Yes. 43 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Mulungu alonjeza kupulumutsa anthu ake

1Koma tsopano Chauta amene adakulenga iwe Yakobe,

amene adakuumba iwe Israele, akunena kuti,

“Usaope, chifukwa ndidakuwombola,

ndidachita kukutchula dzina lako, ndiwe wanga.

2Pamene ukuwoloka nyanja, ndidzakhala nawe,

pamene ukuwoloka mitsinje, siidzakukokolola.

Pamene ukudutsa pa moto sudzapsa,

malaŵi ake sadzakutentha.

3Pajatu Ine ndine Chauta, Mulungu wako.

Ndine Woyera uja wa Israele,

Mpulumutsi wako.

Ndidzapereka Ejipito pofuna kuwombola iwe.

Ndidzapereka Etiopiya ndi Seba m'malo mwa iwe.

4Popeza kuti ndiwe wanga wapamtima,

ndidzapereka anthu m'malo mwa iwe.

Chifukwa ndiwe wamtengowapatali pamaso panga,

ndipo ndimakukonda, ndidzapereka

mitundu ya anthu pofuna kuwombola moyo wako.

5Usaope, ndili nawe.

Ndidzabweza zidzukulu zako kuchokera kuvuma,

ndidzakusonkhanitsani nonse kuchokera kuzambwe.

6Ndidzauza akumpoto kuti ‘Muŵaleke.’

Ndidzalamula akumwera kuti ‘Musaŵagwire.’

Ana anga aamuna abwerere kuchokera

ku maiko akutali,

ana anga aakazi abwerere kuchokera

ku mathero a dziko lapansi.

7Onsewo amadziŵika ndi dzina langa,

ndidaŵalenga chifukwa cha ulemerero wanga,

ndidaŵapanga ndi kuŵapatsa moyo.”

Aisraele ndi mboni za Chauta

8Mulungu akunena kuti,

“Itanani anthu anga ku bwalo la milandu.

Maso ali nawo, koma sakupenya.

Makutu ali nawo, koma sakumva.

9Mitundu yonse ya anthu isonkhane,

anthu a m'maiko onse akhalepo pamlandupo.

Ndani mwa iwo adaathapo kuneneratu zimenezi?

Ndani mwa iwo adaathapo kutifotokozera zakale?

Abwere ndi mboni zao,

kuti zidzatsimikize mau ao,

kuti anthu ena amve ndi kunena kuti, ‘Nzoonadi.’

10Inu Aisraele, ndinu mboni zanga,

ndinu atumiki anga amene ndidakusankhulani,

kuti mundidziŵe ndi kundikhulupirira,

ndipo mumvetse kuti Mulungu ndine ndekha.

Patsogolo panga sipadapangidwepo mulungu wina,

ndipo pambuyo panga sipadzakhalanso wina.

11Chauta ndi Ineyo,

mpulumutsi wanu ndine ndekha.

12Ndine amene ndidaneneratu zimenezi,

ndipo ndine ndidakupulumutsani.

Si mulungu wina wachilendo

amene adazichita pakati pa inu.

Inu nomwe ndinu mboni zanga,

ndikutero Ine Chauta.

13Ine ndine Mulungu

ndipo ndidzakhalapo nthaŵi zonse.

Palibe amene angathe kuthaŵa m'manja mwanga,

palibe amene angathe kusintha zochita zanga.”

Aisraele adzachokako ku Babiloni

14Chauta, Momboli wanu, Woyera uja wa Israele,

akunena kuti,

“Ndidzatuma gulu lankhondo

kukalimbana ndi Babiloni,

kuti ndikupulumutseni.

Ndidzagwetsa zipata za mzindawo,

ndipo kukondwa kwa anthu ake kudzasanduka kulira.

15Ine ndine Chauta, Woyera wanu uja,

Mlengi wa Israele.

Ine ndekha ndine mfumu yanu.”

16Kale lija Chauta adapanga njira pa nyanja,

njira pakati pa madzi amphamvu.

17Adasonkhanitsa magaleta ndi akavalo,

ndiponso gulu lankhondo ndi asirikali amphamvu.

Onsewo adagwa osadzukanso,

adazimitsidwa ndi kutheratu ngati chingwe cha nyale.

18Iyeyo akunena kuti, “Musakumbukire zakale

kapena kumaganiziranso zinthu zimene zidachitika kale.

19Ndikuchita zinthu zatsopano.

Zayamba kale kuwoneka, kodi simukuzipenya?

Ndikulambula mseu m'chipululu,

ndipo ndikukupatsani mitsinje m'dziko louma.

20Nyama zakuthengo zidzandilemekeza,

nkhandwe ndi nthiŵatiŵa zidzanditamanda,

chifukwa ndidzayendetsa madzi m'chipululu

ndipo ndidzayendetsa mitsinje m'dziko louma,

kuti ndiŵapatse madzi anthu anga osankhidwa.

21Amenewo ndi anthu amene ndidadzilengera,

ndipo azindiimbira nyimbo zotamanda Ine.”

Tchimo la Israele

22Chauta akuti,

“Koma simudapemphere kwa Ine,

inu am'banja la Yakobe,

mudatopa nane, inu Aisraele.

23Simudadzatule kwa Ine nkhosa

kuti zikhale zopereka zopsereza,

simudandilemekeze ndi nsembe zanu.

Sindidakulemetseni pomakupemphani zopereka zanu,

sindidakutopetseni pomakupemphani lubani.

24Simudandigulire bango lonunkhira,

simudandipatse mafuta okwanira a nsembe zanu.

Koma m'malo mwake inu mwanditopetsa ndi machimo anu,

mwandilemetsa ndi zolakwa zanu.

25“Ine, Ineyo ndithu,

ndine amene ndimafafaniza machimo anu,

kuti ulemerero wanga uwoneke.

Sindidzasungabe mlandu wa machimo anu.

26Mundikumbutse zakale, titsutsane.

Mufotokoze mlandu wanu

kuwonetsa kuti simudalakwe.

27Atate anu oyamba adachimwa,

atsogoleri anu aja adandilakwira.

28Mafumu anu adaipitsa malo anga opatulika.

Nchifukwa chake ndidalola

kuti banja la Yakobe liwonongedwe,

ndidalola kuti Aisraele anyozedwe.”

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help