Miy. 18 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Munthu wodzipatula mwa anzake

amangotsata zomkomera iyeyo,

amangofuna kutsutsana ndi zimene

onse akudziŵa kuti ndi zoona.

2Chitsiru sichisamalako za kumvetsa zinthu.

Koma chimangolankhula za maganizo ake okha.

3Kuipa mtima kukaoneka, pamabweranso manyozo,

kunyozeka kumaitana manyazi.

4Mau a munthu angathe kukhala kasupe wa nzeru,

ozama ngati nyanja yamchere yaikulu,

omweka ngati a mu mtsinje wothamanga.

5Si kwabwino pa mlandu kukondera munthu woipa,

kapena kupondereza munthu wosalakwa.

6Mau a chitsiru amautsa mkangano,

ndipo pakamwa pake pamaitana mkwapulo.

7Pakamwa pa chitsiru ndipo pamabweretsa

chiwonongeko chake.

Mau ake ali ngati msampha wodzikolera mwiniwakeyo.

8Mau a kazitape ali ngati chakudya chokoma,

anthu amaŵameza onse mokondwa.

9Wogwira ntchito yake mwaulesi,

ali pachibale ndi munthu woononga zinthu.

10Chauta ali ngati nsanja yolimba,

munthu wokhulupirira amathaŵiramo napulumuka.

11Chuma cha munthu wolemera chili

ngati mzinda wake wolimba, chili ngati linga lalitali

limene amayesa ndi lomutchinjiriza.

12Chiwonongeko chisanafike, mtima wa munthu umadzikuza,

koma ulemu umatsatira kudzichepetsa.

13 Mphu. 11.8 Ukayankha usanamve nkhani yonse,

umaoneka wopusa ndipo umachita manyazi.

14Mtima wa munthu umatha kupirira matenda,

koma munthu akataya mtima, ndani angathe kumlimbitsanso?

15Munthu wochenjera amafuna kuphunzirabe zambiri,

amafunitsitsa kudziŵa bwino zinthu.

16Mphatso ya munthu imakhala ngati konza kapansi,

imatha kumfikitsa pamaso pa akuluakulu.

17Amene amayamba kufotokoza mlandu wake

amaoneka ngati wokhoza ndiye,

mpaka mnzake atabwera nadzamufunsitsa bwino.

18Maere amathetsa mikangano.

Amalekanitsa okangana amphamvu.

19Mnzako ukamthandiza amakhala ngati mzinda wolimba,

koma kukangana naye kumakutsekera thandizo lililonse.

20Munthu amapeza bwino kapena ai,

malinga ndi zolankhula zake,

amalandira zotsatira za mau a pakamwa pake.

21Zimene umanena zingathe kukuphetsa

kapena kukukhalitsa moyo,

munthu wolankhulalankhula adzapeza bwino kapena tsoka.

22 Mphu. 26.1-4 Wopeza mkazi, wapeza chinthu chabwino,

Chauta wamukomera mtima.

23Anthu osauka amapemba,

koma anthu olemera amayankha mwaukali.

24Pali abwenzi ena amene chibwenzi chao

nchachiphamaso chabe,

koma pali ena amene amakukangamira koposa mbale yemwe.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help