1 2Maf. 24.1; 2Mbi. 36.5-7; Dan. 1.1, 2 Naŵa mau amene mneneri Yeremiya adalembetsa Baruki mwana wa Neriya m'buku, chaka chachinai cha ufumu wa Yehoyakimu mwana wa Yosiya mfumu ya ku Yuda:
2“Chauta, Mulungu wa Israele, akunena kuti,
3Iwe Baruki udati, ‘Tsoka kwa ine, poti Chauta wandiwonjezera chisoni pa mavuto anga onse. Ndatopa nako kubuula kwanga, sindikutha kupeza mpumulo konse!’
4Chauta adandiwuza kuti ndilankhule mau aŵa kwa iwe Baruki, ‘Chimene ndidamanga, ndikuchigwetsa. Chimene ndidabzala, ndikuchizula. Umu ndi m'mene ndidzachitire ndi dziko lonse lapansi.
5Kodi ukudzifunira zazikulu? Ai, usadzifunire zoterezi. Ndidzagwetsera anthu onse zoipa. Koma iwe ndidzasunga moyo wako kulikonse kumene ungapite,’ ” akuterotu Chauta.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.