1 Eks. 12.1-13 Pa mwezi woyamba wa chaka chachiŵiri Aisraele atatuluka m'dziko la Ejipito, Chauta adauza Mose m'chipululu cha Sinai kuti,
2“Aisraele azichita Paska pa nthaŵi yake.
3Muzichita Paska tsiku la 14 la mwezi uno, madzulo ake. Muzichita Paskayo potsata malamulo ake ndi malangizo ake onse.”
4Choncho Mose adauza Aisraele kuti azichita Paska.
5Ndipo Aisraele adachita Paska pa mwezi woyamba pa tsiku la 14, madzulo ake, m'chipululu cha Sinai. Adachita Paska monga momwe Chauta adaalamulira Mose.
6Panali anthu ena amene anali atadziipitsa chifukwa chokhudza mtembo wa munthu, kotero kuti sadathe kuchita nao Paska pa tsikulo. Motero adabwerera kwa Mose ndi kwa Aroni pa tsiku lomwelo.
7Anthuwo adauza Mose kuti, “Ife ndife oipitsidwa chifukwa tidakhudza mtembo wa munthu. Chifukwa chiyani tikuletsedwa kubwera ndi zopereka zathu kwa Chauta pa nthaŵi yake pakati pa anzathu Aisraele?”
8Mose adayankha kuti, “Dikirani kuti ndimve zimene Chauta alamule za inu.”
9Chauta adauza Mose kuti,
10“Uza Aisraele kuti, munthu wina aliyense mwa inu, kapena mwa zidzukulu zanu, akadziipitsa pokhudza mtembo wa munthu, kapena akakhala paulendo, achitebe Paska ya Chauta.
11Achite pa mwezi wachiŵiri, pa tsiku la 14, madzulo ake. Adye nyama ya Paskayo pamodzi ndi buledi wosafufumitsa ndi ndiwo zoŵaŵa zamasamba.
12Eks. 12.46; Yoh. 19.36 Asasiyeko nyamayo mpaka m'maŵa kapena kuphwanya mafupa ake. Achite Paskayo potsata malamulo ake onse.
13Koma munthu amene sadadziipitse ndipo sali paulendo, komabe akana kuchita Paska, ameneyo achotsedwe pakati pa Aisraele, chifukwa sadabwere ndi zopereka zake kwa Chauta pa nthaŵi yake. Ameneyo adzalangidwa chifukwa cha tchimo lake.
14Mlendo akakhala pakati panu, nafuna kuchita nao Paska ya Chauta, nayenso achite Paskayo potsata malamulo ake ndi malangizo ake. Kaya ndinu alendo kapena ndinu mbadwa, nonse mukhale ndi lamulo limodzi lokha.”
Za mtambo wamoto(Eks. 40.34-38)15Pa tsiku limene adamanga malo opatulika, mtambo udaphimba malo opatulikawo, ndiye kuti chihema chaumboni chija. Madzulo aliwonse mpaka m'maŵa mwake, mtambowo unkaphimba malo opatulika uli ndi maonekedwe a moto.
16Zinkachitika motero mosalekeza. Mtambowo unkaphimba chihema chamsonkhano masana, ndipo usiku unkaoneka ngati moto.
17Mtambowo ukangokwera kuchoka pachihemapo, Aisraele ankanyamuka ulendo; ndipo pamene mtambowo unkakaima, Aisraele ankamanga mahema ao pamalo pamenepo.
18Aisraele ankanyamuka ulendo wao Chauta akaŵalamula, ndipo ankamanga mahema ao Chauta akaŵalamula. Nthaŵi yonse pamene mtambowo unali pa chihemacho, iwo ankakhalabe m'mahema.
19Ngakhale mtambowo ukhale masiku ambiri pamwamba pa chihemacho, Aisraele ankasungabe lamulo la Chauta, ndipo sankanyamuka.
20Nthaŵi zina mtambowo unkaphimba masiku oŵerengeka, ndipo Aisraele ankakhalabe m'mahema potsata malamulo a Chauta. Tsono ankanyamuka ulendo Chauta akaŵalamula.
21Nthaŵi zina mtambowo unkangophimba chihemacho kuyambira madzulo mpaka m'maŵa. M'maŵa mwake mtambowo ukachoka, iwo ankanyamuka ulendo wao. Mwina mtambowo unkaphimba chihema chija tsiku lonse ndi usiku womwe, koma ukangochokapo, iwowo ankanyamuka ulendo wao.
22Ngakhale mtambowo uphimbe pamwamba pa chihema cha Mulungu nkumakhala pomwepo masiku aŵiri kapena mwezi, kapena chaka, kapena nthaŵi yopitirirapo, Aisraele ankakhalabe m'mahema, ndipo sankanyamuka. Koma mtambowo ukangochokapo, iwo ankanyamuka ulendo.
23Aisraele ankamanga mahema ao Chauta akaŵalamula, ndipo ankanyamuka ulendo wao Chauta akaŵalamula. Ankasunga lamulo la Chauta, loŵafikira kudzera mwa Mose.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.