1Tsiku lina ena a m'gulu la aneneri adauza Elisa kuti, “Onani, malo tikukhala ndi inu ano akutichepera kwambiri.
2Mutilole tipite ku Yordani, tikadule nsichi imodzi-imodzi, kuti tidzakonze malo oti tizikhalamo.” Elisa adayankha kuti, “Chabwino, pitani.”
3Apo mmodzi mwa iwo adati, “Bwanji inuyo mupite nafe, atumiki anufe.” Elisa adavomera nati, “Tiyeni.”
4Choncho Elisayo adapita nawo. Atafika ku Yordani, anthu aja adayamba kudula mitengo.
5Koma pamene wina ankagwetsa nsichi, nkhwangwa yake idaguluka nigwa m'madzi, ndipo adafuula kuti, “Kalanga ine mbuyanga! Ndipotu nkhwangwa imeneyi njobwereka!”
6Tsono munthu wa Mulungu uja adafunsa kuti, “Kodi yagwera pati?” Atamuwonetsa malowo, Elisa adadula kamtengo nakaponya pamadzipo, nkhwangwayo nkuyandama.
7Ndipo Elisa adati, “Kaitole.” Munthu uja adatambalitsa dzanja, naigwira.
Elisa achititsa khungu ankhondo a ku Siriya8Nthaŵi ina mfumu ya ku Siriya inkamenyana nkhondo ndi Aisraele. Ndipo idapangana ndi aphungu ake kuti, “Tikamange zithando zathu pa malo akutiakuti.”
9Koma mneneri Elisa adatumiza mau kwa mfumu ya ku Israele kuti, “Chenjerani ku malo akutiakutiŵa, poti Asiriya akukabisala kumeneko.”
10Tsono mfumu ya ku Israele idatuma anthu ku malo amene mneneri wa Mulungu uja adaanenaŵa. Umu ndimo m'mene mneneri ankachenjezera mfumu, kotero kuti idapulumuka kangapo konse.
11Tsono mfumu ya ku Siriya inkavutika kwambiri mu mtima chifukwa cha zimenezi. Choncho idaitana aphungu ake niŵafunsa kuti, “Kodi simungandiwuze pakati pathu pano munthu amene akuthandizira mfumu ya ku Israele?”
12Mmodzi mwa aphunguwo adayankha kuti, “Palibe ndi mmodzi yemwe, inu mbuyanga mfumu. Koma Elisa mneneri wa ku Israele ndiye amene amauza mfumu ya ku Israele mau amene inuyo mumalankhula kumbali m'chipinda mwanu.”
13Tsono mfumuyo idati, “Pitani mukaone kumene akukhala, kuti nditumeko anthu, akamgwire.” Anthuwo atabwerako, adamuuza kuti, “Ali ku Dotani.”
14Motero mfumuyo idatumako akavalo ndi magaleta, kudzanso gulu lalikulu la ankhondo. Ankhondowo adakafikako usiku, nazinga mzindawo.
15Tsono wantchito wa munthu wa Mulungu uja, atadzuka m'mamaŵa nkutuluka, adangoona gulu lankhondo lokwera pa akavalo ndi magaleta, litazinga mzinda wonsewo. Pomwepo wantchitoyo adabwerera nati, “Kalanga ine mbuyanga! Kodi titani?”
16Elisa adati, “Usachite mantha, pakuti amene ali pa mbali yathu ngambiri kupambana m'mene aliri iwoŵa.”
17Tsono Elisa adapemphera, adati, “Inu Chauta ndikukupemphani kuti mutsekule maso ake kuti apenye.” Motero Chauta adatsekula maso a wantchito uja, ndipo adangoona kuti phiri lili lodzaza ndi akavalo ndi magaleta amoto atamzungulira Elisa uja.
18Tsono pamene Asiriya adayamba kumthira nkhondo Elisa, iye adapemphera kwa Chauta, adati, “Ndikukupemphani kuti muŵachititse khungu anthu ameneŵa.” Motero Chauta adachititsa ankhondo aja khungu, monga momwe Elisa adapemphera.
19Ndipo Elisa adauza ankhondowo kuti, “Njira si imeneyi, ndipo mzinda si umenewunso ai. Tsatani ine, ndikakufikitsani kwa munthu amene mukumfunafunayo.” Choncho adaŵatsogolera mpaka ku Samariya.
20Atangoloŵa mu mzinda wa Samariyawo, Elisa uja adapemphera kuti, “Inu Chauta, atsekuleni maso anthuŵa apenye.” Choncho Chauta adatsekuladi maso ao, napenya. Ndipo adangoona kuti ali m'kati mwenimweni mwa Samariya.
21Tsono mfumu ya ku Israele itaona ankhondowo, idafunsa Elisa kuti, “Bambo wanga, kodi ndiŵaphe? Kodi ndiŵaphe?”
22Elisa adayankha kuti, “Usaŵaphe ai. Kodi ungaŵaphe anthu amene udachita kuŵagwira ukapolo pomenyana nawo nkhondo? Iyai, koma apatseni chakudya ndi madzi kuti ayambe apeza bwino, kenaka apite kwa mbuyao.”
23Motero adaŵakonzera madyerero aakulu. Atadya ndi kumwa, mfumuyo idaŵalola ankhondowo kuti achoke, ndipo iwo adapita kwa mbuyao. Pambuyo pake magulu ankhondo a Asiriya adaleka kuthira nkhondo dziko la Israele.
Asiriya azinga mzinda wa Samariya24Patapita nthaŵi ndithu, Benihadadi mfumu ya ku Siriya, adasonkhanitsa gulu lake lankhondo, napita kukazinga Samariya ndi zithando zankhondo.
25Ku Samariyako kunali njala yoopsa pa nthaŵi imene Asiriya ankazinga mzindawo ndi zithando zankhondo, mpaka kuti mutu wa bulu ankaugula ndi ndalama zasiliva 80. Ndipo magaramu 200 a zitosi za nkhunda ankagulitsa pamtengo wa masekeli asiliva asanu.
26Tsiku lina mfumu ikuyenda pa makoma a mzinda, mai wina adamfuulira kuti, “Inu mbuyanga mfumu, thandizeni.”
27Apo mfumuyo idafunsa kuti, “Kodi Chauta akapanda kukuthandiza, nanga ine ndingazipeze kuti zokuthandizira? Kodi kwatsalako kanthu ngati ku malo opunthira tirigu kapena ku malo opondera mphesa?
28Nanga chakuvuta nchiyani?” Iyeyo adayankha kuti, “Tsiku lina mai uyu adandiwuza kuti, ‘Ipha mwana wako kuti tidye lero, wanga tidye maŵa.’
29Deut. 28.57; Mali. 4.10 Motero tidaphika mwana wangayo, ndipo tidadya. Tsono m'maŵa mwake ndidamuuza kuti, ‘Iphatu mwana wako uja kuti tidye.’ Koma iyeyu wabisa mwana wakeyo.”
30Mfumuyo itamva mau a maiwo idang'amba zovala zake. Pamenepo nkuti mfumuyo ikuyenda pa khoma. Ndipo anthu adangoona kuti mfumuyo yavala chiguduli m'kati mwa zovala zake.
31Tsono mfumu ija idati, “Mulungu andiphe, ndikapanda kudulitsa mutu wa Elisa mwana wa Safati lero.”
32Nthaŵiyo Elisa adaakhala pansi m'nyumba mwake, ndipo akuluakulu anali naye limodzi. Tsono mfumu ija idatuma mmodzi mwa atumiki ake kuti akatenge Elisa. Koma wamthengayo asanafike, Elisa adauza akuluakulu aja kuti, “Ha! Wopha anthu uja watuma munthu kuti adzandidule mutu. Akangofika wamthengayo, inu mutseke chitseko, ndipo muchigwiritse, asaloŵe. Kodi mgugu ukumveka pambuyo pakewo si wa mbuyake?”
33Elisayo akulankhulabe ndi akuluakuluwo, mfumu ija idafika, ndipo idati, “Mavuto ameneŵa watigwetsera ndi Chauta. Kodi ndingathe bwanji kudikira thandizo lochokera kwa Chauta?”
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.