1Chaka cha 23 cha ufumu wa Yowasi, mwana wa Ahaziya mfumu ya ku Yuda, Yehowahazi mwana wa Yehu, adayamba kulamulira Aisraele ku Samariya, ndipo adakhala mfumu zaka 17.
2Iyeyo adachita zoipa kuchimwira Chauta. Zoipa zomwe Yerobowamu mwana wa Nebati adachimwitsa nazo Aisraele sadazileke ai.
3Nchifukwa chake Chauta adakwiyira Aisraele, ndipo kaŵirikaŵiri adalola kuti Hazaele mfumu ya ku Siriya ndiponso Benihadadi mwana wa Hazaeleyo aŵagonjetse.
4Tsono Yehowahazi adapemphera kwa Chauta ndipo Chauta adamumvera, poti adaona kupsinjidwa kwa Aisraele kumene mfumu ya ku Siriya idaŵapsinja nako.
5Nchifukwa chake Chauta adasankha mtsogoleri kuti apulumutse Aisraele m'manja mwa Asiriya. Motero Aisraele adakhala mwamtendere m'dziko mwao, monga momwe ankakhalira kale.
6Komabe Aisraelewo sadaleke kuchita zoipa zimene ankazichita anthu a pa banja la Yerobowamu, zimene iye ankachimwitsa nazo Aisraele. Aisraele adachitabe zoipazo, ndipo fano la Asera nalonso lidakhalabe ku Samariya.
7Nthaŵi imeneyo Yehowahazi analibe gulu lankhondo lalikulu. Anali ndi asilikali a pa akavalo makumi asanu okha, magaleta khumi ndiponso asilikali oyenda pansi zikwi khumi, popeza kuti mfumu ya ku Siriya inali itaononga asilikali ambiri nkuŵaponderezeratu ngati fumbi.
8Tsono ntchito zina za Yehowahazi pamodzi ndi zimene adazichita, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele.
9Motero Yehowahazi adamwalira, naikidwa m'manda momwe adaikidwa makolo akewo ku Samariya. Tsono Yehowasi mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
Yehowasi mfumu ya ku Israele10Chaka cha 37 cha ufumu wa Yowasi mfumu ya ku Yuda, Yehowasi mwana wa Yehowahazi adayamba kulamulira Aisraele ku Samariya, ndipo adalamulira zaka 16.
11Nayenso adachita zoipa kuchimwira Chauta. Sadaleke kuchita zoipa zonse zimene ankachita Yerobowamu mwana wa Nebati, zimene adachimwitsa nazo Aisraele.
12Tsono ntchito zina za Yehowasi ndi zonse zimene adazichita, kudzanso zamphamvu zimene adaonetsa pomenyana nkhondo ndi Amaziya mfumu ya ku Yuda, zidalembedwa m'buku la Mbiri ya Mafumu a ku Israele.
13Motero Yehowasi adamwalira, naikidwa ku Samariya pamodzi ndi mafumu a ku Israele. Tsono Yerobowamu mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
Mneneri Elisa amwalira14 2Maf. 2.12 Masiku amenewo Elisa adadwala matenda ofa nawo, ndipo Yehowasi mfumu ya ku Israele adapita kukamzonda. Adakalira misozi pamaso pake nkumati, “Atate, atate! Magaleta a Israele ndiponso okwerapo ake!”
15Pamenepo Elisa adauza Yehowasi kuti, “Tengani uta ndi mivi yake.” Adatenga utawo ndi miviyo.
16Tsono Elisa adauza Yehowasi mfumu ya ku Israeleyo kuti, “Kokani utawu.” Iye nkukokadi. Apo Elisayo adaika manja ake pa manja a mfumuyo,
17ndipo adati, “Tsekulani windo lakuvuma.” Ndipo adatsekuladi. Tsono Elisa adati, “Ponyani.” Yehowasi nkuponya. Pomwepo Elisa adati, “Inuyo ndinu muvi wa Chauta wogonjetsera pa nkhondo, muvi wogonjetsera Asiriya. Pakuti mudzamenyana nawo nkhondo Asiriya ku Afeki mpaka kuŵatha onse.”
18Ndipo adati, “Tengani mivi inayo.” Yehowasi adaitenga. Tsono Elisa adauza mfumu ya ku Israele ija kuti, “Lasani pansi miviyo.” Ndipo iye adalasa pansi katatu, nkuleka.
19Tsono Elisa munthu wa Mulungu uja adazazira Yehowasiyo nati, “Mukadalasa kasanu kapena kasanu ndi kamodzi konse, mukadagonjetsa Asiriya mpaka kuŵatha onse. Koma tsopano mudzaŵagonjetsa katatu kokha.”
20Pambuyo pake Elisa adamwalira ndipo adamuika m'manda.
Nthaŵi imeneyo magulu ankhondo a Amowabu ankathira nkhondo m'dzikomo chaka ndi chaka.
21Tsiku lina Aisraele ena kuti akaike mnzao ku manda, adangoona gulu lankhondo la Amowabuwo, iwo nkungoponya mtembowo m'manda mwa Elisa. Munthu wakufayo atangokhudza mafupa a Elisa, pomwepo adatsitsimuka nakhala chilili.
Nkhondo pakati pa Siriya ndi Israele22Hazaele mfumu ya ku Siriya ankazunza Aisraele masiku onse a Yehowahazi.
23Koma Chauta adaŵakomera mtima Aisraelewo ndi kuŵamveranso chifundo. Adaŵalezera mtima chifukwa cha chipangano chimene Iye adaachita ndi Abrahamu, Isaki ndi Yakobe, choncho sadalole kuti adani aŵaononge. Ndipo sadaiŵale anthu akewo mpaka tsopano.
24Hazaele mfumu ya ku Siriya atamwalira, Benihadadi mwana wake adaloŵa ufumu m'malo mwake.
25Nthaŵi imeneyo Yehowasi, mwana wa Yehowahazi, adalandanso kwa Benihadadi, mwana wa Hazaele, mizinda imene Benihadadiyo anali atailanda pomenyana nkhondo ndi Yehowahazi bambo wa Yehowasi. Yehowasi adagonjetsa Benihadadi katatu, nalandanso mizinda yonse ya Israele.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.