1Adonizedeki mfumu ya ku Yerusalemu adamva kuti Yoswa wagonjetsa kotheratu mzinda wa Ai, ndipo waononga mzindawo pamodzi ndi mfumu yake, monga momwe adachitira Yeriko pamodzi ndi mfumu yake yomwe. Adamvanso kuti anthu a ku Gibiyoni adapangana za mtendere ndi Aisraele, ndipo kuti anali kukhala pakati pao.
2Motero anthu a ku Yerusalemu adachita mantha kwambiri, pakuti Gibiyoni unali mzinda waukulu, monga mzinda uliwonse wokhala ndi mfumu. Unali waukulu kupambana Ai, ndipo ankhondo ake anali olimba mtima.
3Motero Adonizedeki adatuma mithenga kwa Hohamu mfumu ya ku Hebroni, kwa Piramu mfumu ya ku Yaramuti, kwa Yafiya mfumu ya ku Lakisi ndi kwa Debiri mfumu ya ku Egiloni. Adatuma mau akuti,
4“Bwerani mudzandithandize kumenyana ndi Gibiyoni, chifukwa anthu ake apangana za mtendere ndi Yoswa ndiponso ndi Aisraele onse.”
5Mafumu asanu a Aamoriwo, mfumu ya ku Yerusalemu, mfumu ya ku Hebroni, mfumu ya ku Yaramuti, mfumu ya ku Lakisi ndiponso ya ku Egiloni, adagwirizana. Adasonkhanitsa ankhondo ao nazinga mzinda wa Gibiyoni, ndi kuuthira nkhondo.
6Anthu a ku Gibiyoni adatumiza mau kwa Yoswa ku zithando ku Giligala kuja kuti, “Mbuyathu, musatitaye ife atumiki anu. Bwerani msanga mudzatithandize! Tipulumutseni! Mafumu onse a Aamori atsika mapiri kudzamenyana nafe.”
7Tsono Yoswa ndi ankhondo ake onse ndi anthu ake onse olimba mtima adayambapo ulendo kuchoka ku Giligala.
8Ndipo Chauta adauza Yoswa kuti, “Usaŵaope anthu amenewo. Ndaŵapereka kale kwa iwe kuti uŵagonjetse. Palibe ndi mmodzi yemwe mwa iwo amene adzatha kulimbika.”
9Yoswa ndi ankhondo ake adayenda usiku wonse kuchoka ku Giligala, ndipo adakathira nkhondo mwadzidzidzi.
10Chauta adaŵachititsa mantha adaniwo pamene adangoona nkhondo ya Aisraele ija. Motero Aisraele adapambana Aamori ku Gibiyoni, naŵathamangitsa kutsika phiri la ku Betehoroni ndi kuŵakantha mpaka ku Azeka ndi ku Makeda.
11Pamene ankathaŵa nkhondo ya Aisraeleyo kutsika phiri ku Betehoroni mpaka ku Azeka, Chauta adagwetsa miyala yaikulu yamatalala pa iwo kuchokera kumwamba, ndipo idaŵapha. Ophedwa ndi matalala anali ambiri kupambana ophedwa ndi Aisraele.
12Pa tsiku limene Chauta adapatsa Aisraele mphamvu kuti agonjetse Aamori, Yoswa adalankhula naye. Tsono pamaso pa Aisraele onse adati,
“Iwe dzuŵa, ima pamwamba pa Gibiyoni,
iwe mwezi, ima pamwamba pa chigwa cha Ayaloni.”
13 2Sam. 1.18; Mphu. 46.4-6 Choncho dzuŵa lidaima pamodzimodzi, ndipo mwezi sudayendenso mpaka Aisraele atagonjetsa adaniwo kotheratu. Zimenezi zidalembedwa m'buku la Yasara. Dzuŵa lidangoima pamodzimodzi pakati pa mutu mu mlengalenga, ndipo silidayendenso mofulumira pafupi tsiku lonse.
14Chiyambire nkale lonse, sipadaonekepo tsiku longa limeneli loti Chauta adamvera munthu, popeza kuti ankamenyera Israele nkhondo.
15Zitatha izo Yoswa ndi gulu lake lankhondo adabwerera ku zithando ku Giligala.
Yoswa agwira mafumu asanu a Aamori.16Mafumu asanu onse aja adathaŵa nakabisala ku phanga ku Makeda.
17Pambuyo pake adapezeka, ndipo ena adadzauza Yoswa kuti mafumuwo akubisala kumeneko.
18Iye adalamula kuti, “Kunkhuniziranipo miyala pa khomo la phangalo, ndipo muikepo alonda.
19Koma inuyo musakhaleko kumeneko. Muŵapirikitse adaniwo, ndipo muŵathire nkhondo kuchokera kumbuyo. Musalole kuti akafike ku mizinda yao. Chauta, Mulungu wanu, wakupatsani mphamvu zoŵagonjetsera.”
20Ndipo Yoswa pamodzi ndi Aisraele adapha anthuwo. Amene sadaphedwe ndi okhawo amene adabisala m'mizinda yamalinga.
21Tsono anthu onse a Yoswa adabwerako bwino, nakafika ku zithando ku Makeda. Palibe ndi mmodzi yemwe m'dzikomo amene adayesanso kuputa Aisraele.
22Tsono Yoswa adati, “Tsekulani khomo la phanga lija, ndipo mafumu asanuwo mubwere nawo kuno.”
23Anthu adachita zimenezo: mafumu asanu aja adaŵatulutsadi, mfumu ya ku Yerusalemu, ya ku Hebroni, ya ku Yaramuti, ya ku Lakisi ndi ya ku Egiloni.
24Mafumu ameneŵa atabwera nawo kwa Yoswa, iye adaitana Aisraele onse. Ndipo adalamula akuluakulu ake amene adapita naye limodzi kuti, “Bwerani kuno, muŵaponde pa khosi mafumu ameneŵa, kusonyeza kuti agonjetsedwa.” Iwo adabweradi, naŵaponda pa khosi.
25Tsono Yoswa adauza akuluakuluwo kuti, “Musaope kapena kutaya mtima. Mukhale amphamvu ndiponso mulimbe mtima, poti Chauta adzaŵachita zimenezi adani anu onseŵa.”
26Pamenepo Yoswa adapha mafumu onsewo naŵapachika pa mitengo isanu, ndipo adakhala pa mitengo imeneyo mpaka madzulo.
27Dzuŵa litangoloŵa, Yoswa adalamula kuti atsitse mafumu aja pamitengopo, ndipo kuti aikidwe m'phanga lomwe ankabisalamolo. Tsono pa khomo la phangalo adatsekapo ndi miyala ikuluikulu, ndipo ikali pomwepo mpaka lero lino.
Yoswa apitiriza kulanda dziko la Aamori.28Tsiku lomwelo Yoswa adathira nkhondo mzinda wa Makeda naugwira pamodzi ndi mfumu yake. Adapha onse amumzindamo, ndipo panalibe ndi mmodzi yemwe wotsala wamoyo. Mfumu ya ku Makeda adaichita zomwe adaichita mfumu ya ku Yeriko.
29Tsono Yoswa pamodzi ndi Aisraele adapitirira kuchokera ku Makeda nakafika ku Libina, nauthira nkhondo mzindawo.
30Ndipo Chauta adapereka mzindawo m'manja mwa Aisraele. Adakantha munthu aliyense mumzindamo ndi lupanga, osasiyapo ndi mmodzi yemwe. Mfumu ya mzindawo adaichita zomwe adaichita mfumu ya ku Yeriko.
31Zitatha zimenezi, Yoswa pamodzi ndi ankhondo ake adapitirira kuchokera ku Libina mpaka ku Lakisi. Adazinga mzindawo ndi kuuthira nkhondo.
32Chauta adapatsa Aisraele mphamvu zogonjetsera mzinda wa Lakisi pa tsiku lachiŵiri la nkhondoyo. Tsono monga momwe adachitira ku Libina, sadapulumutsepo ndi mmodzi yemwe, koma adapha onse.
33Pamenepo Horamu, mfumu ya ku Gezere, anadza kudzathandiza Lakisi, koma Yoswa adamgonjetsa pamodzi ndi anthu ake omwe, osasiyapo wamoyo ndi mmodzi yemwe.
34Pambuyo pake Yoswa pamodzi ndi ankhondo ake adapitirira ku Lakisi mpaka ku Egiloni. Adazinga mzinda wa Egiloniwo ndi kuuthira nkhondo.
35Adaugonjetsa tsiku limodzi lomwelo, napha onse amumzindamo monga momwe adachitira ku mzinda wa Lakisi uja.
36Tsono Yoswa ndi ankhondo ake adapitirira ku Egiloni mpaka kubzola mapiri, ndi kukafika ku mzinda wa Hebroni. Adauthira nkhondo,
37mpaka kuugonjetsa. Adapha ndi lupanga mfumu pamodzi ndi anthu onse amumzindamo, ndi onse a m'midzi yapafupi omwe. Tsono Yoswa adalamula kuti mzindawo auwononge, monga momwe adachitira mzinda wa Egiloni. Palibe ndi mmodzi yemwe m'menemo amene adatsala wamoyo.
38Pamenepo Yoswa pamodzi ndi ankhondo ake adatembenukira mzinda wa Debiri, ndipo adauthira nkhondo.
39Adaugonjetsa naulanda pamodzi ndi mfumu yake, kudzanso midzi yoyandikana nawo. Adapha anthu onse akumeneko. Yoswa adauchita mzinda wa Debiri zomwe adauchita mzinda wa Hebroni ndi Libina pamodzi ndi mafumu ake.
40Choncho Yoswa adagonjetsa dziko lonselo. Adagonjetsa mafumu onse m'dziko lamapiri lija, m'dziko lakumwera, m'dziko lakuchigwa ndi lamagomo. Sadasiyepo ndi mmodzi yemwe, koma adapha onse. Zimenezi ndi zimene Chauta, Mulungu wa Aisraele, adalamula.
41Yoswa adagonjetsa adani onse kuyambira ku Kadesi-Baranea chakumwera, mpaka ku Gaza kufupi ndi nyanja, kuphatikizapo dziko lonse la Goseni mpaka ku Gibiyoni.
42Yoswa adagonjetsa mafumu onseŵa pamodzi ndi dziko lao lonse kamodzinkamodzi, chifukwa choti Chauta, Mulungu wa Aisraele, ndiye amene ankaŵamenyera nkhondoyo.
43Zitatha zimenezi, Yoswa pamodzi ndi ankhondo ake adabwerera ku zithando zao ku Giligala.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.