Mik. 6 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Israele adzudzulidwa chifukwa cha machimo a anthu ake

1Imvani tsopano zimene Chauta anene.

Dzukani Ambuye,

mufotokoze pamaso pa mapiri mlandu wanu.

Magomo amve mau anu.

2Imvani mlandu wa Chauta, inu mapiri,

ndi inunso maziko amuyaya a dziko lapansi.

Chautatu akuimba mlandu anthu ake,

akutsutsana ndi Aisraele.

3Chauta akuti,

“Inu anthu anga, kodi ndakuchitani chiyani?

Kodi ndakutopetsani nchiyani?

Tandiyankhani!

4 Eks. 12.50, 51; Eks. 4.10-16; Eks. 15.20 Paja Ine ndidakutulutsani ku dziko la Ejipito.

Ndidakuwombolani ku dziko laukapololo.

Ndipo ndidaachita kutuma Mose, Aroni

ndi Miriyamu kuti akutsogolereni.

5 Num. 22.2—24.25; Yos. 3.1—4.19 Inu anthu anga,

kumbukirani zimene Balaki, mfumu ya ku Mowabu,

adaafuna kukuchitani,

ndiponso m'mene Balamu mwana wa Beori adamuyankhira.

Kumbukirani zimene zidachitika

pa ulendo wochoka ku Sitimu kupita ku Giligala.

Kumbukirani zonsezi kuti muzindikire

zimene Ine Chauta ndidachita pofuna kukupulumutsani.”

Zimene Chauta afuna

6Kodi nditenge chiyani kuti ndifike pamaso pa Chauta,

kuti ndikapembedze Mulungu Wakumwamba?

Kodi nditenge anaang'ombe a chaka chimodzi

kuti ndipereke nsembe zopsereza?

7Kodi Chauta adzakondwera ndi nkhosa zamphongo

zikwi zingapo kapena mitsinje ya mafuta zikwi khumi?

Kodi ndidzapereke mwana wanga wachisamba

chifukwa cha zolakwa zanga?

Kodi mwana wanga adzakhale nsembe

yolipira tchimo langa?

8Iyai, Chauta adakuwonetsa kale, munthu iwe,

chimene chili chabwino.

Zimene akufuna kuti uzichita ndi izi:

uzichita zolungama, uzikhala wachifundo,

ndipo uziyenda modzichepetsa pamaso pa Mulungu wako.

Aisraele alakwa, nalangidwa

9Ndi nzeru kuwopa dzina la Chauta.

Akuuza mzinda wa Yerusalemu kuti,

“Imvani, inu anthu onse okhala mumzinda muno.

10Kodi Ine ndingathe kuiŵala chuma chimene

chili m'nyumba za anthu oipa,

chimene adachipata monyenga,

ndiponso muyeso wopereŵera

umene uli wotembereredwa?

11Kodi ndingathe kulekerera munthu

amene ali ndi sikelo zobera anzake

ndiponso miyeso yonyenga?

12Anthu olemera amachita zankhondo.

Anthu onse ndi abodza,

amangokhalira kunama.

13Nchifukwa chake ndayambapo kukukanthani,

kukuwonongani chifukwa cha machimo anu.

14Mudzadya, koma simudzakhuta.

Njala sidzakuchokani.

Mudzakundika zinthu, koma sizidzasungika.

Zimene mudzakundika zidzaonongedwa pa nkhondo.

15Mudzabzala, koma simudzakolola,

Mudzayenga mafuta a olivi, koma simudzaŵadzola.

Mudzaponda mphesa, koma vinyo wake simudzamulaŵa.

16 1Maf. 16.23-28; 1Maf. 16.29-34; 21.25, 26 Mwasunga machitidwe oipa a mfumu Omuri

ndi ntchito zonse za banja la Ahabu.

Mwatsata njira zao zonse.

Motero ndidzakuwonongani kotheratu.

Anthu a mitundu ina adzakunyodolani,

kulikonse anthu adzakunyozani.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help