1Chauta mwafufuzafufuza,
ndipo mwandidziŵa.
2Inu mumadziŵa pamene ndikhala pansi,
pamenenso ndidzuka,
mumazindikira maganizo anga muli kutali.
3Mumandipenyetsetsa ndikamayenda ndiponso ndikamagona,
mumadziŵa njira zanga zonse.
4Ngakhale mau anga asanafike pakamwa panga,
Inu Chauta mumaŵadziŵa onse.
5Mumandizinga kumbuyo ndi kutsogolo,
ndipo mumandisanjika dzanja lanu.
6Nzeru zimenezi nzopitirira nzeru zanga,
nzapamwamba, sindingathe kuzimvetsa.
7Ndidzapita kuti, pofuna kupewa Mzimu wanu,
kapena pofuna kuthaŵa nkhope yanu?
8Ndikakwera kumwamba, Inu muli komweko,
ndikagona m'dziko la anthu akufa, Inu muli momwemo.
9Ndikaulukira kotulukira dzuŵa,
kapena kukafika kuzambwe,
ku mathero a nyanja,
10ngakhale kumenekonso mudzanditsogolera,
dzanja lanu lamanja lidzandichirikiza.
11Ndikanena kuti, “Mdima undiphimbe,
kuŵala kumene kwandizinga kusanduke mdima,”
12ngakhale mdimawo, kwa Inu si mdima konse,
kwa Inu usiku umaŵala ngati usana,
mdima uli ngati kuŵala.
13Paja ndinu mudapanga za m'kati mwanga,
mudandiwumba m'mimba mwa amai anga.
14Ndikukutamandani, Inu oopsa ndi odabwitsa.
Ntchito zanu zonse nzodabwitsa.
Mumandidziŵa bwino kwambiri.
15Mapangidwe anga sadabisike pamaso panu
pamene ndinkapangidwa mwachinsinsi,
pamene ndinkaumbidwa mwaluso m'mimba mwa amai anga.
16Maso anu adandiwona ndisanabadwe.
Masiku a moyo wanga mudaŵalemberatu m'buku mwanu,
asanayambe nkuŵerengedwa komwe.
17 Mphu. 18.5-7 Maganizo anu, Inu Mulungu, ndi ozama kwa ine,
ndi osaŵerengeka konse.
18Ndikadaŵaŵerenga, bwenzi ali ambiri koposa mchenga.
Ndikamadzuka ndimakhala nanube.
19Ndikadakonda kuti muwononge anthu oipa, Inu Mulungu,
ndipo kuti anthu okhetsa magazi andichokere.
20Anthuwo amakunenani zinthu zoipa,
namakuukirani ndi mtima woipa.
21Kodi sindidana nawo anthu odana nanu, Inu Chauta?
Kodi sindinyansidwa nawo anthu okuukirani?
22Ndimadana nawo ndi chidani chenicheni.
Ndimaŵayesa adani anga.
23Fufuzeni, Inu Mulungu, kuti mudziŵe mtima wanga.
Yeseni kuti mudziŵe maganizo anga.
24Muwone ngati ndimatsata njira yoipa iliyonse,
ndipo munditsogolere m'njira yanu yamuyaya.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.