Mas. 112 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Kukondwa kwa munthu wabwino

1Tamandani Chauta!

Ngwodala munthu woopa Chauta,

wokonda kusunga malamulo ake.

2Zidzukulu zake zidzakhala zamphamvu pa dziko lapansi.

Ana a munthuyo adzakhala odala.

3Banja lake lidzakhala lachuma ndi lolemera,

ndipo kulungama kwake kudzakhala kwamuyaya.

4Ngakhale nthaŵi ya mdima,

munthu wochita chilungamo ayenda m'kuŵala,

chifukwa ngwokoma mtima, wachifundo ndi woongoka.

5Munthu amene amakongoza mosafuna phindu,

amene amayendetsa ntchito zake mwachilungamo,

zinthu zimamuyendera bwino.

6Pakuti munthu wochita chilungamo sadzagwedezeka konse,

sadzaiŵalika mpaka muyaya.

7Saopa akamva zoipa zimene zachitika.

Mtima wake ndi wosasinthika,

amakhulupirira Chauta.

8Ali wolimba mtima,

sadzachita mantha,

potsiriza adzaona adani ake atagonja.

9 2Ako. 9.9 Amapereka chithandizo mwaufulu,

amaoloŵa manja kwa anthu osauka.

Chilungamo chake chidzakhala chamuyaya,

adzakhala wamphamvu

ndipo anthu adzampatsa ulemu.

10Munthu woipa amaona zimenezi,

ndipo amapsa nazo mtima.

Amakukuta mano nazimirira.

Zokhumba za munthu woipa sizidzachitika konse.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help