1Nthaŵi imeneyo atsogoleri a mabanja a Aisraele ankakhala ku Yerusalemu. Tsono anthu ena onse adachita maele kuti apeze munthu mmodzi pa anthu khumi aliwonse oti azikhala ku Yerusalemu, mzinda wopatulikawo, ndipo anthu asanu ndi anai otsala azikhalabe m'midzi.
2Ndipo anthu adayamika anzao onse amene adadzipereka kuti azikhala ku Yerusalemu.
3 Neh. 7.73 Aisraele wamba ambiri, pamodzi ndi ansembe, Alevi, anthu otumikira ku Nyumba ya Mulungu, ndiponso zidzukulu za atumiki a Solomoni, onsewo ankakhala m'midzi mwao, aliyense m'dera la choloŵa chake. Koma akuluakulu a m'chigawo cha Yuda anali atakhazikika ku Yerusalemu.
4Ku Yerusalemu kunkakhalanso ena a fuko la Yuda ndiponso ena a fuko la Benjamini. Zina mwa zidzukulu za Yuda ndi izi: Ataya mwana wa Uziya, mwana wa Zekariya, mwana wa Amariya, mwana wa Sefatiya, mwana wa Mahalalele, onsewo anali ana a Perezi.
5Panalinso Maaseiya mwana wa Baruki, mwana wa Kolihoze, mwana wa Hazaya, mwana wa Adaya, mwana wa Yoyaribu, mwana wa Zekariya, mwana wa Msiloni.
6Ana ndi adzukulu onse a Perezi amene ankakhala ku Yerusalemu analipo anthu akuluakulu okwanira 468.
7Zidzukulu za Benjamini zinali izi: Salu mwana wa Mesulamu, mwana wa Yoedi, mwana wa Pedaya, mwana wa Kolaya, mwana wa Maaseiya, mwana wa Itiyele, mwana wa Yesaya.
8Achibale ake anali Gabai ndi Salai. Onse pamodzi analipo 928.
9Yowele, mwana wa Zikiri, ndiye amene anali kapitao wao. Ndipo Yuda mwana wa Hasenuwa anali kapitao wachiŵiri wa mumzindamo.
10Ansembe anali aŵa: Yedaya mwana wa Yoyaribu, Yakini,
11Seraya mwana wa Hilikiya, mwana wa Mesulamu, mwana wa Zadoki, mwana wa Meraiyoti, mwana wa Ahitubi amene anali mkulu wa ansembe ku Nyumba ya Mulungu,
12ndiponso achibale ao amene ankagwira ntchito m'Nyumbamo, onse pamodzi analipo 822. Panalinso Adaya, mwana wa Yerohamu, mwana wa Pelaliya, mwana wa Amizi, mwana wa Zekariya, mwana wa Pasuri, mwana wa Malikiya
13ndiponso achibale ao amene anali akuluakulu a banja lao. Onse pamodzi analipo 242. Amasisai, mwana wa Azarele, mwana wa Ahazai, mwana wa Mesilemoti, mwana wa Imeri,
14ndiponso achibale ao amene anali ankhondo olimba mtima. Onse pamodzi analipo 128, ndipo kapitao wao anali Zabidiele, mwana wa Hagedolimu.
15Alevi anali aŵa: Semaya, mwana wa Hasubu, mwana wa Azirikamu, mwana wa Hasabiya, mwana wa Buni.
16Sabetai ndiponso Yozabadi anali atsogoleri a Alevi amene ankayang'anira ntchito ya kunja kwa Nyumba ya Mulungu.
17Mataniyo, mwana wa Mika, mwana wa Zabidi, mwana wa Asafu, amene anali mtsogoleri pa mapemphero achiyamiko m'Nyumba ya Mulungu, ndiponso Bakibukiya, amene anali wachiŵiri pakati pa abale ake. Panalinso Abida, mwana wa Samuwa, mwana wa Galali, mwana wa Yedutuni.
18Alevi onse amene ankakhala mu mzinda wopatulika analipo 284 pamodzi.
19Alonda a ku Nyumba ya Mulungu anali aŵa: Akubu, Talimoni ndiponso achibale ao onse pamodzi analipo 172.
20Aisraele ena ndiponso ansembe ndi Alevi otsala anali m'midzi ya Yuda ndipo aliyense ankakhala m'dera la choloŵa chake.
21Koma anthu otumikira ku Nyumba ya Mulungu ankakhala ku Ofele, mu Yerusalemu, ndipo Ziha ndi Gisipa ankaŵayang'anira.
22Kapitao wa Alevi ku Yerusalemu anali Uzi, mwana wa Bani, mwana wa Hasabiya, mwana wa Mataniya, mwana wa Mika. Anali mmodzi mwa zidzukulu za a Asafu, amene anali oimba nyimbo zofunika pa miyambo ya m'Nyumba ya Mulungu.
23Pakuti mfumu idaalamula kuti magulu oimbawo azikhalapo tsiku ndi tsiku, potsogolera maimbidwe a nyimbo za m'Nyumba ya Mulungu.
24Tsono Petahiya, mwana wa Mesezabele, mmodzi mwa adzukulu a Sera wa m'fuko la Yuda, ankaimirira Aisraele ku bwalo la mfumu ya ku Persiya.
Anthu okhala m'midzi ina ndi m'mizinda ina25Anthu ena a fuko la Yuda ankakhala ku Kiriyati-Ariba ndi midzi yake, ku Diboni ndi midzi yake, ku Yekabizeele ndi midzi yake.
26Ankakhalanso ku Yesuwa, ku Molada ndi ku Betepeleti,
27ku Hazarisuwala, ku Beereseba ndi midzi yake.
28Ena ankakhala ku Zikilagi, ku Mekona ndi midzi yake,
29ku Enirimoni, ku Zora, ku Yarimuti,
30Zanowa, Adulamu ndi midzi yake. Ankakhalanso ku Lakisi ndi ku minda yake, ku Azeka ndi midzi yake. Motero ankakhala m'midzi yonse kuyambira ku Beereseba mpaka ku chigwa cha Hinomu.
31Anthu a fuko la Benjamini nawonso adakhala kuyambira ku Geba, kubzola mpaka ku Mikimasi, Aiya, Betele ndi midzi yake,
32Anatoti, Nobi, Ananiya,
33Hazori, Rama, Gitaimu,
34Hadidi, Zeboimu, Nebalati,
35Lodi, Ono, ndiponso ku chigwa cha anthu aluso.
36Magulu ena a Alevi amene ankakhala m'dziko la Yuda adasamukira ku dziko la Benjamini.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.