1 Ako. 10 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mbiri ya Aisraele ikhale chenjezo kwa akhristu

1 Eks. 13.21, 22; Eks. 14.22-29 Abale, ndifuna kuti mudziŵe zimene zidaŵachitikira makolo athu akale aja. Onse adayenda mu mthunzi wa mtambo, ndipo onse adaoloka Nyanja Yofiira.

2Motero mumtambomo ndi m'nyanjamo onsewo adachita ngati kubatizidwa ndi kukhala amodzi ndi Mose.

3Eks. 16.35 Onse ankadya chakudya chauzimu chimodzimodzi.

4Eks. 17.6; Num. 20.11 Onse ankamwanso chakumwa chauzimu chimodzimodzi, pakuti analikumwa m'thanthwe lauzimu limene linkaŵatsatira. Thanthwelo linali Khristu yemwe.

5Num. 14.29, 30 Komabe ambirimbiri mwa iwo Mulungu sadakondwere nawo, kotero kuti adafera m'chipululu.

6 Num. 11.4 Tsono zimene zidachitikazi ndi zitsanzo zotichenjeza ife, kuti tisamasirira zoipa monga adaachitira iwowo.

7Eks. 32.6 Tisakhale opembedza mafano, monga analiri ena mwa iwo. Paja Malembo akuti, “Anthu adakhala pansi kuti adye ndi kumwa, kenaka nkuimirira kuti azivina.”

8Num. 25.1-18 Tisachite dama monga momwe adaachitira ena mwa iwo: paja pa tsiku limodzi adafa anthu zikwi makumi aŵiri ndi zitatu.

9Num. 21.5, 6 Tisapute Ambuye monga momwe adaaŵaputira ena mwa iwo: paja anthuwo adaphedwa ndi njoka.

10Num. 16.41-49 Musadandaule monga momwe adaadandaulira ena mwa iwo: paja adaphedwa ndi mngelo wodzetsa imfa.

11Zonsezi zidaŵagwera makolo athuwo kuti zikhale zoŵachenjeza. Ndipo zidalembedwa kuti tipezepo phunziro ifeyo, amene tikuyandikira nthaŵi ya kutha kwa zonse.

12Tsono amene akuganiza kuti waimirira molimba, achenjere kuti angagwe.

13Yud. 8.25-27; Mphu. 15.11-20Mayeso amene inu mwakumana nawo, sasiyana ndi mayeso amene anthu ena onse adakumana nawo. Mulungu ndi wokhulupirika, sangalole kuti muyesedwe kopitirira mphamvu zanu. Koma pamene mudzayesedwa, Iye yemwe adzakukonzerani njira yopulumukira, pakukupatsani mphamvu kuti mupirire.

Aŵachenjeza za kupembedza mafano

14Tsono okondedwa anga, pewani kupembedza mafano.

15Ndikulankhula nanu ngati anthu anzeru. Muweruze nokha zimene ndikunenazi.

16Mt. 26.26-28; Mk. 14.22-24; Lk. 22.19, 20 Nanga chikho chimene timachidalitsa mothokoza Mulungu, kodi suja timaphatikizana ndi magazi a Khristu tikamweramo? Nanga mkate umene timaunyema, kodi suja timaphatikizana ndi thupi la Khristu tikaudya?

17Popeza kuti mkate ndi umodzi wokha, ife tonse, ngakhale tili ambiri, ndife thupi limodzi, chifukwa tonse timagaŵana mkate umodzi womwewo.

18 Lev. 7.6 Onani zimene amachita Ayuda. Nanga amene amadyako zoperekedwa nsembe, kodi suja amachita nao miyambo ya pa guwa lansembelo?

19Tsono tanthauzo la zimene ndikunenazi nchiyani? Kodi ndiye kuti nsembe yoperekedwa kwa fano nkanthu? Kapena kuti fanolo nkanthu?

20Deut. 32.17 Iyai, koma kuti zimene anthu akunja amapereka nsembe, amapereka kwa Satana, osati kwa Mulungu. Sindifuna kuti inu muyanjane ndi Satana.

21Simungathe kumwera m'chikho cha Ambuye nkumweranso m'chikho cha Satana. Simungathe kudyera pa tebulo la Ambuye nkudyeranso pa tebulo la Satana.

22Deut. 32.21Kodi tichite kuŵaputa dala Ambuye? Kodi mphamvu zathu nkupambana zao?

Azilemekeza Mulungu pa zochita zao zonse

23 1Ako. 6.12 Zinthu zonse nzololedwa, koma si zonse zili ndi phindu. Zonse nzololedwa, koma si zonse zimathandiza.

24Munthu asamangodzifunira yekha zabwino, koma makamaka azifunira anzake zabwino.

25Mungathe kudya nyama iliyonse imene amagulitsa pa msika, osafunsa mafunso okhudzana ndi m'mene mtima wanu umamvera.

26Mas. 24.1 Paja Malembo akuti, “Dziko lapansi ndi zonse zam'menemo ndi za Chauta.”

27Mkunja akakuitanani kuti mukadye naye, inuyo nkuvomera kupitako, mukadye chilichonse chimene akakupatseni. Musakafunse mafunso okhudzana ndi m'mene mtima wanu umamvera.

28Koma wina akakuuzani kuti, “Nyama iyi idaperekedwa kwa mafano,” apo ndiye musadye nyamayo. Chifukwa cha amene wakuuzayo, usadye nyamayo, kuwopa kuti mtima ungavutike.

29Osati kuti iweyo ungavutike mu mtima ai, koma iye uja amene wakuuzayo.

Pamenepo udzati, “Kodi ufulu wanga utsekerezedwe chifukwa munthu wina mtima wake ukumuvuta?

30Ngati ine ndikuthokoza Mulungu chifukwa cha chakudya changa, nanga munthu angandinyoze bwanji chifukwa cha chakudya chimene ndikuchilandira mothokoza Mulungu?”

31Tsono, kaya mulikudya, kaya mulikumwa, kaya mukuchita chilichonse, muzichita zonse kuti mulemekeze Mulungu.

32Moyo wanu ukhale wosaphunthwitsa Ayuda, kapena anthu a mitundu ina, kapenanso Mpingo wa Mulungu.

33Muzichita monga momwe ndimachitira ine. Ndimayesa kukondweretsa anthu onse pa zonse. Sindifunafuna zokomera ineyo, koma ndimafunafuna zokomera anthu onse, kuti apulumuke.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help