1Inu anthu a mitundu yonse,
bwerani pafupi kuti mumve,
inu anthu onse tcherani makutu!
Limvetsere dziko pamodzi ndi zonse zokhalamo,
limvetsere dziko lapansi
pamodzi ndi zonse zofuma m'menemo.
2Pakuti Chauta waŵakwiyira anthu a mitundu yonse,
waŵapsera mtima magulu ao onse ankhondo,
watsimikiza kuti adzaonongedwa,
waŵapereka kuti aphedwe.
3Mitembo ya anthu ao ophedwa adzangoitaya kunja,
nimaola ndi kumanunkha,
ndipo mapiri adzafiira ndi magazi.
4 Mt. 24.29; Mk. 13.25; Lk. 21.26; Chiv. 6.13, 14 Dzuŵa, mwezi ndi nyenyezi zidzanyenyeka,
ndipo mlengalenga udzakulungika
monga chimachitira chikopa.
Nyenyezi zonse zidzayoyoka
monga amachitira masamba a mpesa kapena a mkuyu.
5 Yes. 63.1-6; Yer. 49.7-22; Ezek. 25.12-14; 35.1-15; Amo. 1.11, 12; Oba. 1.1-14; Mal. 1.2-5 Chauta akuti,
“Lupanga langa lakhutiratu kumwamba.
Si ili likutsika kudzalanga Aedomu,
anthu amene ndatsimikiza kuti ndiŵaononga.”
6Lupanga la Chauta lakhuta magazi,
ndipo lakutidwa ndi mafuta.
Magazi ake a anaankhosa ndi a mbuzi,
ndipo mafuta ake a ku impso za nkhosa zamphongo.
Pakuti Chauta ali ndi nsembe mu mzinda wa Bozira,
ndiye kuti kuphedwa kwa anthu ambiri m'dziko la Edomu.
7Pamodzi ndi anthuwo zidzaphedwanso
njati ndiponso ng'ombe zamphongo
zazing'ono ndi zazikulu zomwe.
Dziko lao lidzakhuta magazi,
ndipo nthaka yao idzakutidwa ndi mafuta.
8Imeneyi ndiyo nthaŵi imene Chauta adzalipsira,
pamene adzalanga adani a Ziyoni, ndi kuteteza anthu ake.
9Madzi a m'mitsinje ya ku Edomu adzasanduka phula,
ndipo dothi lake lidzasanduka sulufure.
Dziko lonse lidzasanduka phula lamoto.
10 Chiv. 14.11; 19.3 Motowo udzayaka usana ndi usiku,
ndipo utsi udzafuka kosalekeza.
Dziko lidzakhala chipululu pa mibadwo ndi mibadwo,
palibe ndi mmodzi yemwe amene adzayendamonso.
11M'dzikomo muzidzakhala akabaŵi ndi nungu,
akadzidzi ndi makwangwala.
Chauta adzalisandutsanso dziko loguga
ndi lopanda kanthu.
12Akuluakulu sadzasankhanso mfumu kumeneko,
ndipo atsogoleri ake onse adzakhala atachotsedwa.
13Minga idzamera m'nyumba zake zankhondo zotetezedwa,
khwisa ndi mitungwi zidzamera m'malinga mwake.
Nkhandwe zizidzayendayenda m'menemo,
nthiŵatiŵa zidzapezamo mokhala.
14Avumbwe adzakumana ndi afisi,
nyama zakuthengo zizidzaitanizana.
Kumeneko mizimu yoipa yausiku idzafika
ndipo idzapeza malo opumulirako.
15Akadzidzi adzamangako zisa zao, nkuikirako mazira,
ndi kuswa ana ao namaŵasamala.
Adembo adzasonkhana kumeneko aŵiriaŵiri.
16Funafunani ndi kuŵerenga m'buku la Chauta.
Mwa zolengedwazi palibe chimene chidzasoŵa,
ndipo sipadzakhala nchimodzi chomwe chopanda chinzake.
Pakuti Chauta walamula kuti zitero,
ndipo mzimu wake wazisonkhanitsa pamodzi.
17Chauta ndiye wagaŵa dzikolo,
wapatsa chilichonse chigawo chake.
Dzikolo lidzakhala lao mpaka muyaya,
ndipo zidzakhala m'menemo pa mibadwo yonse.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.