Mik. 7 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za kuipa kwa Aisraele

1Kalanga ine!

Ndasanduka ngati wokunkha wosapeza zotsalira.

Sipadatsalenso mphesa zoti nkudya.

Sipadatsaleko nkhuyu zimene ndimazikonda.

2Anthu abwino atha pa dziko lapansi,

palibe ndi mmodzi yemwe wolungama.

Onse akubisalirana mwachiwembu.

Aliyense akusakira mbale wake mu ukonde.

3Ndi akatswiri pochita zoipa.

Akalonga ndi aweruzi amafuna ziphuphu,

ndipo mtsogoleri amaŵauza zoipa

zimene afuna kuti iwo achite.

Motero amalakwira pamodzi.

4Munthu wabwino koposa ali ngati lunguzi,

wolungama koposa ndi wolasa ngati tchinga laminga.

Lafika tsiku la chilango,

limene alonda ao, aneneri, adanena.

Lafika tsiku la chisokonezo chao.

5Wina asakhulupirire mnansi,

asadalire bwenzi lake lapamtima.

Aliyense achenjere ndi pakamwa pake,

ngakhale polankhula ndi mkazi wake yemwe.

6 Mt. 10.35, 36; Lk. 12.53 Makono ana aamuna akunyoza atate ao,

ana aakazi akuukira amai ao.

Mtengwa akulongolozana ndi mpongozi wake,

nkhondo ndi anansi.

7Koma ine ndidzadalira Chauta.

Ndidzaika mtima pa Mulungu Mpulumutsi wanga.

Mulungu wanga adzandimva.

Chauta apulumutsa anthu ake

8Inu adani athu musatiseke.

Tidagwa inde, koma tidzadzukanso.

Ngakhale tikhale mu mdima,

Chauta ndiye nyale yathu.

9Tachimwira Chauta,

nchifukwa chake tiyenera kupirira mkwiyo wake,

mpaka atazenga mlandu wathu ndi kuugamula.

Koma pambuyo pake adzatiloŵetsa m'kuŵala,

ndipo tidzaona chipulumutso chake.

10Tsono adani athu adzaona zimenezi,

ndipo manyazi adzaŵagwira

anthu amene ankatifunsa kuti,

“Ali kuti Chauta, Mulungu wanu?”

Tidzaona kugonjetsedwa kwao,

adzaponderezedwa ngati matope m'miseu.

11Inu anthu a ku Yerusalemu,

idzafikatu nthaŵi yomanganso malinga anu.

Nthaŵi imeneyo malire anu adzafutuzidwa.

12Nthaŵi imeneyo anthu anu adzabwerera kwa inu

kuchokera ku Asiriya mpaka ku Ejipito,

kuchokera ku Ejipito mpaka ku Mtsinje wa Yufurate,

ndiponso kuchokera ku nyanja ina mpaka ku nyanja inanso,

kuchokera ku phiri lina mpaka ku phiri linanso.

13Koma dziko lapansi lidzasanduka chipululu

chifukwa cha zoipa za anthu ake.

Amenewo ndiwo malipiro a ntchito zao.

Za chifundo cha Chauta

14Inu Chauta muŵatsogolere anthu anu ndi

ndodo yanu yoŵatetezera,

muŵete nkhosa zanu zimene mudazisankha.

Tsopano zikukhala zokha m'nkhalango

pakati pa dziko la chonde.

Koma muzilole kuti zikadye ku busa labwino,

ku Basani ndi Giliyadi,

monga masiku akale.

15Chauta akuti,

“Ndidzaŵaonetsa zodabwitsa,

monga masiku amene ankatuluka ku Ejipito.”

16Anthu a mitundu yambiri akadzaona zimenezo

adzachita manyazi,

ngakhale ali ndi mphamvu zotani.

Adzangogwira pakamwa,

ndi kutseka makutu motaya mtima.

17Adzavimvinizika pa dothi ngati njoka,

ngati zolengedwa zina zokwaŵa.

Adzabwera ali njenjenje kuchokera ku malinga ao.

Moopa adzatembenukira kwa Inu Chauta,

Mulungu wathu,

ndipo adzachita nanu mantha.

18Kodi ndani ali Mulungu ngati Inu,

amene amakhululukira machimo

ndi kuiŵala zolakwa za anthu anu otsala?

Simusunga mkwiyo mpaka muyaya,

chifukwa muli ndi chikondi chosasinthika.

19Mudzatichitiranso chifundo.

Mudzapondereza pansi zolakwa zathu,

mudzataya machimo athu onse pansi pa nyanja.

20Mudzaonetsa kukhulupirika kwanu kwa Yakobe,

ndi chikondi chanu chosasinthika kwa Abrahamu,

monga mudalonjezera molumbira kwa makolo athu

kuyambira pa masiku amakedzana.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help