2 Am. 8 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

1Koma Yudasi, amene ankatchedwanso Makabeo pamodzi ndi anzake, adaloŵa kachetechete m'midzi, naitana achibale ao kuti abwere. Adasankhula onse otsatabe za chipembedzo Chachiyuda, nasonkhanitsa khamu la anthu ngati 6,000 pamodzi.

2Adapempha Ambuye kuti ayang'anire ndi kuthandiza anthu ao amene anthu a mitundu ina yonse ankaŵapondereza, ndipo kuti aimvere chisoni Nyumba yao imene anthu osapemphera adaiipitsa.

3Adapemphanso kuti aumvere chifundo mzinda umene udagwetsedwa pansi ndipo unali pafupi kusalazidwa, ndiponso kuti amve magazi okhetsedwa amene ankalira kwa Iye.

4Ndipo adapempha kuti akumbukire ana aang'ono osachimwa amene adaphedwa, ndiponso kuti agwetse mkwiyo wake waukulu pa anthu amene adaalalatira dzina lake.

5Makabeo atakonza bwino gulu lake lankhondo, anthu a mitundu ina sadathe kulimbana naye, chifukwa mkwiyo wa Ambuye udaasanduka chifundo.

6Ankafika mwadzidzidzi nkutentha mizinda ndi midzi. Atalanda malo abwino omenyera nkhondo, ankathamangitsa adani kambirimbiri.

7Adazindikira kuti nthaŵi yausiku ndiye inali yabwino yomenyera nkhondo zimenezi. Motero mbiri ya kulimba mtima kwake idawanda ponseponse.

Ptolemeyo atuma Nikanore kukamenyana ndi Yudasi

8Filipo ataona kuti Yudasi pang'onopang'ono akulanda malo ambiri, ndi kugonjetsa adani ake kaŵirikaŵiri, adalemba kalata kwa Ptolemeyo, bwanamkubwa wa ku Celesiriya ndi Fenisiya, kuti adzamthandize pa ntchito zake zaufumu.

9Mosachedwa Ptolemeyo adatuma Nikanore, mwana wa Patrokulo, mmodzi mwa abwenzi enieni a mfumu. Adampatsa ankhondo opitirira 20,000 a mitundu ina yosiyanasiyana, kuti akaonongeretu mtundu wonse wa Ayuda. Pamodzi ndi iyeyo adatuma Gorjiyasi amene anali mkulu wolamulira ankhondo ndiponso katswiri pa zankhondo.

10Nikanore adafuna kuti apeze ndalama zamsonkho zokwanira makilogramu 68,000 a siliva, zimene mfumu inkayenera kulipira ku Roma, azipeze pogulitsa anthu achiyuda odzagwidwa.

11Tsono mosataya nthaŵi adatumiza mau ku mizinda yoyandikana ndi nyanja yaikulu, kuti adzagule akapolo achiyuda. Adaŵalonjeza kuti pa akapolo 90 adzapereka makilogramu 34 a siliva. Sadadziŵe chilango chimene Wamphamvuzonse anali pafupi kudzamlanga nacho.

12Yudasi atamva kuti Nikanore akubwera, adadziŵitsa anzake za nkhondo imene inkabwerayo.

13Tsono ena amene anali ndi mitima yofooka ndi osakhulupirira chilungamo cha Mulungu, adathaŵa kupita kwina.

14Koma ena adagulitsa zonse zoŵatsalira, chonsecho ankapemphera kwa Ambuye kuti apulumutse anzao amene Nikanore wosamverayo anali ataŵagulitsa asanakumane nawo pa nkhondo.

15Adapemphera motero osati chifukwa cha eniake okhawo ai, koma chifukwa cha chipangano chimene Ambuye adaachita ndi makolo ao, ndiponso chifukwa chakuti dzina lake loyera ndi laulemerero linkalemekezedwa pakati pao.

16Tsono Makabeo adasonkhanitsa anthu ake 6,000 omutsalira. Adaŵalangiza kuti asaope adani ao, ndipo asavutike ndi unyinji wa akunja odzamenyana nawo mopanda chilungamowo. Koma adaŵauzitsa kuti amenye nkhondo ndi mtima wolimba,

17pokumbukira ntchito zoipa za akunjawo zonyozetsa malo oyera, zoononga mzinda ndi zofuna kufafaniza miyambo ya makolo ao.

18Adati, “Iwo akukhulupirira zida zao ndi chamuna chao, koma ife tikukhulupirira Mulungu Wamphamvuzonse amene nkutsinzina chabe angathe kugwetsa pansi anthu ofuna kumenyana nafe, ngakhalenso dziko lonse lapansi.”

19Kenaka Yudasi adaŵakumbutsa za chithandizo chimene Mulungu adaapatsa makolo ao; monga pa nthaŵi ya Senakeribu, pamene paja anthu ake 185,000 adafa.

20Pa nthaŵinso imene ku Babiloni Ayuda ankamenyana nkhondo ndi Agalatiya, Ayuda analipo 8,000, anthu a ku Masedoniyawo othandizana nawo analipo 4,000. Komabe Amasedoniya atapanikizidwa, Ayuda 8,000 aja adaŵathandiza nagonjetsa anthu 120,000, chifukwa cha chithandizo chochokera kumwamba. Pambuyo pake adalanda zofunkha zambiri.

21Ataŵalimbikitsa motero ndi kuŵauza kuti avomere kufera Malamulo a Mulungu ndi dziko lao, adagaŵa gulu lakelo panai.

22Abale ake Simoni, Yosefe ndi Yonatani adaŵapatsa ntchito yolamulira magulu atatu napatsa aliyense anthu 1,500.

23 1Am. 3.48 Tsono adalamula kuti Eleazara aŵerenge momveka mau a m'buku loyera, ndipo adaŵapatsa mau oŵafuula pa nkhondo akuti “Mulungu adzatithandiza.” Motero iye adatsogolera gulu loyamba, ndipo adakamenyana nkhondo ndi Nikanore.

24Popeza kuti Wamphamvuzonse ankaŵathandiza, iwo adapha adani opitirira 9,000. Adavulaza ankhondo ambiri a Nikanore, gulu lonse lankhondo nkulithaŵitsa.

25Adalandanso ndalama za anthu aja amene adaafuna kudzaŵagula ngati akapolo. Atapirikitsira adaniwo kutali pang'ono, adayenera kubwerera m'mbuyo, chifukwa nthaŵi idaapita.

26Pajanso tsikulo linali lokonzekera Sabata, nchifukwa chake adaleka kuŵalondola.

27Tsono adatenga zida za adani ndi kuŵalanda chuma chao. Ndipo adayeretsa tsiku la Sabata, nayamika ndi kutamanda Ambuye, chifukwa choŵapulumutsa pa tsikulo limene adaalisankhula kuti ayambepo kuŵachitira chifundo.

28Tsiku la Sabata litapita adaŵagaŵira zofunkha zina anthu amene adaazunzika pa nthaŵi ya masautso ija. Zina adagaŵira akazi amasiye ndi ana amasiye. Tsono iwowo adagaŵana zotsala.

29Atatero, adapemphera onse pamodzi napempha Ambuye achifundo kuti ayanjanenso kwathunthu ndi atumiki ao.

Yudasi agonjetsa Timoteo ndi Bakide

30Ayuda adamenyananso ndi ankhondo a Timoteo ndi a Bakide napha opitirira 20,000, nkulanda nyumba zankhondo zazitali zedi. Zofunkha zinali zambiri, adazigaŵa molingana, gawo lina lokhalira iwo omwe, gawo lina lokhalira anthu amene adaazunzika, ndiponso ana amasiye, akazi amasiye ndi nkhalamba.

31Adatola zida za adani, naziika pa malo oyenera mosamala. Kenaka chuma chotsala adapita nacho ku Yerusalemu.

32Adapha mtsogoleri wa ankhondo a Timoteo; iye anali munthu woipa kwambiri, amene adaaŵachita Ayuda zoipa zambiri.

33Pa masiku amene ankachita chikondwerero mu mzinda wa makolo ao, adatentha adani onse amene kale adaatentha zitseko zopatulika za Nyumba ya Mulungu. Adaniwo anali Kalistene ndi anthu ena, amene anali atathaŵira m'nyumba yaing'ono. Motero anthuwo adalandira chilango cha chipongwe chao.

34Nikanore, munthu wachifwamba amene adaaitana amalonda 1,000 aja kuti aŵagulitsire Ayuda,

35adagonjetsedwa ndi mphamvu za Ambuye ndi za anthu amene iye ankaŵayesa achabechabe. Adavula zovala zake zokongola zankhondo nachokapo mwamsanga yekhayekha ngati kapolo wothaŵa; adayenda mwamwai podutsa m'minda mpaka kukafika ku mzinda wa Antiokeya, atataya ankhondo ake onse.

36Motero iye uja amene ankaganiza zokhoma msonkho kwa Aroma pakugulitsa Ayuda a ku Yerusalemu ngati akapolo, adatsimikiza kuti Ayudawo anali wina naye woŵateteza, ndipo choncho panalibe munthu wotha kuŵagonjetsa, chifukwa ankamvera malamulo ake a Mtetezi waoyo.

Kufa kwa Antioko Epifane
Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help