1Musakondwere Aisraele inu!
Musakhale ndi chisangalalo
chonga cha mitundu ina ya anthu.
Mwasiya Mulungu wanu
monga amachitira mkazi wosakhulupirika.
Mwadzigulitsa kwa Baala ngati mkazi wadama,
kuti mukalandireko zokolola zambiri.
2Tirigu ndi mphesa simudzakhala nazo zokwanira.
Mudzasoŵanso vinyo woti muzimwa.
3Simudzakhalanso m'dziko la Chauta.
Aefuremu inu, mudzabwerera ku ukapolo ku Ejipito,
mudzadya chakudya choletsedwa ku dziko la Asiriya.
4Kumeneko anthu sadzaperekanso zopereka za chakumwa
kupereka kwa Chauta.
Sadzamkondwetsanso ndi nsembe zao.
Chakudya chao chidzakhala ngati chakudya chapamaliro,
onse amene adzadya chakudya chimenecho adzaipitsidwa.
Chakudyacho chidzangokhala chodyera njala chabe,
osati choti nkukapereka ku Nyumba ya Chauta.
5Kodi pa tsiku la chikondwerero,
tsiku lolemekeza Chauta,
anthuwo adzachitapo chiyani?
6Nthaŵi ya chilango ikadzafika,
iwo nkubalalika,
Aejipito adzaŵakusa,
nakaŵaika m'manda komweko ku Memfisi.
Khwisa adzamera pa ziŵiya zao zasiliva.
M'nyumba mwao mudzamera minga.
7
Nchifukwa chake Mulungu sadzaiŵala kuipa kwao,
ndipo adzalanga machimo ao.
Uchimo wa Israele ndi chilango chake10 Num. 25.1-5 Chauta akuti,
“Israele ndidampeza ngati mphesa zam'thengo.
Makolo ake aja ndidaŵakondwerera
ngati nkhuyu zoyamba kupsa.
Koma iwowo adapita kwa Baala-Peori,
ndipo kumeneko adadzipereka kwa Baala.
Motero adasanduka chinthu chonyansa ngati fano laolo,
limene ankalikonda lija.
11Ulemerero wa Aefuremu udzaŵathaŵa mouluka
ngati mbalame.
Sadzabalanso ana.
Akazi ao sadzaima,
sadzatenga pathupi.
12Ngakhale abale ana, ndidzaŵaononga,
sadzakhalapo ndi mmodzi yemwe.
Tsoka kwa anthuwo ndikadzaŵasiya.”
13Inu Chauta, monga ndikuwonera,
ana a Efuremu adzakhala ngati nyama zojiwa.
Aefuremu adzatsogolera ana ao kunkhondo
kumene adzaphedwe.
14Muŵapatse, Inu Chauta.
Kodi mudzaŵapatse chiyani?
Muŵapatse mimba yopita padera ndi maŵere ouma!
Israele adzakhala ngati muzu wouma15Chauta akuti,
“Kuipa kwao konse kudaoneka makamaka ku Giligala.
Ndidayamba kudana nawo kumeneko.
Ndidzaŵapirikitsa m'dziko mwanga,
chifukwa makhalidwe ao ndi oipa.
Sindidzaŵakondanso,
atsogoleri ao onse andiwukira.
16Efuremu ali ngati mtengo wodulidwa
umene mizu yake yauma,
ndipo sudzabalanso zipatso.
Ngakhale anthuwo abale ana,
ndidzaŵapha ana ao okondedwawo.”
Chipembedzo chachikunja chidzaonongedwa17Mulungu wanga adzaŵataya anthu
amenewo chifukwa choti sadamumvere.
Adzasanduka oyendayenda
pakati pa mitundu ya pa dziko lapansi.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.