka kwao.

24Mopanda chifundo konse ndidzasakaza kotheratu mzinda uliwonse ndi dziko lililonse m'mene anthu ake sadzatsata zimene ndalamulazi. Ndidzaithira nkhondo mizindayo nkuitentha ndi moto. Kumeneko sikudzangokhala kosapitika ndi anthu, komanso ngakhale nyama zakuthengo ndi mbalame zidzadana nako mpaka muyaya.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help