2 Mbi. 16 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Asa apeza mavuto ndi Israele(1 Maf. 15.17-22)

1Pa chaka cha 36 cha ufumu wa Asa, Baasa mfumu ya ku Israele, adapita kukathira nkhondo dziko la Yuda. Adamangira linga mzinda wa Rama kuti aziletsa anthu kuloŵa kapena kutuluka m'dziko la Asa, mfumu ya ku Yuda.

2Tsono Asa adatenga siliva ndi golide ku malo osungira chuma cha ku Nyumba ya Chauta ndiponso ku nyumba ya mfumu, nazitumiza kwa Benihadadi, mfumu ya ku Siriya, amene ankakhala ku Damasiko. Mau a Asa anali akuti,

3“Tiye tigwirizane ine ndi iwe, monga m'mene ankachitira bambo wanga ndi bambo wako. Ona ndikukutumizira mphatso za siliva ndi golide. Pita ukaphwanye chigwirizano chako ndi Baasa, mfumu ya ku Israele, kuti asadzanditherenso nkhondo.”

4Benihadadi adamvera zimene adanena mfumu Asa zija, motero adatuma atsogoleri a magulu ake ankhondo kukathira nkhondo mizinda ya ku Israele. Adagonjetsa Iyoni, Dani, Abele-Maimu ndi mizinda yonse ya ku Nafutali yosungiramo zinthu.

5Tsono Baasa atazimva zimenezi, adaleka kumangira Rama linga ndipo ntchito yonseyo adaisiya.

6Apo mfumu Asa adabwera ndi Ayuda onse, ndipo adadzanyamula miyala ndi mitengo imene Baasa ankamangira linga la Rama. Zimenezi Asa adamangira linga la Geba ndi la Mizipa.

Za Mneneri Hanani

7Nthaŵi imeneyo mneneri Hanani adadza kwa Asa mfumu ya ku Yuda, namuuza kuti, “Chifukwa chakuti mudakhulupirira mfumu ya ku Siriya, osakhulupirira Chauta, Mulungu wanu, gulu lankhondo la mfumu ya ku Siriya lakuthaŵirani.

8Kodi Aetiopiya ndi Alibiya sanali gulu lalikulu lankhondo, lokhala ndi magaleta ochuluka ndiponso anthu ambirimbiri okwera pa akavalo? Komabe chifukwa chodalira Chauta, Chautayo adaŵapereka kwa inu.

9Paja maso a Chauta amayang'ana uku ndi uku pa dziko lonse lapansi, kuti aonetse mphamvu zake kwa anthu amene mtima wao uli wangwiro kwa Iyeyo. Inuyo mwachita zopusa pa zimenezi. Ndiye kuyambira tsopano lino, mpaka m'tsogolo muno, mudzakhala pa nkhondo.”

10Apo Asa adapsera mtima mneneriyo, ndipo adammanga namuika m'ndende, popeza kuti adaakwiya naye kwambiri chifukwa cha zimenezi. Kenaka Asayo adayamba kuchita zankhalwe pa anthu enanso nthaŵi yomweyo.

Kufa kwa Asa(1 Maf. 15.23-24)

11Tsono ntchito za Asa, kuyambira pa chiyambi mpaka pomaliza, zidalembedwa m'buku la Mafumu a ku Yuda ndi a ku Israele.

12Pa chaka cha 39 cha ufumu wake, Asa adayamba kudwala nthenda ya mapazi, ndipo nthendayo idakula kwambiri. Komabe ngakhale ankadwala choncho, sadapemphe chithandizo kwa Chauta, koma kwa asing'anga.

13Tsono adamwalira, pa chaka cha 41 cha ufumu wake.

14Adamuika m'manda amene iyeyo adaadzisemera mu mzinda wa Davide. Adagoneka mtembo wake pa chithatha chimene adaikapo zonunkhira zamitundumitundu zimene anthu opanga zonunkhira adazikonza. Ndipo adasonkha chimoto chachikulu kwambiri chomchitira ulemu.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help