Owe. 6 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za Gideoni.

1Aisraele adachitanso zinthu zoipira Chauta, ndipo Chauta adaŵapereka m'manja mwa Amidiyani zaka zisanu ndi ziŵiri.

2Amidiyani anali amphamvu ndi oopsa kupambana Aisraele. Nchifukwa chake Aisraele ankakumba malo obisalamo m'mapiri ndiponso m'mapanga, namanganso malinga ao.

3Aisraele ankati akabzala mbeu, Amidiyani ndi Aamaleke pamodzi ndi anthu akuvuma, ankabwera kudzaŵathira nkhondo.

4Ankamanga zithando zao moyang'anana ndi Aisraele, ndi kuwononga zokolola zao zonse mpaka ku Gaza, osaŵasiyirako Aisraelewo chakudya chilichonse, nkhosa, ng'ombe kapenanso bulu.

5Iwo Amidiyani ankabwera ndi ng'ombe zao zomwe pamodzi ndi mahema ao. Ankabwera ambiri ngati dzombe. Kunali kosatheka kuŵaŵerenga anthuwo ndi ngamira zao. Ankaononga dzikolo pamene ankabwera.

6Motero Amidiyani adalulutsa dziko la Israele kwambiri. Ndipo Aisraele adalira kwa Chauta kuti aŵathandize.

7Pamene Aisraele adalira kwa Chauta chifukwa cha Amidiyaniwo,

8Chautayo adaŵatumizira mneneri. Ndipo iye adaŵauza kuti, “Zimene Chauta, Mulungu wa Israele, wanena ndi izi, ‘Ndine amene ndidakutsogolerani kuchokera ku Ejipito, nkukutulutsani m'dziko laukapolo.

9Ndidakupulumutsani kwa Aejipito ndiponso kwa onse amene ankakuzunzani. Ndidakupirikitsirani adani anu inu mulikufika, ndi kukupatsani dziko lao.

10Ndidakuuzani kuti Ine ndine Chauta, Mulungu wanu, musapembedze milungu ya Aamori amene mukukhala m'dziko lao, koma inu simudasamale mau anga.’ ”

11Tsiku lina mngelo wa Chauta adabwera ku Ofura ndi kukhala pansi patsinde pa mtengo wa thundu umene unali wa Yoasi Mwabiyezere. Nthaŵiyo nkuti Gideoni, mwana wake, akupuntha tirigu, atabisala m'nyumba yofinyira mphesa, kuti Amidiyani asamuwone tiriguyo.

12Apo mngelo wa Chauta uja adamuwonekera namuuza kuti, “Chauta ali nawe, iwe munthu wamphamvu ndi wolimba mtima.”

13Gideoni adauza mngeloyo kuti, “Pepani mbuyanga, ngati Chauta ali nafe, chifukwa chiyani tsono zonsezi zatigwera? Nanga zili kuti ntchito zake zonse zodabwitsa zimene makolo athu ankatisimbira zakuti ati Chauta adatitulutsa ku dziko la Ejipito? Koma tsopano watitaya, ndipo watipereka kwa Amidiyani.”

14Chauta adamlamula kuti, “Pita ndi mphamvu zakozi, ukapulumutse Aisraele kwa Amidiyani. Nanga kodi sindine amene ndikukutuma?”

15Apo Gideoni adayankha kuti, “Inu Chauta, ndapota nanu, kodi ndingathe bwanji kupulumutsa Aisraele? Onani, mbumba yanga ndiye yofooka kwambiri m'fuko la Manase, ndipo m'banja mwa bambo wanga, wamng'ono koposa ndine.”

16Chauta adamuuza kuti, “Koma Ine ndidzakhala nawe, ndipo udzaŵagonjetsa Amidiyani onse ngati munthu mmodzi.”

17Tsono Gideoni adati, “Ngati tsopano mwandikomera mtima, onetseni chizindikiro chosonyeza kuti ndinudi Chauta amene mukulankhula nane.

18Musachoke pano, ndapota nanu, mpaka nditabwerera kwa inu kudzakutulirani chopereka cha chakudya.” Apo Chauta adati, “Chabwino, ndikudikira mpaka utabwerera.”

19Tsono Gideoni adakaloŵa m'nyumba mwake, nakakonza mwanawambuzi, naphika makeke osatupitsa a ufa wa makilogramu khumi. Nyamayo adaiika m'dengu ndipo msuzi wake adauthira mu mphika, nabwera nazo zonsezo kudzazipereka kwa mngelo uja patsinde pa mtengo wa thundu paja.

20Mngelo wa Mulunguyo adamuuza kuti, “Tenga nyamayi pamodzi ndi makekeŵa, uziike pathanthwepo, ndi kuthira msuzi pamwamba pake.” Gideoni adachitadi zimenezo.

21Tsono mngelo wa Chauta adatenga ndodo m'manja mwake nakhudza nayo nyama ija ndi makeke aja. Pompo padabuka moto pathanthwepo ndi kupsereza nyamayo pamodzi ndi makeke aja. Basi mngelo wa Chauta adazimirira osaonekanso.

22Apo Gideoni adazindikira kuti analidi mngelo wa Chauta, ndipo adati, “Kalanga ine, Chauta Wamphamvuzonse! Ndaona mngelo wa Chauta ndi maso.”

23Koma Chauta adamuuza kuti, “Mtendere ukhale nawe. Usaope, suufa,”

24Tsono Gideoni adamangira Chauta guwa pa malo omwewo ndipo adalitcha dzina loti “Chauta ndiye mtendere.” Guwalo lili ku Ofura, mzinda wa Aabiyezere, mpaka lero lino.

25Usiku umenewo Chauta adauza Gideoni kuti, “Utenge ng'ombe yamphongo ya bambo wako, ng'ombe ina yachiŵiri, ya zaka zisanu ndi ziŵiri, ndipo ugwetse guwa la Baala limene bambo wako ali nalo, ndi kugwetsanso fano la Asera limene lili pambali pake.

26Kenaka pamwamba pa linga pano umange ndi miyala yoyala bwino guwa la Chauta, Mulungu wako. Tsono utenge ng'ombe yamphongo yachiŵiri ija ndi kuipereka kuti ikhale nsembe yopsereza, pogwiritsa ntchito mtengo wa fano la Asera limene udule ngati nkhunilo.”

27Choncho Gideoni adatenga anthu khumi mwa atumiki ake, ndipo adachitadi monga momwe Chauta adaamuuzira. Koma popeza kuti ankaopa kwambiri a m'banja la bambo wake ndiponso anthu am'mudzimo, sadachite zimenezo masana, adachita usiku.

28Pamene anthu am'mudzimo adadzuka m'mamaŵa, adangoona guwa la Baala litagwetsedwa, fano la Asera limene linali pambali pake litadulidwa, ndipo ng'ombe yamphongo yachiŵiri ija itaperekedwa nsembe pa guwa adaamangalo.

29Ndiye adayamba kufunsana kuti, “Wachita zimenezi ndani?” Atafufuza ndi kufunsafunsa, adati, “Gideoni, mwana wa Yoasi, ndiye amene wachita zimenezi.”

30Pomwepo anthu am'mudzimo adauza Yoasi kuti, “Mutulutse mwana wako. Ayenera kufa popeza kuti wagwetsa guwa la Baala, ndipo wadula fano la Asera limene linali pambali pake pa guwalo.”

31Koma onse amene adamuukirawo, Yoasi adaŵauza kuti, “Kodi inu ndinu amene mukuti mummenyere nkhondo Baala? Kodi ndinu amene mukuti mumtchinjirize? Aliyense amene amenyere Baala nkhondo, aphedwa maŵa m'maŵa. Ngati iye ndi mulungudi, adzimenyere nkhondo yekha, popeza kuti guwa lake lagwetsedwa.”

32Nchifukwa chake pa tsiku limenelo Gideoni adatchedwa Yerubaala, ndiye kuti, “Baala alimbane naye,” poti adaagwetsa guwa lake.

33Tsono Amidiyani ndi Aamaleke onse, pamodzi ndi anthu onse akuvuma, adasonkhana, ndipo ataoloka Yordani, adakamanga zithando zankhondo m'chigwa cha Yezireele.

34Koma Mzimu wa Chauta udaloŵa mwa Gideoni. Choncho Gideoniyo adaimba lipenga, ndipo Aabiyezere aja adaitanidwa kuti amtsate.

35Adatuma amithenga m'dziko lonse la Manase, nawonso Amanasewo adaitanidwa kuti amtsate. Adatumanso amithenga kwa Aasere, Azebuloni ndiponso Anafutali. Onsewo adapita kukaŵachingamira.

36Gideoni adalankhula ndi Mulungu nati, “Ngati mukuti mupulumutse Aisraele ndi dzanja langa, monga momwe mwaneneramu,

37chabwino, tsono ine ndikuyala ubweya wankhosa pa malo opunthira tirigu. Mame akangogwa pa ubweya wankhosa pokhapo, koma panthaka nkukhala pouma, apo ndidziŵa kuti Inu mudzapulumutsadi Aisraele kudzera mwa ine, monga momwe mudanenera.”

38Ndipo zidachitikadi choncho. Pamene adadzuka m'mamaŵa ndi kuufinya ubweya uja, adafinya madzi odzaza mkhate.

39Tsono Gideoni adalankhulanso ndi Mulungu nati, “Musandipsere mtima, mundilole ndilankhulenso kamodzi kokhaka. Ndapota nanu, mulole kuti paubweya pokhapa pakhale pouma koma panthaka ponsepa pagwe mame.”

40Mulungu adachitadi momwemo usiku umenewo, mwakuti paubweya pokha panali pouma, koma panthaka ponse padagwa mame.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help