Yer. 52 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za kuwonongeka kwa Yerusalemu(2 Maf. 24.18—25.7)

1Zedekiya anali wa zaka 21 pamene adaloŵa ufumu, ndipo adalamulira zaka khumi ndi chimodzi ku Yerusalemu. Mai wake anali Hamutala, mwana wa Yeremiya wa ku Libina.

2Zedekiyayo adachita zoipa pamaso pa Chauta potsata zonse zimene ankachita Yehoyakimu.

3Chifukwa cha zonse zimene zidachitika ku Yerusalemu ndi ku Yudazi, Chauta adakwiya kwambiri, mpaka kuŵachotsa anthuwo pamaso pake.

Tsono Zedekiya adapandukira mfumu ya ku Babiloni.

4Ezek. 24.2 Ndiye pa chaka chachisanu ndi chinai cha ufumu wa Zedekiyayo, mwezi wakhumi, tsiku lakhumi la mwezi, Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni adabwera ndi ankhondo ake onse kudzathira nkhondo mzinda wa Yerusalemu. Adauzinga ndi zithando zankhondo ponseponse.

5Motero mzindawo udaazingidwa ndi zithandozo mpaka chaka cha 11 cha ufumu wa Zedekiya.

6Tsono pa tsiku lachisanu ndi chinai, pa mwezi wachinai wa chaka chimenecho, pamene njala inali itakula kwambiri mumzindamo kotero kuti anthu analibiretu chakudya m'dzikomo,

7Ezek. 33.21malinga a mzindawo adabooledwa. Pamenepo ankhondo onse adathaŵa mumzindamo usiku, kutulukira pa chipata cha pakati pa makoma aŵiri, pafupi ndi munda wa mfumu, ngakhale kuti Ababiloni anali atauzinga mzindawo. Ndipo adathaŵira ku Araba.

8Koma gulu lankhondo la Ababiloni lidamlondola mfumu Zedekiya nkukamgwirira m'zigwa za ku Yeriko. Ankhondo ake adabalalika namsiya.

9Apo a ku Babiloni aja atamgwira Zedekiya, adapita naye kwa Nebukadinezara, ku Ribula m'dziko la Hamati. Komweko Nebukadinezarayo adagamula mlandu wa Zedekiya uja.

10Pompo adapha ana a Zedekiya iyeyo akupenya. Adaphanso akalonga onse a ku Yuda ku Ribula komweko.

11Ezek. 12.13 Ndipo adamkolowola maso Zedekiyayo, nammanga ndi maunyolo nkupita naye ku Babiloni. Kumeneko adamuponya m'ndende kuti akhalemo moyo wake wonse.

Za kuwonongedwa kwa Nyumba ya Mulungu(2 Maf. 25.8-17)

12Mwezi wachisanu, pa tsiku lakhumi la mwezi, chaka cha 19 cha ufumu wa Nebukadinezara mfumu ya ku Babiloni, Nebuzaradani, mkulu wa asilikali oteteza mfumu, mmodzi wa aphungu ake, adadza ku Yerusalemu.

131Maf. 9.8 Ndipo adatentha Nyumba ya Chauta, nyumba ya mfumu, ndi nyumba zina zonse za ku Yerusalemu, nyumba yaikulu iliyonse adaitentha.

14Tsono gulu lonse lankhondo la ku Babiloni limene linali ndi mkulu wa asilikali uja, lidagumula malinga onse ozinga Yerusalemu.

15Anthu ena onse amene adaatsala mumzindamo, ndi ena amene adaadzipereka kale kwa mfumu ya ku Babiloni, pamodzi ndi anthu aluso otsala, Nebuzaradani mkulu wa asilikali uja adaŵatenga kupita nawo ku Babiloni.

16Koma Nebuzaradani adasiyako anthu ena osauka kwambiri am'dzikomo, kuti azilima minda ya mphesa ndi minda ina.

17 1Maf. 7.15-47 Ankhondo a ku Babiloni adaphwanya nsanamira zamkuŵa za m'Nyumba ya Chauta, ndiponso maphaka ndi chimbiya chamkuŵa, ndipo adatenga mkuŵa wonsewo, napita nawo ku Babiloni.

18Ankhondowo adachotsanso mbiya, zoolera phulusa, zozimira nyale, mbale zofukizira lubani, zikho kudzanso ziŵiya zonse zamkuŵa zimene ankagwiritsira ntchito ku Nyumba ya Chauta.

19Mkulu wa Asilikali uja adatenga mabeseni, ziwaya zosonkhapo moto, mbale zowazira madzi, zoikapo nyale, zipande zofukizira lubani ndi zikho, ndi zina zonse zagolide ndi zasiliva.

20Nsanamira ziŵiri zija, chimbiya, maphaka ndiponso ng'ombe zamphongo khumi ndi ziŵiri zimene zinkachirikiza chimbiyacho, zimene mfumu Solomoni adaapangira Nyumba ya Chauta kulemera kwake kwa mkuŵa wa zonsezo kunali kosaŵerengeka.

21Nsanamira imodzi kutalika kwake inali mamita asanu ndi atatu, kuzungulira kwake inali mamita asanu ndi theka. Inali ndi chiboo m'kati, ndipo kuchindikira kwake inali zala zinai.

22Inali ndi mutu wamkuŵa, kutalika kwake mamita aŵiri. Pozungulira mutuwo panali ukonde ndi makangaza, zonsezo zamkuŵa. Nsanamira inayo inalinso ndi makangaza ndipo inkafanana ndi inzakeyo pa zonse.

23Makangaza 96 anali pambali, koma onse pamodzi analipo zana limodzi, kuzungulira ukonde wonsewo.

Anthu a ku Yuda atengedwa kupita ku Babiloni(2 Maf. 25.18-21, 27-30)

24Tsono Nebuzaradani mkulu wa asilikali uja, adagwira Seraya mkulu wa ansembe ndi Zefaniya, wachiŵiri kwa mkulu wa ansembe, ndi alonda atatu apachipata.

25Mumzindamo adagwiramo mkulu amene ankalamulira ankhondo, ndiponso anthu asanu ndi aŵiri amene anali aphungu a mfumu mumzindamo. Adagwiranso mlembi wa mtsogoleri wa ankhondo, amene ankalemba anthu am'dzikomo, ndiponso akuluakulu ena 60, amene anali mumzindamo.

26Nebuzaradani, mkulu wa asilikali uja, adaŵatenga onsewo napita nawo kwa mfumu ya ku Babiloni ku Ribula.

27Mfumu ya ku Babiloni idalamula kuti onsewo aphedwe ku Ribula m'dziko la Hamati.

Motero anthu a ku Yuda adatengedwa ukapolo kuŵachotsa kutali ndi dziko lao.

28Nachi chiŵerengero cha anthu amene Nebukadinezara adaŵatenga ukapolo. Pa chaka chachisanu ndi chiŵiri cha ufumu wake, adatengedwa Ayuda 3,023.

29Pa chaka cha 18 cha ufumu wake, Nebukadinezara adatenga ukapolo anthu 832 kuchokera ku Yerusalemu.

30Pa chaka cha 23 cha ufumu wa Nebukadinezara, Nebuzaradani mtsogoleri wa alonda oteteza mfumu uja adatenga ukapolo Ayuda 745. Onse pamodzi otengedwa ukapolo adakwanira 4,600.

31Pa chaka cha 37 cha ukapolo wa Yehoyakimu, mfumu ya ku Yuda, tsiku la 25 la mwezi wa 12, Evili-Merodaki, mfumu ya ku Babiloni adangoti ataloŵa ufumu, adakomera mtima Yehoyakimu mfumu ya ku Yuda, namtulutsa m'ndende.

32Adalankhula naye mwachifundo, nampatsa malo aulemu kuposa mafumu ena amene anali naye ku Babiloni.

33Motero Yehoyakimu adavula zovala zake zakundende, ndipo tsiku ndi tsiku ankadya ndi mfumu pa moyo wake wonse.

34Kunena za phoso, mfumu ya ku Babiloni inkampatsa Yehoyakimu phoso lake tsiku ndi tsiku mpaka kufa kwake.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help