Num. 3 - Buku Loyera Catholic Edition - Chichewa

Za ana a Aroni

1Nayi mibadwo ya Aroni ndi Mose pa nthaŵi imene Chauta adalankhula ndi Mose pa phiri la Sinai.

2Num. 26.60 Maina a ana a Aroni naŵa: Nadabu mwana wake wachisamba, Abihu, Eleazara ndi Itamara.

3Ameneŵa ndiwo maina a ana a Aroni, ansembe odzozedwa amene iye adaŵasankha kuti azitumikira pa ntchito yaunsembe.

4Lev. 10.1, 2; Num. 26.61 Koma Nadabu ndi Abihu adafa pamaso pa Chauta pamene adapereka moto wosaloledwa pamaso pa Chauta m'chipululu cha Sinai. Iwowo analibe ana, ndipo choncho Eleazara ndi Itamara adatumikira pa ntchito yaunsembe pa nthaŵi imene Aroni bambo wao anali moyo.

Ntchito za Alevi

5Chauta adauza Mose kuti,

6“Bwera nawo anthu a fuko la Levi, ndipo uŵapereke kwa wansembe Aroni kuti azimtumikira.

7Azigwirira ntchito iyeyo ndi mpingo wonse, pakhomo pa chihema chamsonkhano, monga momwe amachitira potumikira m'Chihema cha Mulungu.

8Aziyang'anira zipangizo zonse za m'chihema chamsonkhano, ndipo azigwirira Aisraele ntchito potumikira m'Chihema cha Mulungu.

9Aleviwo uŵapereke kwa Aroni ndi kwa ana ake aamuna. Uŵapereke kwathunthu kwa iyeyo, kuŵachotsa pakati pa Aisraele.

10Umusankhe Aroni ndi ana ake, kuti azitumikira pa ntchito yaunsembe. Koma wina aliyense akayandikira pafupi, aphedwe.”

11Chauta adauza Mose kuti,

12Eks. 13.2“Pakati pa Aisraele, ndaŵapatula Alevi, m'malo mwa mwana wamwamuna aliyense woyamba kubadwa, amene amatsekula mimba ya mai wake. Aleviwo ndi anga,

13pakuti ana onse aamuna oyamba kubadwa ndi anga. Pa tsiku lija lomwe ndidapha ana onse aamuna oyamba kubadwa m'dziko la Ejipito, ndidadzipatulira ana onse oyamba kubadwa a m'dziko la Israele, ana a anthu ndi a nyama omwe. Onsewo ndi anga, Ine ndine Chauta.”

Chiŵerengero cha Alevi

14Chauta adauza Mose m'chipululu cha Sinai kuti,

15“Uŵerenge ana aamuna a Levi potsata mabanja ao ndiponso banja la makolo ao. Uŵerenge wamwamuna aliyense kuyambira wa mwezi umodzi ndi wopitirirapo.”

16Choncho Mose adaŵaŵerenga potsata mau a Chauta monga momwe adamlamulira.

17Maina a ana a Leviwo ndi aŵa: Geresoni, Kohati ndi Merari.

18Tsono ana a Geresoni potsata mabanja ao naŵa: Labini ndi Simei.

19Ana a Kohati potsata mabanja ao ndi aŵa: Amuramu, Izara, Hebroni ndi Uziyele.

20Ndipo ana a Merari potsata mabanja ao ndi aŵa: Mali ndi Musi. Ameneŵa ndiwo mabanja a Levi potsata banja la makolo ao.

21Alibini ndi Asimei anali mabanja otuluka mwa Geresoni. Ameneŵa ndiwo anali mabanja a Ageresoni.

22Chiŵerengero chao potsata kuchuluka kwa amuna onse, kuyambira mwana wamwamuna wa mwezi umodzi ndi wopitirapo, chinali 7,500.

23Mabanja a Geresoni ankamanga zithando zao kumbuyo kwa chihema cha Mulungu mbali yakuzambwe.

24Eliyasafu mwana wa Laele ndiye anali mtsogoleri wa banja la makolo a Ageresoni.

25Ndipo ntchito imene ana a Geresoni adapatsidwa m'chihema chamsonkhano inali yosamala chihema cha Mulungu, pamodzi ndi chophimbira chake, nsalu yochinga pakhomo pa chihema chamsonkhano,

26nsalu zochingira bwalo, nsalu zochingira khomo la bwalo lozungulira chihema cha Mulungu ndi guwa lansembe, ndiponso zingwe zake. Ankagwira ntchito zonse zokhudza zimenezi.

27Aamuramu, Aizari, Ahebroni ndi Auziyele, anali mabanja otuluka mwa Kohati. Ameneŵa ndiwo amene anali mabanja a Akohati.

28Potsata chiŵerengero cha amuna onse kuyambira mwana wamwamuna wa mwezi umodzi ndi wopitirirapo, onse anali 8,600, amene ankagwira ntchito m'malo opatulika.

29Mabanja a ana a Kohati ankamanga zithando zao kumwera kwa chihema cha Mulungu,

30pamodzi ndi Elizafani, mwana wa Uziyele, amene anali mutu wa mabanja a Akohati,

31Ndipo ntchito imene iwo adapatsidwa inali yosamala Bokosi lachipangano, tebulo, choikaponyale, maguwa, zipangizo za m'malo opatulika zimene ansembe ankagwirira ntchito, pamodzi ndi nsalu yochingira. Ankagwira ntchito zonse zokhudza zimenezi.

32Tsono Eleazara mwana wa wansembe Aroni, ndiye amene anali mkulu wa atsogoleri a Alevi, ndiponso amene ankayang'anira iwo amene ankasamala malo opatulika.

33Amali ndi Amusi anali mabanja otuluka mwa Merari. Ameneŵa ndiwo amene anali mabanja a Merari.

34Chiŵerengero chao potsata kuchuluka kwa amuna onse, kuyambira mwana wamwamuna wa mwezi umodzi ndi wopitirirapo, chinali 6,200.

35Ndipo munthu amene anali mutu wa mabanja a Merari anali Zuriyele mwana wa Abihaili. Iwo ankamanga zithando zao kumpoto kwa chihema cha Mulungu.

36Ntchito imene ana aamuna a Merari adapatsidwa, inali yosamala mitengo ya malo opatulika monga: nsichi zake, mizati yake, masinde ake ndi zina zonse zoyendera limodzi ndi zimenezo. Ankayang'anira ntchito zonse zokhudza zimenezi.

37Ankasamalanso mizati yozungulira bwalo ndi masinde ake, ndiponso zikhomo zake ndi zingwe zake.

38Amene ankamanga zithando zao patsogolo pa chihema cha Mulungu kuvuma kotulukira dzuŵa, kutsogolo kwa chihema chamsonkhano, anali Mose ndi Aroni pamodzi ndi ana ake a Aroni. Iwoŵa adaŵapatsa udindo wosamala kayendetsedwe ka chipembedzo m'malo opatulika, zonse zimene ankayenera kuchita m'malo mwa Aisraele. Munthu wina aliyense wofika pafupi ankayenera kuphedwa.

39Alevi onse amene Mose pamodzi ndi Aroni adaŵerenga potsata mabanja ao, Chauta ataŵalamula kutero, ndiye kuti amuna onse kuyambira a mwezi umodzi ndi opitirirapo, anali 22,000.

Alevi aloŵa m'malo mwa ana aamuna achisamba

40Chauta adauza Mose kuti, “Uŵerenge ana achisamba onse aamuna a Aisraele, kuyambira a mwezi umodzi ndi opitirirapo, potchula maina ao.

41Tsono unditengere Alevi m'malo mwa ana achisamba onse pakati pa Aisraele, utengenso ng'ombe za Alevi m'malo mwa ana onse oyamba kubadwa pakati pa ng'ombe za Aisraele, Ine ndine Chauta.”

42Choncho Mose adaŵerenga ana onse achisamba, monga Chauta adamlamula.

43Ndipo ana onse achisamba aamuna, potsata chiŵerengero cha maina ao, kuyambira a mwezi umodzi ndi opitirirapo, adakwanira 22,273.

44Chauta adauza Mose kuti,

45“Utenge Alevi m'malo mwa ana onse achisamba pakati pa Aisraele, utengenso ng'ombe za Alevi m'malo mwa ng'ombe za Aisraele. Aleviwo ndi anga, Ine ndine Chauta.

46Pofuna kuwombola ana achisamba 273 a Aisraele amene aposa chiŵerengero cha amuna a fuko la Levi,

47utenge masekeli asiliva asanu pa munthu aliyense. Masekeliwo akhale olingana ndi masekeli asiliva a ku malo opatulika kumene sekeli imodzi ikwanira magera makumi aŵiri.

48Upatse Aroni pamodzi ndi ana ake aamuna ndalama zimenezi, kuti zikhale mtengo woombolera Aisraele a chiŵerengero chopitirira chija.”

49Choncho Mose adatenga ndalama zoombolera zija kwa Aisraele amene chiŵerengero chao chidapitirira chiŵerengero cha amene adaomboledwa ndi Alevi.

50Adatenga ndalama zasiliva kwa ana achisamba a Aisraele okwanira 1,365, molingana ndi kaŵerengedwe ka masekeli asiliva a ku Chihema cha Mulungu.

51Ndipo Mose adapereka ndalama zoombolerazo kwa Aroni ndi kwa ana ake, potsata mau amene Chauta adalamula Mose.

Blog
About Us
Message
Site Map

Who We AreWhat We EelieveWhat We Do

Terms of UsePrivacy Notice

2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.

Home
Gospel
Question
Blog
Help