1Ambuye, ndinu Atate,
ndinu Mwini wa moyo wanga,
musandisiye kuti nditsate mau aliwonse
a m'kamwa mwanga.
Musalole kuti andilakwitse.
2Ndani adzandithandiza
kuyendetsa maganizo anga mosamala,
ndani adzandithandiza
kuika nzeru ndi mwambo mu mtima mwanga,
kuti zisandilekerere m'zolakwa zanga,
ndipo zisalephere kundidzudzula
chifukwa cha machimo anga?
3Tsono zolakwa zanga sizidzachuluka,
ndipo machimo anga sadzakula.
Choncho sindidzagwa pansi
pamaso pa adani anga,
ndipo sadzandiseka.
4Ambuye, ndinu Atate,
ndinu Mulungu wa moyo wanga,
musalole kuti ndikhale wonyada,
5Chotsereni zilakolako zoipa.
6Ndisakhale wadyera ndi wokonda zadama,
musalole kuti ndivomere zilakolako
zochititsa manyazi.
Za kulumbira7Ana anga, mverani malangizo anga
pa za kusunga pakamwa.
Wosunga malangizo ameneŵa sadzapalamula.
8Munthu wochimwa amakodwa m'mau ake omwe.
Anthu osinjirira ndi amwano amagwa ndi mau ao.
9 Mt. 5.34; Yak. 5.12 Pakamwa pako pasazoloŵere kulumbira
pasamanzemanze kutchula dzina la Woyera uja.
10Kapolo wokwapulidwa nthaŵi zonse salephera
kukhala ndi mikwingwirima,
chimodzimodzi munthu wokonda kulumbira ndi kutchula
dzina la Mulungu ameneyo sangalephere kuchimwa.
11Munthu wokonda kulumbira amadzaza ndi machimo,
ndipo mkwapulo sudzachoka m'nyumba mwake.
Akalephera kuchita zimene adalumbira,
akhalabe ndi tchimo.
Akachita kunyozera zimene adalumbirazo,
achimwa moŵirikiza.
Ngati adalumbira monyenga sadzamkhululukira,
ndipo m'nyumba mwake mavuto adzachita kudzaza.
Za nkhani zonyansa12Pali kulankhula kwina kumene kuli ngati imfa.
Zoterezi zisamapezeka pakati pa zidzukulu za Yakobe!
Paja zimenezi zili kutali ndi anthu okonda Mulungu,
iwo sakondwera m'machimo.
13Usazoloŵere kumakamba nkhani zoipa ndi zonyansa,
chifukwa mau ake ali ndi uchimo.
14Ukakhala pakati pa anthu omveka
uzikumbukira bambo wako ndi mai wako,
kuwopa kuti ungadziiŵale pamaso pa akuluakuluwo,
kuyamba mkhalidwe wauchitsiru.
Pambuyo pake nkumaganiza kuti
kukadakhala kwabwino udakapanda kubadwa,
kenaka nkumatemberera tsiku udabadwa.
15Munthu wozoloŵera kulankhula mau ochititsa manyazi
sadzathanso kulankhula zabwino mpaka kufa kwake.
Za machimo a dama16Pali mitundu iŵiri ya anthu
ochulukitsa machimo,
palinso mtundu wachitatu wa anthu
odziitanira chilango.
Chilakolako choipa chili ngati moto woyaka
umene suzimika mpaka utatentha zonse.
Munthu wochita chigololo ndi wachibale wake
sadzaleka mpaka moto utampsereza.
17Kwa munthu wadama akazi onse ngokoma,
ndipo sadzalekeza dama lake mpaka kufa.
18Munthu wochimwira ukwati wake amati,
“Ndani angandiwone?
Ponseponse pali mdima, ndipo zipupa zikundibisa.
Palibe wondipenya, ndivutikirenji?
Ngakhale Mulungu Wopambanazonse sadzasamalako
za machimo anga.”
19Munthu ameneyu amangoopa
maso a anthu anzake.
Amaiŵala kuti maso a Ambuye
ndi oŵala kwambiri
kupambana m'mene limaŵalira dzuŵa.
Amapenya zonse zimene anthu akuchita,
amapenya ngakhale zinthu zobisika.
20Dziko lisanalengedwe, Ambuye ankalidziŵa,
atatsiriza kulilenga, akulidziŵabe.
21Munthu wochimwa ameneyo adzalangidwa poyera mu mzinda,
atamugwira pamene iye sakuyembekeza konse.
Za mkazi wachigololo22Ndi m'mene alirinso mkazi wosakhulupirika kwa
mwamuna wake,
amatha kubereka mwana woloŵa chuma ndi mwamuna wina.
23Choyamba, waswa lamulo la Mulungu.
Kachiŵiri, wachimwira mwamuna wake.
Kachitatu, wadzisandutsa wadama pochita chigololo,
ndipo wabereka ana am'thengo.
24Adzamzenga mlandu pamaso pa gulu,
ndipo chilango chidzagwera ana ake.
25Ana ake sadzazika mizu
ndipo nthambi zake sizidzabereka zipatso.
26Adzamkumbukira momtemberera,
ndipo manyazi sadzamchoka.
27Motero onse am'tsogolo adzadziŵa
kuti palibe kanthu kena kabwino kupambana kuwopa Ambuye.
Palibedi chabwino china choposa kumvera Malamulo a Mulungu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.