1Ndikukweza maso anga kwa Inu,
Inu amene mumakhala pa mpando wachifumu kumwamba.
2Monga momwe anyamata amayang'anira
ku dzanja la bwana wao,
monga momwe adzakazi amayang'anira
ku dzanja la dona wao,
ndi momwenso timayang'anira ife
kwa Chauta Mulungu wathu,
mpaka atatichitira chifundo.
3Mutichitire chifundo, Inu Chauta,
mutichitire chifundo,
pakuti adani athu atinyoza kopitirira malire.
4Pa nthaƔi yaitali,
anthu olemera akhala akutinyodola,
anthu onyada akhala akutinyoza.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.