Mas. 1 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

BUKU LOYAMBA(Mas. 1—41)Za kudala koona

1Ngwodala munthu wosatsata uphungu wa anthu oipa,

wosatsanzira mayendedwe a anthu ochimwa,

wosakhala nawo m'gulu la anthu onyoza Mulungu,

2koma wokondwerera kumvera malamulo a Chauta,

nkumasinkhasinkha za malamulowo usana ndi usiku.

3 Yer. 17.8 Munthuyo ali ngati mtengo

wobzalidwa m'mbali mwa mtsinje wa madzi,

ngati mtengo wobereka zipatso pa nthaŵi yake,

umene masamba ake safota konse.

Zochita zake zonse zimamuyendera bwino.

4Anthu oipa sali choncho,

ali ngati mungu wouluzika ndi mphepo.

5Nchifukwa chake anthu ochimwa,

Mulungu adzaŵazenga mlandu,

adzaŵachotsa iwo pakati pa anthu ake.

6Paja Chauta amaŵasamalira anthu ake,

koma anthu ochimwa adzaonongeka.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help