1Pamene adzakufikirani madalitso ndi matemberero amene ndatchula aja, mudzaŵakumbukira muli pakati pa mitundu ina kumaiko kumene Chauta, Mulungu wanu, adakumwazirani.
2Tsono inuyo ndi zidzukulu zanu mudzabwerera kwa Chauta, ndipo mau ake amene ndikukupatsani leroŵa mudzaŵamvera ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.
3Pamenepo Chauta, Mulungu wanu, adzakukhazikaninso pabwino ndi kukuchitirani chifundo. Adzakusokolotsani kukuchotsani ku mitundu ina ya anthu, kumene adakumwaziraniko, ndipo adzakusandutsaninso olemera.
4Ngakhale mutamwazikira ku malekezero a dziko lapansi, Chauta, Mulungu wanu, adzakusonkhanitsani komweko nadzakutengani kuchokera kumeneko.
5Adzakuperekezani ku dziko limene makolo anu anali nalo kale, kuti mukakhazikikeko ndinu. Ndipo adzakupezetsani bwino ndi kukuchulukitsani kopambana m'mene adaaliri makolo anu.
6Chauta, Mulungu wanu, adzakupatsani inu ndi zidzukulu zanu mtima womvera, kotero kuti muzidzamkonda ndi mtima wanu wonse, ndi moyo wanu wonse. Motero mudzakhalabe ndi moyo m'dziko limenelo.
7Koma Chauta, Mulungu wanu, adzagwetsa matemberero onse aja pa adani anu amene adakuzunzani.
8Inuyo mudzamveranso ndi kumatsata malamulo amene ndikukupatsani leroŵa.
9Chauta adzakupezetsani bwino pa zochita zanu zonse. Mudzakhala ndi ana ambiri, zoŵeta zambiri, ndipo minda yanu idzakubalirani zokolola zambiri. Adzakondwera nanu kuti mwakhoza chotere, monga momwe adakondwera ndi makolo anu pamene anali okhoza.
10Komatu muzidzamvera Chauta, Mulungu wanu, ndi kusunga malamulo ndi malangizo ake onse amene ali m'buku lino la malamulo ake. Mutembenukire kwa Iye ndi mtima wanu wonse ndi moyo wanu wonse.
11Lamulo ndikukupatsani leroli si lovuta kulimvetsa ndipo si lapatali.
12Aro. 10.6-8 Silili kumwamba, kuti muzichita kudzifunsa kuti, “Kodi amene akwere kumwamba kukatitsitsira lamulo kuti tilimve, ndani?”
13Komanso silili pa tsidya la nyanja, kuti muthe kufunsa kuti, “Kodi amene aoloke nyanja kukatitengera lamulo kuti tilimve, ndani?”
14Muli nalo pompano. Mukulidziŵa, mumalitchula ndipo mungathe kulitsata.
15 Mphu. 15.16, 17 Ndikukupatsani mpata lero woti musankhe, kapena moyo ndi zabwino, kapena imfa ndi zoipa.
16Mukamamvera malamulo a Chauta, Mulungu wanu, ndi malangizo ake amene ndikukupatsani lero, mukamamkonda Chauta, Mulungu wanu ndi kutsata mau ake onse, pamenepo mudzakhala pabwino ndipo mudzakhala mtundu wa anthu ochuluka. Chauta, Mulungu wanu, adzakudalitsani m'dziko mukukakhalamolo.
17Koma mukapanda kumvera, mukamakana kumva, m'malo mwake nkumatengeka kuti mupembedze milungu ina,
18ndikuchenjezeranitu tsopano kuti mudzaonongeka. Dziko ili la patsidya pa Yordani limene mukupita kukakhalamolo, simudzakhalitsamo.
19Tsopano ndikukupatsani mpata woti musankhe, kapena moyo kapena imfa, madalitso a Mulungu kapena matemberero ake. Zonse zakumwamba ndi zapansi zikhale mboni za zimene ndakuuzani lerozi. Tsono sankhani moyo,
20Gen. 12.7; Gen. 26.3; Gen. 28.13 mukonde Chauta, Mulungu wanu, muzimvera mau ake ndi kukhala okhulupirika kwa Iye, kuti inu ndi zidzukulu zanu mudzakhalitsemo m'dziko limene adalonjeza kuti adzapatsa makolo anu, Abrahamu, Isaki ndi Yakobe.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.