1Zidzukulu za Aroni ndi izi. Ana a Aroni naŵa: Nadabu, Abihu, Eleazara ndi Itamara.
2Lev. 10.1, 2 Koma Nadabu ndi Abihu adafa bambo wao akali moyo, ndipo analibe ana. Motero Eleazara ndi Itamara adaloŵa unsembe.
3Zidzukulu za Aroni mfumu Davide adazigaŵira ntchito molongosoka bwino, pothandizidwa ndi Zadoki, mmodzi mwa zidzukulu za Eleazara, ndiponso Ahimeleki, mmodzi mwa zidzukulu za Itamara.
4Popeza kuti pakati pa zidzukulu za Eleazara padapezeka atsogoleri ambiri kupambana pakati pa zidzukulu za Itamara, Davide adasankhula atsogoleri 16 pakati pa zidzukulu za Eleazara, ndiponso asanu ndi atatu pakati pa zidzukulu za Itamara.
5Adaŵasankhula pochita maere mosakondera, poti panali atumiki a ku Nyumba ya Chauta ndi atsogoleri achipembedzo pakati pa zidzukulu za Eleazara ndiponso pakati pa zidzukulu za Itamara.
6Magulu aŵiri a zidzukuluzi adachita maerewo motsatana, ndipo mlembi Semaya, mwana wa Netanele, amene anali Mlevi, adalemba maina ao. Mboni zake zinali izi: mfumu, nduna, wansembe Zadoki, Abimeleki mwana wa Abiyatara, ndiponso atsogoleri a mabanja a ansembe ndi a Alevi.
7Maere oyamba adagwera Yehoyaribu, achiŵiri adagwera Yedaya,
8achitatu adagwera Harimu, achinai adagwera Seorimu,
9achisanu adagwera Malikiya, achisanu ndi chimodzi adagwera Miyamini,
10achisanu ndi chiŵiri adagwera Hakozi, achisanu ndi chitatu adagwera Abiya,
11achisanu ndi chinai adagwera Yesuwa, achikhumi adagwera Sekaniya,
12a 11 adagwera Eliyasibu, a 12 adagwera Yakimu,
13a 13 adagwera Hupa, a 14 adagwera Yesebeabu,
14a 15 adagwera Biliga, a 16 adagwera Imeri,
15a 17 adagwera Heziri, a 18 adagwera Hapizeze,
16a 19 adagwera Petahiya, a 20 adagwera Yehezikele,
17a 21 adagwera Yakini, a 22 adagwera Gamuli,
18a 23 adagwera Delaya, a 24 adagwera Maaziya.
19Ntchito yao ya anthu ameneŵa inali yotumikira m'Nyumba ya Mulungu potsata mwambo umene adaukhazikitsa Aroni kholo lao, monga momwe Chauta Mulungu wa Aisraele adaamlamulira.
Maina a Alevi20Atsogoleri ena a mabanja a Levi naŵa: Yedeiya, mdzukulu wa Subaele, amene anali mdzukulu wa Amuramu.
21Isiya, mdzukulu wa Rehabiya,
22Yahati, mdzukulu wa Selomoti, amene anali mdzukulu wa Izihara.
23Ana a Hebroni naŵa: Yeriya mtsogoleri, wachiŵiri Amariya, wachitatu Yahaziele, wachinai Yekameani.
24Samiri anali mdzukulu wa Mika, kholo lao linali Uziyele.
25Mbale wake wa Mika anali Isiya. Zekariya anali mdzukulu wa Uziyele, kholo lao linali Isiya.
26Zidzukulu za Merari nazi: Mali, Musi ndi Yaziya.
27Adzukulu a Merari, kuchokera mwa Yaziya mwana wake, naŵa: Sohamu, Zakuri ndi Ibiri.
28Ana a Mali anali aŵa: Eleazara, amene analibe ana, ndiponso Kisi,
29amene mwana wake anali Yerameele.
30Ana a Musi anali Mali, Edere ndi Yerimoti.
Ameneŵa ndiwo amene anali zidzukulu za Levi potsata mabanja a makolo ao.
31Mabanja ameneŵanso kuti adziŵe ntchito zao, adachita maere monga abale ao, zidzukulu za Aaroni, akuluakulu ndi ang'onoang'ono omwe. Ochita umboni anali mfumu Davide, Zadoki, Ahimeleki, ndiponso atsogoleri a mabanja a ansembe ndi a Alevi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.