1Titalaŵirana nawo, tidachoka kumeneko m'chombo, ndipo tidayenda molunjika kukafika ku Kosi. M'maŵa mwake tidakafika ku Rode, ndipo kuchokera kumeneko tidakafika ku Patara.
2Kumeneko tidapeza chombo chopita ku Fenisiya. Tsono tidaloŵamo nkunyamuka.
3Tidaona chilumba cha Kipro, koma tidachisiya ku dzanja lamanzere nkupita ku Siriya. Tidakafika ku Tiro, popeza kuti chombo chinkayenera kukatsitsa katundu kumeneko.
4Tidafunafuna ophunzira akumeneko, ndipo titaŵapeza, tidakhala nawo masiku asanu ndi aŵiri. Ndi chiwongolero cha Mzimu Woyera iwo aja adauza Paulo kuti asapite ku Yerusalemu.
5Koma pamene masiku athu aja adatha, tidachokako nkupitirira ulendo wathu. Onsewo, pamodzi ndi akazi ao ndi ana awo omwe, adatiperekeza mpaka kunja kwa mzinda. Tidagwada pa mchenga m'mbali mwa njanja nkupemphera.
6Ndipo titatsazikana, ife tidakaloŵa m'chombo, iwowo nkumabwerera kwao.
7Tidapitirira ulendo wathu wochokera ku Tiro mpaka tidakafika ku Ptolemaisi. Kumeneko tidacheza pang'ono ndi abale, nkukhala nawo tsiku limodzi.
8 ndipo tidakhala kunyumba kwakeko.
9Iyeyo anali ndi ana aakazi anai osakwatiwa, amene ankalalika uthenga wa Mulungu.
10 Akuluampingo onse anali kumeneko.
19Atalonjerana nawo, Paulo adaŵafotokozera mwatsatanetsatane zonse zimene Mulungu adaachita pakati pa anthu a mitundu ina kudzera mu utumiki wake.
20Pamene iwo adamva zimenezi, adayamika Mulungu. Ndipo adauza Paulo kuti, “Inu mbale wathu, mukuwona kuti pali Ayuda ambirimbiri amene asanduka okhulupirira. Onsewo ngokhulupirika kwambiri pa kutsata Malamulo a Mose.
21Anthu aŵauza za inu kuti Ayuda onse okhala ku maiko achilendo, inu mumaŵaphunzitsa kuti alekane nawo Malamulowo. Akutinso mumaŵaphunzitsa kuti asamaumbale ana ao kapena kusamala miyambo yachiyuda.
22Tsono pamenepa titani? Kumva adzamva ndithu kuti mwafika.
23 nkutsogolera zigaŵenga zikwi zinai kupita nazo ku chipululu?”
39Paulo adayankha kuti, “Inetu ndine Myuda, nzika ya ku Tariso, mzinda wotchuka wa ku Silisiya. Ndikukupemphani tsono, mundilole kuti ndilankhule nawo anthuŵa.”
40Adamloladi, ndipo Paulo adaima pamakwerero paja, naweyula dzanja kuti anthuwo akhale chete. Pamene onse adakhala chete, Paulo adayamba kulankhula nawo pa Chiyuda. Adati,
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.