Eks. 18 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Yetero achezera Mose

1Yetero, wansembe wa ku Midiyani, mpongozi wake wa Mose, adamva zonse zija zimene Mulungu adachitira Mose ndiponso anthu ake Aisraele. Adamvanso za m'mene Chauta adaŵatulutsira ku Ejipito.

2 Eks. 2.21, 22 Motero adabwera ndi Zipora, mkazi wa Mose, amene Moseyo anali atamsiya.

3Ntc. 7.29 Yetero adabweranso ndi ana aamuna aŵiri aja a Zipora. Mwana woyamba Mose adaamutcha Geresomo (chifukwa adati, “Ndakhala mlendo m'dziko lachilendo.”)

4Mwana wake wachiŵiri Mose adaamutcha Eliyezere, (chifukwa adati, “Mulungu wa atate anga ndiye thandizo langa, ndipo adandipulumutsa ku lupanga la Farao.”)

5Yeteroyo adabwera ndi mkazi wa Mose ndi ana ake aamuna kuchipululu kuja, ku malo amene Mose adamangako mahema, pa phiri la Mulungu.

6Munthu wina adakauza Mose kuti, “Mpongozi wanu Yetero akubwera ndi mkazi wanu ndi ana anu aŵiri aamuna.”

7Tsono Mose adamchingamira nakakumana naye, ndipo adamgwadira ndi kumumpsompsona. Atalonjerana ndi kufunsana za moyo, adakaloŵa mu hema.

8Ndipo Mose adamufotokozera zonse zimene Chauta adamchita Farao ndi Aejipito chifukwa cha Aisraelewo. Adamsimbiranso za mavuto omwe adaakumana nawo pa njira, ndi zonse zimene Chauta adaachita poŵapulumutsa.

9Yetero adakondwa kwambiri ndi ntchito zabwino zimene Chauta adaachitira Aisraele pakuŵapulumutsa kwa Aejipito.

10Tsono adati, “Mtamandeni Chauta amene adakupulumutsani kwa Aejipito ndi kwa Farao. Mtamandeni Chauta amene adapulumutsa anthu ake ku ukapolo wa Aejipito.

11Tsopano ndikudziŵa kuti Chauta ndi wamkulu kupambana milungu ina yonse, chifukwa adapulumutsa Aisraele kwa Aejipito, pamene Aejipitowo ankaŵanyoza.”

12Pamenepo Yetero adapereka kwa Mulungu nsembe yopsereza ndi nsembe zinanso. Kenaka Aroni ndi atsogoleri a Aisraele adabwera pamaso pa Mulungu kudzadya pamodzi ndi Yetero mpongozi wa Mose.

Mose aika aweruzi(Deut. 1.9-18)

13M'maŵa mwake Mose adayamba kuweruza milandu ya anthu. Ndipo anthuwo ankabwera ndi milandu yao kwa Moseyo kuyambira m'maŵa mpaka usiku.

14Yetero mpongozi wake wa Mose ataona zonse zimene Moseyo ankachita, adafunsa kuti, “Kodi zonse zimene mukuchitira anthuzi nzotani? Chifukwa chiyani mukukhala nokha pano, pamene anthu akubwerabe kwa inu kuyambira m'maŵa mpaka usiku?”

15Mose adayankha kuti, “Ndiyenera kuchita zimenezi chifukwa choti anthu amabwera kwa ine, kuti amve zimene Mulungu afuna.

16Anthu aŵiri akamakangana, amabwera kwa ine, ndipo ndimaŵaweruza, ndi kuwona kuti wakhoza ndani. Ndipo ndimaŵauza mau a Mulungu ndi malamulo ake.”

17Apo Yetero mpongozi wa Moseyo adati, “Simukuchita bwino ai.

18Inu mudzafooka msanga, pamodzi ndi anthu muli nawoŵa. Ntchito imeneyi njaikulu kuposa mphamvu zanu, ndipo simungaithe nokha.

19Tandimverani tsono, ndikulangizeni, ndipo Mulungu adzakhala nanu. Inu muyenera kuima m'malo mwa anthu pamaso pa Mulungu ndi kubwera ndi makangano ao kwa Iye.

20Muyenera kuŵaphunzitsa mau ndi malamulo a Mulungu, ndi kuŵafotokozera m'mene azikhalira ndi m'mene azichitira.

21Komanso sankhulani amuna anzeru, ndipo muŵaike kuti akhale atsogoleri a anthu, motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 100, ena a anthu 50, ena a anthu khumi chabe. Ayenera kukhala anthu oopa Mulungu, okhulupirika, ndiponso osakopeka ndi ziphuphu.

22Iwo ndiwo aziweruza anthu nthaŵi zonse. Azibwera ndi milandu yovuta yokha kwa inu, koma timilandu ting'onoting'ono aziweruza okha. Adzakuchepetserani ntchito iwowo pakusenza katunduyo pamodzi nanu.

23Mukachita zimenezi monga Mulungu akulamulira, simudzafooka, ndipo anthu onseŵa adzatha kumabwerera kwao, zao zonse zitakonzeka.”

24Mose adamvera zonse zimene adanena Yetero zija.

25Adasankha anthu anzeru pakati pa Aisraelewo ndi kuŵaika kuti akhale atsogoleri a anthu motere: atsogoleri a anthu 1,000, ena a anthu 100, ena a anthu 50, ena a anthu khumi chabe,

26ndipo iwowo ankaweruza anthu nthaŵi zonse. Milandu yovuta yokha ankabwera nayo kwa Mose, koma timilandu ting'onoting'ono ankangomaliza okha.

27Tsono Yeteroyo atalaŵirana naye Mose, adabwerera kwao.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help