1Zonse zimene ndakulamulani lero, mumvere mokhulupirika, kuti mukhale ndi moyo, muchulukane, ndipo mukakhazikike m'dziko limene Chauta adalonjeza makolo anu.
2Kumbukirani m'mene Chauta, Mulungu wanu, adakutsogolerani m'chipululu, pa ulendo wa pa zaka zonse makumi anai zapitazi. Adakuvutani nakuyesani ndi zoŵaŵa, kuti adziŵe zimene zinali m'mitima mwanu, ndipo kuti aone ngati mudzamvera malamulo ake kapena ai.
3Mt. 4.4; Lk. 4.4 Adakutsitsani pokukhalitsani ndi njala, komanso adakupatsani mana kuti mudye. Inu ndi makolo anu simudadyepo ndi kale lonse chakudya chimenechi. Adachita zimenezi kuti akuphunzitseni kuti munthu sakhala ndi moyo ndi chakudya chokha ai, koma ndi mau onse otuluka m'kamwa mwa Mulungu.
4Zovala zanu sizidathe, ndipo ngakhale mapazi anu omwe sadatupe konse m'chipululu pa zaka makumi anai zonsezi.
5Lun. 11.9, 10Dziŵani kuti Chauta, Mulungu wanu, amakulangani monga momwe bambo amalangira ana ake.
6Tsono inu, muzichita monga momwe Chauta akulamulirani. Muziyenda m'njira zake ndipo muzimuwopa.
7Chauta, Mulungu wanu, adzakuloŵetsani m'dziko lokoma, dziko la mitsinje, la zitsime, la akasupe otumphukira m'zigwa ndi m'mapiri.
8Lilinso ndi tirigu, barele, mphesa, nkhuyu, makangaza, olivi ndi uchi.
9Kumeneko simudzakhala ndi njala, ndipo simudzasoŵa kanthu. Zitsulo zimapezeka m'miyala ya kumeneko, ndipo mungathe kukumbamo mkuŵa m'mapiri mwake.
10Mudzakhala ndi chakudya chokwanira ndipo mudzakhuta, tsono mudzathokoza Chauta, Mulungu wanu, chifukwa wakupatsani dziko lokoma.
Aŵachenjeza kuti asamaiŵala Chauta11 Hos. 13.5, 6 Samalani kuti musamaiŵala Chauta, Mulungu wanu. Musamalephera kumvera malamulo ndi malangizo ake amene ndakupatsani leroŵa.
12Mukadzadya ndi kukhuta, mukadzamanga nyumba zabwino zoti mudzakhalemo,
13mukadzakhala ndi ng'ombe, nkhosa, siliva ndi golide, ndipo chuma chanu chikadzanka chiwonjezekeraonjezekera,
14pamenepo musadzanyade ndi kuiŵala Chauta, Mulungu wanu, amene adakutulutsani ku Ejipito kumene mudaali akapolo.
15Iye adakutsogolerani, mpaka mudabzola chipululu chachikulu ndi choopsa chija, m'mene munali njoka za ululu woopsa ndi zinkhanira. Adakupatsani madzi otuluka m'thanthwe, m'dziko louma lopanda madzi lija.
16Adakupatsani mana oti mudye, chakudya chimene makolo anu anali asanadyepo, pofuna kukutsitsani ndi kukuyesani, kuti pambuyo pake akuchitireni zokoma.
17Tsono muchenjere, musamati, “Ndapeza chuma chonsechi ndi mphamvu zanga ndi nyonga zanga.”
18Kumbukirani kuti amene amakupatsani mphamvu zoti mulemerere, ndi Chauta, Mulungu wanu. Adachita zimenezi kale popeza kuti sadafune kuphwanya chipangano chake chimene adachita ndi makolo anu, chimodzimodzi m'mene akuchitira lero.
19Musamuiŵale Chauta, Mulungu wanu, ndi kutembenukira kwa milungu ina kuti muipembedze. Mukachimwa motero, ndithudi mudzaonongeka.
20Mukapanda kumvera Chauta, Mulungu wanu, mudzaonongeka monga momwe Chauta akuwonongera mitundu ina pamaso panu.
Who We AreWhat We EelieveWhat We Do
2025 by iamachristian.org,Inc All rights reserved.