Num. 29 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Zopereka za pa tsiku la chikondwerero cha chaka chatsopano(Lev. 23.23-25)

1“Pa tsiku loyamba la mwezi wachisanu ndi chiŵiri, muzichita msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito zotopetsa. Tsiku limeneli muziliza malipenga.

2Ndipo mupereke nsembe yopsereza, yotulutsa fungo lokomera Chauta. Ikhale ya mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa imodzi yamphongo, anaankhosa asanu ndi aŵiri amphongo a chaka chimodzi, opanda chilema.

3Muperekenso chopereka cha chakudya chosakaniza ndi mafuta, wa makilogaramu atatu pa ng'ombe yamphongo iliyonse, wa makilogaramu aŵiri pa nkhosa yamphongoyo,

4ndiponso wa kilogaramu limodzi pa mwanawankhosa aliyense.

5Muperekenso tonde mmodzi kuti akhale nsembe yochitira mwambo wopepesera machimo anu.

6Mupereke zonsezi kuwonjezera pa nsembe yopsereza yopereka mwezi ukakhala, pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya, kuwonjezeranso pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija, pamodzi ndi nsembe zaufa ndi zopereka za chakumwa, potsata malamulo ake, kuti zitulutse fungo lokoma, nsembe zotentha pa moto, zopereka kwa Chauta.

Zopereka za pa tsiku la mwambo wopepesera machimo(Lev. 23.26-32)

7 Lev. 16.29-34 “Pa tsiku lakhumi la mwezi wachisanu ndi chiŵiri womwewo, muchite msonkhano wopatulika, ndipo musale zakudya. Musagwire ntchito iliyonse,

8koma mupereke kwa Chauta nsembe yopsereza, yotulutsa fungo lokoma. Ikhale ya mwanawang'ombe mmodzi wamphongo, nkhosa imodzi yamphongo, ndi anaankhosa asanu ndi aŵiri amphongo a chaka chimodzi. Musankhule nyama zopanda chilema.

9Ndipo mupereke chopereka cha chakudya chosakaniza ndi mafuta, wa makilogaramu atatu pa ng'ombe yamphongoyo, wa makilogaramu aŵiri pa nkhosa yamphongoyo,

10ndiponso wa kilogaramu limodzi pa mwanawankhosa aliyense.

11Muperekenso tonde mmodzi kuti akhale nsembe yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe yopepesera machimo ya pa tsiku la mwambo wopepesera machimo, kuwonjezeranso pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija, pamodzi ndi chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa.”

Zopereka za tsiku la chikondwerero cha misasa(Lev. 13.33-44)

12 Lev. 23.34; Deut. 16.13-15 “Pa tsiku la 15 la mwezi wachisanu ndi chiŵiri womwewo, muchite msonkhano wopatulika. Musagwire ntchito zotopetsa, ndipo muchite chikondwerero cholemekeza Chauta masiku asanu ndi aŵiri.

13Pa tsiku loyamba mupereke nsembe yopsereza, nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta. Ikhale ya anaang'ombe khumi ndi atatu amphongo, nkhosa ziŵiri zamphongo, anaankhosa khumi ndi anai amphongo a chaka chimodzi. Nyama zonsezo zikhale zopanda chilema.

14Muperekenso choperaka cha chakudya chosakaniza ndi mafuta, wa makilogaramu atatu pa ng'ombe yamphongo iliyonse, wa makilogaramu aŵiri pa nkhosa yamphongo iliyonse,

15ndi wa kilogaramu limodzi pa mwanawankhosa aliyense.

16Muperekenso tonde mmodzi kuti akhale nsembe yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija, pamodzi ndi chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa.

17“Pa tsiku lachiŵiri mupereke anaang'ombe khumi ndi aŵiri amphongo, nkhosa ziŵiri zamphongo, anaankhosa khumi ndi anai amphongo a chaka chimodzi opanda chilema,

18pamodzi ndi chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa pa ng'ombe zamphongo zija, pa nkhosa zamphongo zija, ndi pa anaankhosa aja, malinga ndi chiŵerengero cha nyamazo ndi potsata malangizo ake.

19Muperekenso tonde mmodzi kuti akhale nsembe yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija, pamodzi ndi zopereka za chakudya ndi za zakumwa.

20“Pa tsiku lachitatu mupereke ng'ombe zamphongo khumi ndi imodzi, nkhosa ziŵiri zamphongo, anaankhosa khumi ndi anai amphongo, a chaka chimodzi, opanda chilema,

21pamodzi ndi zopereka zake zachakudya ndi za chakumwa pa ng'ombe zamphongo zija, pa nkhosa zamphongo zija, ndi pa anaankhosa aja, molingana ndi chiŵerengero cha nyamazo ndi potsata malangizo ake.

22Muperekenso tonde mmodzi kuti akhale yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku zija, pamodzi ndi zopereka zachakudya ndi za chakumwa.

23“Pa tsiku lachinai mupereke ng'ombe khumi zamphongo, nkhosa ziŵiri zamphongo, anaankhosa amphongo khumi ndi anai a chaka chimodzi opanda chilema,

24pamodzi ndi zopereka zake zachakudya ndi za chakumwa pa ng'ombe zija, pa nkhosa zija, ndi pa anaankhosa aja, molingana ndi chiŵerengero cha nyamazo ndi potsata malangizo ake.

25Muperekenso tonde mmodzi kuti akhale nsembe yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija, pamodzi ndi zopereka zake zachakudya ndi za chakumwa.

26“Pa tsiku lachisanu mupereke ng'ombe zisanu ndi zinai zamphongo, nkhosa ziŵiri zamphongo, anaankhosa khumi ndi anai amphongo a chaka chimodzi opanda chilema,

27pamodzi ndi zopereka zake zachakudya ndi za chakumwa pa ng'ombe zija, pa nkhosa zija, ndi pa anaankhosa aja, molingana ndi chiŵerengero cha nyamazo ndi potsata malangizo ake.

28Muperekenso tonde mmodzi kuti akhale nsembe yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija, pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.”

29“Pa tsiku lachisanu ndi chimodzi mupereke ng'ombe zisanu ndi zitatu zamphongo, nkhosa ziŵiri zamphongo, anaankhosa khumi ndi anai amphongo a chaka chimodzi opanda chilema,

30pamodzi ndi chopereka cha chakudya ndi cha chakumwa pa ng'ombe zamphongo zija, pa nkhosa zamphongo zija, ndi pa anaankhosa aja, molingana ndi chiŵerengero cha nyamazo ndi potsata malangizo ake.

31Muperekenso tonde mmodzi kuti akhale nsembe yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija, pamodzi ndi zopereka zake za chakudya ndi za chakumwa.

32“Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri mupereke ng'ombe zisanu ndi ziŵiri zamphongo, nkhosa ziŵiri zamphongo, anaankhosa khumi ndi anai amphongo a chaka chimodzi opanda chilema.

33Muperekenso chopereka cha zakudya ndi zachakumwa pa ng'ombe zamphongo zija, pa nkhosa zamphongo zija, ndi pa anaankhosa aja, molingana ndi chiŵerengero cha nyamazo ndi potsata malangizo ake.

34Muperekenso tonde mmodzi kuti akhale nsembe yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija, pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi zachakumwa.”

35“Pa tsiku lachisanu ndi chitatu muchite msonkhano waulemu. Musagwire ntchito zotopetsa,

36koma mupereke nsembe yopsereza, nsembe yotentha pa moto, yotulutsa fungo lokomera Chauta. Ikhale ya ng'ombe imodzi yamphongo, nkhosa imodzi yamphongo, anaankhosa asanu ndi aŵiri amphongo a chaka chimodzi opanda chilema.

37Ndipo mupereke chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa pa ng'ombe yamphongo ija, pa nkhosa yamphongo ija, ndi pa anaankhosa aja, molingana ndi chiŵerengero cha nyamazo ndi potsata malangizo ake.

38Muperekenso tonde mmodzi kuti akhale nsembe yopepesera machimo, kuwonjezera pa nsembe zopsereza za tsiku ndi tsiku zija, pamodzi ndi chopereka chake cha chakudya ndi chakumwa.

39“Zimenezi ndizo zimene mudzapereke kwa Chauta pa masiku osankhidwa achikondwerero, kuwonjezera pa zopereka zanu zimene mudazilumbirira ndi pa zopereka zanu zaufulu: nsembe zanu zopsereza, nsembe zanu zaufa, nsembe zanu zachakumwa ndi nsembe zanu zachiyanjano.”

40Tsono Mose adauza Aisraele zonse, monga momwe Chauta adaamlamulira.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help