1Chauta adauza Mose kuti,
2Mt. 8.4; Mk. 1.44; Lk. 5.14; 17.14 “Lamulo la munthu wakhate pa tsiku la kuyeretsedwa kwake nali: Abwere naye kwa wansembe.
3Tsono wansembeyo atuluke kunja kwa mahema, ndipo amuwonetsetse wodwalayo. Ngati wakhateyo apezeke kuti wachira,
4wansembe alamule anthu kuti wodwala amene akuti ayeretsedweyo, amtengere mbalame zamoyo ziŵiri zimene Ayuda amaloledwa kudya, nthambi yamkungudza, kansalu kamlangali ndi kanthambi ka hisope.
5Wansembeyo alamule anthuwo kuti mbalame imodzi aiphere m'mbale yadothi pamwamba pa madzi atsopano.
6Wansembe atenge mbalame yamoyo ija pamodzi ndi nthambi yamkungudza ija, kansalu kamlangali kaja ndi kachitsamba ka hisope kaja. Zonsezo pamodzi ndi mbalame yamoyoyo, aziviike m'magazi a mbalame yomwe adaiphera m'mbale pamwamba pa madzi atsopano ija.
7Tsono wansembe awaze magazi kasanu ndi kaŵiri pa munthu amene akuti amuyeretse khateyo. Pamenepo wodwalayo amutche kuti ndi woyeretsedwa, ndipo aiwulutsire ku thengo mbalame yamoyoyo.
8Wodwala amene wayeretsedwayo, achape zovala zake, amete tsitsi lake lonse, ndipo asambe m'madzi; tsono atatero, adzakhala woyeretsedwa. Atatha zonsezo aloŵe chakumahema, koma akhale kunja kwa hema lake masiku asanu ndi aŵiri.
9Pa tsiku lotsiriza amete tsitsi lake lonse kumutu. Ametenso ndevu zake pamodzi ndi nsidze zomwe, tsitsi lake lonse ndithu. Kenaka achape zovala zake ndi kusamba, ndipo atatero, adzakhala woyeretsedwa.
10“Pa tsiku lachisanu ndi chitatu, wodwalayo atenge anaankhosa amphongo aŵiri opanda chilema, atengenso mwanawankhosa mmodzi wamkazi, wa chaka chimodzi, wopanda chilema, ndi chochepereka cha chakudya wosalala wolemera makilogaramu atatu, wosakaniza ndi mafuta, ndiponso mafuta okwanira limodzi mwa magawo atatu a lita.
11Wansembe amene ayeretse wodwalayo, aimiritse munthu woti ayeretsedweyo ali ndi zopereka zake zonse, pamaso pa Chauta, pakhomo pa chihema chamsonkhano.
12Wansembe atengeko mwanawankhosa wamphongo mmodzi ndi kumpereka kuti akhale nsembe yopepesera kupalamula, pamodzi ndi mafuta aja. Aziweyule, kuti zikhale zopereka zoweyula pamaso pa Chauta.
13Mwanawankhosayo amuphere pamalo pomwe amaphera nyama yoperekera nsembe yopepesera machimo ndi nsembe yopsereza, ndiye kuti pa malo oyera aja, pakuti chopereka chopepesera kupalamula ndi chake cha wansembe, monga momwe chimakhalira chopereka chopepesera machimo. Zoperekazo nzoyera kopambana.
14Wansembe atengeko magazi a nyama yoperekera nsembe yopepesera kupalamula, ndi kuŵapaka pa nsonga ya khutu la ku dzanja lamanja la munthu woti ayeretsedweyo. Apakenso pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja, ndi pa chala chachikulu cha ku phazi la ku dzanja lamanja.
15Wansembe atapeko mafuta pang'ono, nkuŵathira m'dzanja lake lakumanzere.
16Ndipo aviike chala chake cha ku dzanja lamanja m'mafuta amene ali m'dzanja lakumanzerewo, ndi kuwazako mafutawo ndi chala chake kasanu ndi kaŵiri pamaso pa Chauta.
17Mafuta otsala m'dzanja la wansembeyo, aŵapakeko pa nsonga ya khutu la ku dzanja lamanja la munthu woyeretsedwa uja, ndiponso pa chala chake chachikulu cha ku dzanja lamanja. Aŵapakenso pa chala chachikulu cha ku phazi la ku dzanja lamanja, pamalo pamene anali atapaka magazi aja a nyama yoperekera nsembe yopepesera kupalamula ija.
18Mafuta otsala m'dzanja la wansembe, aŵathire pamutu pa munthu woti ayeretsedwe uja. Ndimo m'mene wansembe amchitire munthuyo mwambo wompepesera pamaso pa Chauta.
19Pambuyo pake wansembe apereke nsembe yopepesera machimo, kuti achite mwambo wompepesera munthu woti ayeretsedwe khate lake uja. Kenaka wansembeyo aphe nyama yoperekera nsembe yopsereza,
20ndipo aipereke pamodzi ndi chopereka cha chakudya pa guwa. Atatero ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera machimo a munthu wodwalayo, ndipo pamenepo munthuyo adzakhala woyeretsedwa.
21“Koma munthu wodwalayo akakhala wosauka, kuti alibe zonsezo, apereke mwanawankhosa wamphongo kuti akhale nsembe yopepesera kupalamula. Aipereke moweyula manja, kuti achite mwambo wompepesera. Aperekenso kilogaramu limodzi la ufa wosalala wosakaniza ndi mafuta, kuti ukhale nsembe yaufa, pamodzi ndi mafuta okwanira limodzi mwa magawo atatu a lita.
22Aperekenso njiŵa ziŵiri kapena maundaankhunda aŵiri, monga m'mene angathere. Imodzi ikhale ya nsembe yopepesera machimo, inayo ikhale ya nsembe yopsereza.
23Pa tsiku lachisanu ndi chitatu zonsezo abwere nazo kwa wansembe, pakhomo pa chihema chamsonkhano pamaso pa Chauta, kuti munthuyo ayeretsedwe.
24Wansembe atenge mwanawankhosa woperekera nsembe yopepesera kupalamula, pamodzi ndi mafuta aja, ndipo aziweyule, kuti zikhale zopereka zoweyula pamaso pa Chauta.
25Tsono nkhosa yoperekera nsembe yopepesera kupalamulayo aiphe. Atengeko magazi ake ndi kuŵapaka pa nsonga ya khutu la ku dzanja lamanja la munthu amene ayeretsedweyo, ndi pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja, pamodzi ndi pa chala chachikulu cha ku phazi la ku dzanja lamanja.
26Kenaka wansembe athireko mafuta m'dzanja lake lamanzere,
27awazeko mafutawo kasanu ndi kaŵiri ndi chala cha ku dzanja lamanja pamaso pa Chauta.
28Apakekonso mafuta omwewo pa nsonga ya khutu la ku dzanja lamanja la munthu amene ayeretsedweyo. Aŵapakenso pa chala chachikulu cha ku dzanja lamanja pamodzi ndi pa chala chachikulu cha ku phazi la ku dzanja lamanja, pamalo pomwe anali atapaka magazi a nyama yoperekera nsembe yopepesera kupalamula ija.
29Mafuta otsala amene ali m'dzanja la wansembe aŵapake pamutu pa munthu amene ayeretsedweyo, kuti amchitire mwambo wopepesera machimo pamaso pa Chauta.
30Tsono malinga ndi m'mene adapezeramo, apereke njiŵa ziŵiri kapena maundaankhunda aŵiri.
31Azipereke ziŵirizo kuti imodzi ikhale nsembe yopepesera machimo, ndipo ina ikhale nsembe yopsereza, pamodzi ndi chopereka cha chakudya. Atatero, ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera machimo a munthu amene ayeretsedweyo pamaso pa Chauta.
32Limeneli ndilo lamulo la munthu wakhate amene alibe zinthu zoperekera kuyeretsedwa kwake.”
Za Ndere za m'nyumba33Chauta adauza Mose ndi Aroni kuti
34“Mukakaloŵa m'dziko la Kanani limene ndikukupatsani kuti likhale lanu, ndipo ndikakagwetsa ndere m'nyumba iliyonse m'dziko lanulo,
35mwiniwake nyumbayo adzapite kwa wansembe, akamuuze kuti, ‘Ndikuwona ngati kuti m'nyumba mwanga muli ndere.’
36Tsono wansembe asanawonetsetse nderezo, alamule kuti anthu atulutse zinthu zonse m'nyumbamo, kuti zam'nyumbazo angazitchule kuti nzoipitsidwa. Pambuyo pake wansembeyo aloŵe m'nyumbamo kuti aonemo.
37Ndipo aonetsetse nderezo. Akapezeka kuti zili m'khoma la nyumba, niziwoneka ndi maanga achisipu kapena ofiira, ndipo ikaoneka kuti yaloŵera mpaka m'kati,
38wansembeyo atuluke m'nyumbamo ndi kupita pa khomo, ndipo aitseke nyumbayo masiku asanu ndi aŵiri.
39Pa tsiku lachisanu ndi chiŵiri wansembeyo abwerenso kudzayang'ana. Nderezo zikakhala kuti zafalikira m'makoma a nyumbayo,
40wansembeyo alamule kuti anthu agamule miyala m'mene muli nderezo, ndipo akaitaye ku dzala kunja kwa mzinda.
41Pambuyo pake wansembe auze anthu kuti apale makoma onse m'kati mwa nyumbayo, ndipo dothi akupalalo akalitaye ku dzala kunja kwa mzinda.
42Tsono anthuwo atenge miyala ina ndi kuiloŵetsa m'malo mwa miyala adagumula ija, mwiniwakeyo atengenso dothi lina ndipo amate nyumbayo.
43“Nderez zikabukanso m'nyumba atagumula kale miyala ija, ndipo ataipala ndi kuimatanso,
44wansembe apite kukayang'ana. Zikakhala kuti zafalikiranso m'nyumbamo, ndiye kuti ndere zomwe zidafalikira m'nyumbamo ndi zoopsa. Nyumbayo njoipitsidwa.
45Aigwetse nyumbayo, tsono miyala yake, mitengo yake pamodzi ndi dothi limene adamatira nyumbayo, zonse akazitaye ku dzala kunja kwa mzinda.
46Ndipo munthu amene waloŵa m'nyumbamo itatsekedwa, adzakhala woipitsidwa mpaka madzulo.
47Munthu amene wagona m'nyumbamo achape zovala zake, ndipo amene wadyeramo nayenso achape zovala zake.
48“Koma wansembe akabwera naonetsetsa m'nyumbamo ndi kupeza kuti nthendayo sidafalikiremo, nyumbayo ataimata kale, wansembe aitchule nyumbayo kuti njosaipitsidwa, poti nderezo mulibe.
49Mwiniwake wa nyumbayo atenge timbalame tiŵiri, nthambi yamkungudza, kansalu kamlangali, ndi kachitsamba ka hisope, kuti zikhale zoyeretsera nyumbayo.
50Kamodzi mwa timbalame tiŵirito, wansembe akaphere m'mbale yadothi pamwamba pa kasupe.
51Kenaka atenge nthambi yamkungudza, kachitsamba ka hisope, ndi kansalu kamlangali, pamodzi ndi kambalame kamoyo kaja, zonsezo aziviike m'magazi a kambalame kophedwa kaja, ndiponso m'madzi atsopano aja, ndipo awaze nyumbayo kasanu ndi kaŵiri.
52Atatero, ndiye kuti wansembeyo waiyeretsa nyumbayo ndi magazi a mbalame, madzi atsopano, mbalame yamoyo, nthambi yamkungudza, kachitsamba ka hisope, ndiponso kansalu kamlangali.
53Mbalame yamoyo ija aiwulutsire kunja kwa mzinda ku thengo. Pamenepo ndiye kuti wansembe wachita mwambo wopepesera nyumbayo, ndipo idzakhala yoyeretsedwa.”
54Izi ndizo zimene muyenera kuchita ngati muona kuti
55mwadetsedwa chifukwa cha khate la mfundu yonyerenyesa, nguwi la pa chovala, ndere za m'nyumba,
56khate lachithupsa, khate lam'buko ndi khate labanga.
57Malamulo ameneŵa ngonena za chinthu choipitsidwa ndi chosaipitsidwa. Atsatidwe pa nthenda zonse za khate.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.