Ezek. 31 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Afanizira Ejipito ndi mtengo wa mkungudza

1Pa tsiku loyamba la mwezi wachitatu, chaka cha khumi ndi chimodzi cha ukapolo, Chauta adandipatsira uthenga uwu wakuti,

2“Iwe mwana wa munthu, unene mau aŵa kwa Farao mfumu ya ku Ejipito pamodzi ndi gulu lake la nkhondo:

“ ‘Kodi pa ukulu wanu nkukuyerekezani ndi yani?

3Ndithu ndidzakufanizirani

ndi mtengo wa mkungudza wa ku Lebanoni,

wa nthambi zabwino zochititsa mthunzi m'nkhalango,

nthambi zosomphoka, zofika mpaka ku mitambo.

4Madzi ndiwo amene ankaukulitsa,

ndipo akasupe ankautalikitsa.

Mitsinje inkayenda mozungulira kumene unaliri,

mifuleni yake inkafika ku mtengo uliwonse m'dzikomo.

5Koma mtengo uwu udatalika kwambiri

kupambana mtengo wina uliwonse.

Nthambi zake zidachuluka ndi kutalika kwambiri,

popeza kuti mizu yake inkalandira madzi ambiri.

6Mbalame zamumlengalenga zinkamanga zisa zake

m'nthambi za mtengowo.

Nyama zonse zakuthengo zinkaswanirana

m'munsi mwa nthambizo.

Mitundu yonse yotchuka ya anthu

inkakhala mumthunzi mwake.

7Unali mtengo wokongola kwambiri

wa nthambi zitalizitali,

chifukwa choti mizu yake inkazama

ndi kulandira madzi ambiri.

8 Gen. 2.9 M'munda wa Mulungu munalibe mkungudza

wofanafana ndi umenewo.

Munalibe mtengo wa paini

wa nthambi zofanafana ndi zake.

Munalibenso mkuyu umene unali ndi nthambi zotere.

M'munda wa Mulungu munalibe mtengo wina

wofanafana ndi umenewu kukongola kwake.

9Ndi Ineyo Mulungu amene ndidaukongoletsa,

pochulukitsa nthambi zake,

kotero kuti mitengo yonse ya mu Edeni, munda wa Mulungu

inkachita nawo nsanje.’

10“Nchifukwa chake Ine Ambuye Chauta ndikuti, Chifukwa choti mtengowo udatalika kwambiri nkufika mpaka ku mitambo, ndipo unkanyada pokula choncho,

11Ine ndidaupereka m'manja mwa mfumu yolamulira anthu a mitundu ina, kuti mfumuyo iwulange potsata zolakwa zake.

12Alendo ankhalwe kwambiri pakati pa mitundu ya anthu adzaudula, ndipo adzangoutaya. Nthambi zake zidzagwera pa mapiri, ndiponso m'zigwa zonse. Nthambi zakezo zidzathyokera m'mitsinje yam'dzikomo. Motero anthu a mitundu yonse ya dziko lapansi amene ankasangalala mumthunzi mwake adzausiya nachoka.

13Mbalame zonse zamumlengalenga zidzakhala pa thunthu la mtengo wakugwawo. Nyama zonse zakuthengo zidzakhala pa nthambi zake.

14Zonsezi zidzatero kuti pasakhale mtengo ndi umodzi womwe wa m'mbali mwa mtsinje umene udzatalike kwambiri, kapena umene nsonga zake zidzafike ku mitambo. Ndiponso pasadzakhale mitengo ina yolandira bwino madzi, imene msinkhu wake ungafike ku mitambo. Pakuti yonseyo kutha kwake ndi kufa, kupita kunsi kwa dziko lapansi, kukakhala pamodzi ndi anthu akufa, amene adaloŵa kale m'manda.

15“Zimene Ine Ambuye Chauta ndikunena ndi izi: Mkungudzawo utatsikira ku manda, ndidauza nyanja kuti iwulire maliro pa kuuphimba. Ndidaumitsa mitsinje yake, ndipo madzi ambiri adaphwa. Ndidachititsa mdima pa Lebanoni chifukwa cha mtengowo, ndipo mitengo yonse yam'dzikomo idauma.

16Mitundu ya anthu idagwedezeka pakumva mkokomo wa kugwa kwake, pamene ndidautsitsira ku manda pamodzi ndi amene adafa. Pamenepo ku dziko la akufa mitengo yonse ya ku Edeni, ndi yonse yokongola ya ku Lebanoni yothiriridwa bwino, idasangalatsidwa chifukwa cha zimenezi.

17Mitundu imene inkakhala mumthunzi mwake chifukwa cha kumvana nawo, nayonso idapezana nawo kumandako, pamodzi ndi amene adaphedwa ku nkhondo.

18“Pakati pa mitengo ya ku Edeni, kodi unalipo ndi umodzi womwe wolingana nawe pa ulemerero ndi pa ukulu? Komabe iwenso udzatsikira ku dziko la akufa, pamodzi ndi mitengo ina yonse ya ku Edeni. Udzagona pamodzi ndi amene adaphedwa ku nkhondo, m'gulu la anthu osaumbalidwa! Mtengowo ndi mfumu ya ku Ejipito pamodzi ndi anthu ake. Ndikutero Ine Ambuye Chauta.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help